bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 30
Proverbs 30
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 31 →
1
Mau a Aguri mwana wa Yake; uthenga. Munthuyo anati, Ndadzitopetsa, Mulungu; ndadzitopetsa, Mulungu, ndathedwa;
2
pakuti ndipambana anthu onse kupulukira, ndilibe luntha la munthu.
3
Sindinaphunzira nzeru ngakhale kudziwa Woyerayo.
4
Ndani anakwera kumwamba natsikanso? Ndani wakundika nafumbata mphepo? Ndani wamanga madzi m'malaya ake? Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko? Dzina lake ndani? Dzina la mwanake ndani? Kapena udziwa.
5
Mau onse a Mulungu ali oyengeka; ndiye chikopa cha iwo amene amkhulupirira.
6
Usaonjezere kanthu pa mau ake, angakudzudzule, nungatsutsidwe kuti ulikunama.
7
Zinthu ziwiri ndakupemphani, musandimane izo ndisanamwalire:
8
Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera;
9
ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.
10
Usanamizire kapolo kwa mbuyake, kuti angakutemberere nawe ndi kutsutsidwa.
11
Pali mbadwo wotemberera atate ao, osadalitsa amai ao.
12
Pali mbadwo wodziyesa oyera, koma osasamba litsiro lao.
13
Pali mbadwo wokwezatu maso ao, zikope zao ndi kutukula.
14
Pali mbadwo mano ao akunga malupanga, zibwano zao zikunga mipeni; kuti adye osauka kuwachotsa kudziko, ndi aumphawi kuwachotsa mwa anthu.
15
Msundu uli ndi ana akazi awiri ati, Patsa, patsa. Pali zinthu zitatu sizikhuta konse, ngakhale zinai sizinena, Kwatha:
16
Manda, ndi chumba, dziko losakhuta madzi, ndi moto wosanena, Kwatha.
17
Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makungubwi a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.
18
Zinthu zitatu zindithetsa nzeru, ngakhale zinai, sindizidziwa:
19
Njira ya mphungu m'mlengalenga, njira ya njoka pamwala, njira ya ngalawa pakati pa nyanja, njira ya mwamuna ndi namwali.
20
Chomwecho njira ya mkazi wachigololo; adya, napukuta pakamwa, nati, Sindinachita zoipa.
21
Chifukwa cha zinthu zitatu dziko linthunthumira; ngakhale chifukwa cha zinai silingathe kupirira nazo;
22
chifukwa cha kapolo pamene ali mfumu; ndi chitsiru chitakhuta zakudya;
23
chifukwa cha mkazi wodedwa wokwatidwa; ndi mdzakazi amene adzalandira cholowa cha mbuyake.
24
Zilipo zinai zili zazing'ono padziko; koma zipambana kukhala zanzeru:
25
Nyerere ndi mtundu wosalimba, koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe.
26
Mbira ndi mtundu wopanda mphamvu, koma ziika nyumba zao m'matanthwe.
27
Dzombe lilibe mfumu, koma lituluka lonse mabwalomabwalo.
28
Buluzi ungamgwire m'manja, koma ali m'nyumba za mafumu.
29
Pali zinthu zitatu ziyenda chinyachinya; ngakhale zinai ziyenda mwaufulu:
30
Mkango umene uposa zilombo kulimba, supatukira chinthu chilichonse;
31
tambala wolimba m'chuuno, ndi tonde, ndi mfumu yokhala ndi ankhondo ake.
32
Ngati wapusa podzikweza, ngakhale kuganizira zoipa, tagwira pakamwa.
33
Pakuti potakasa mkaka, mafuta ayengekapo; ndi popsinja mfuno, mwazi utulukamo, ndi polimbikira mkwiyo ndeu ionekamo.
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 31 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31