bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 4
Proverbs 4
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 5 →
1
Ananu, mverani mwambo wa atate, nimutchere makutu mukadziwe luntha;
2
pakuti ndikuphunzitsani zabwino; musasiye chilangizo changa.
3
Pakuti ndinali mwana kwa atate wanga, wokondedwa ndi mai, ndine ndekha, sanabale wina.
4
Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine, mtima wako uumirire mau anga; sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.
5
Tenga nzeru, tenga luntha; usaiwale, usapatuke pa mau a m'kamwa mwanga;
6
usasiye nzeru, ndipo idzakusunga; uikonde, idzakutchinjiriza.
7
Nzeru ipambana, tatenga nzeru; m'kutenga kwako konseko utenge luntha.
8
Uilemekeze, ndipo idzakukweza; idzakutengera ulemu pamene uifungatira.
9
Idzaika chisada cha chisomo pamtu pako; idzakupatsa korona wokongola.
10
Tamvera mwananga, nulandire mau anga; ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka.
11
Ndakuphunzitsa m'njira ya nzeru, ndakuyendetsa m'mayendedwe olungama.
12
Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda; ukathamanga, sudzaphunthwa.
13
Gwira mwambo, osauleka; uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.
14
Usalowe m'mayendedwe ochimwa, usayende m'njira ya oipa.
15
Pewapo, osapitamo; patukapo, nupitirire.
16
Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.
17
Pakuti amadya chakudya cha uchimo, namwa vinyo wa chifwamba.
18
Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.
19
Njira ya oipa ikunga mdima; sadziwa chimene chiwaphunthwitsa.
20
Mwananga, tamvera mau anga; tcherera makutu ku zonena zanga.
21
Asachoke kumaso ako; uwasunge m'kati mwa mtima wako.
22
Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza, nalamitsa thupi lao lonse.
23
Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.
24
Tasiya m'kamwa mokhota, uike patali milomo yopotoka.
25
Maso ako ayang'ane m'tsogolo, zikope zako zipenye moongoka.
26
Sinkasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako; njira zako zonse zikonzeke.
27
Usapatuke kudzanja lamanja kapena kulamanzere; suntha phazi lako kusiya zoipa.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31