bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 20
Proverbs 20
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 21 →
1
Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru.
2
Kuopsa kwa mfumu ndiko kubangula kwa mkango; womputa achimwira moyo wakewake.
3
Kuli ulemu kwa mwamuna kupewa ndeu; koma zitsiru zonse zimangokangana.
4
Waulesi salima chifukwa cha chisanu; adzapemphapempha m'masika osalandira kanthu.
5
Uphungu wa m'mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya; koma munthu wozindikira adzatungapo.
6
Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwake; koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?
7
Wolungama woyenda mwangwiro, anake adala pambuyo pake.
8
Mfumu yokhala pa mpando woweruzira ipirikitsa zoipa zonse ndi maso ake.
9
Ndani anganene, Ndasambitsa mtima wanga, ndayera opanda tchimo?
10
Miyeso yosiyana, ndi malichero osiyana, zonse ziwirizi zinyansa Yehova.
11
Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.
12
Khutu lakumva, ndi diso lopenya, Yehova anapanga onse awiriwo.
13
Usakonde tulo ungasauke; phenyula maso, udzakhuta zakudya.
14
Wogula ati, Chachabe chimenecho, koma atachoka adzitama.
15
Alipo golide ndi ngale zambiri; koma milomo yodziwa ndiyo chokometsera cha mtengo wapatali.
16
Tenga malaya a woperekera mlendo chikole; woperekera mkazi wachilendo chikole umgwire mwini.
17
Zakudya za chinyengo zikondweretsa munthu; koma pambuyo pake m'kamwa mwake mudzadzala tinsangalabwi.
18
Uphungu utsimikiza zolingalira, ponya nkhondo utapanga upo.
19
Kazitape woyendayenda awanditsa zinsinsi; usadudukire woyasama milomo yake.
20
Wotemberera atate wake ndi amake, nyali yake idzazima mu mdima woti bii.
21
Cholowa chingalandiridwe msangamsanga poyamba pake; koma chitsiriziro chake sichidzadala.
22
Usanene, Ndidzabwezera zoipa; yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.
23
Miyeso yosiyana inyansa Yehova, ndi mulingo wonyenga suli wabwino.
24
Yehova alongosola mayendedwe a mwamuna; munthu tsono angazindikire bwanji njira yake?
25
Kunena mwansontho, Ichi nchopatulika, kuli msampha kwa munthu, ndi kusinkhasinkha pambuyo pake atawinda.
26
Mfumu yanzeru ipeta amphulupulu, niyendetsapo njinga ya galeta.
27
Mzimu wa munthu ndiwo nyali ya Yehova; usanthula m'kati monse mwa mimba.
28
Chifundo ndi ntheradi zisunga mfumu; chifundo chichirikiza mpando wake.
29
Ulemerero wa anyamata ndiwo mphamvu yao; kukongola kwa nkhalamba ndi imvi.
30
Mikwingwirima yopweteka ichotsa zoipa; ndi mikwapulo ilowa m'kati mwa mimba.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31