bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Proverbs 27
Proverbs 27
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 28 →
1
Usanyadire zamawa, popeza sudziwa tsiku lina lidzabala chiyani?
2
Wina akutume, si m'kamwa mwako ai; mlendo, si milomo ya iwe wekha.
3
Mwala ulemera, mchenga ndiwo katundu; koma mkwiyo wa chitsiru upambana kulemera kwake.
4
Kupweteka mtima nkwa nkhanza, mkwiyo usefuka; koma ndani angalakike ndi nsanje?
5
Chidzudzulo chomveka chiposa chikondi chobisika.
6
Kulasa kwa bwenzi kuli kokhulupirika; koma mdani apsompsona kawirikawiri.
7
Mtima wokhuta upondereza chisa cha uchi; koma wakumva njala ayesa zowawa zonse zotsekemera.
8
Monga mbalame yosochera kuchisa chake, momwemo munthu wosochera kumalo ake.
9
Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima, ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu.
10
Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye; usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako; mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.
11
Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.
12
Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.
13
Tenga malaya a woperekera mlendo chikole; woperekera mkazi wachiwerewere chikole umgwire mwini.
14
Yemwe adalitsa mnzake ndi mau akulu pouka mamawa, anthu adzachiyesa chimenecho temberero.
15
Kudonthadontha tsiku lamvula, ndi mkazi wolongolola ali amodzimodzi.
16
Wofuna kumletsayo afuna kuletsa mphepo; dzanja lake lamanja lingogwira mafuta.
17
Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.
18
Wosunga mkuyu adzadya zipatso zake; wosamalira ambuyake adzalemekezedwa.
19
Monga m'madzi nkhope zionana, momwemo mitima ya anthu idziwana.
20
Kunsi kwa manda ndi kuchionongeko sikukhuta; ngakhale maso a munthu sakhutai.
21
Siliva asungunuka m'mbiya, ndi golide m'ng'anjo, motero chomwe munthu achitama adziwika nacho.
22
Ungakhale ukonola chitsiru m'mtondo ndi munsi, pamodzi ndi mphale, koma utsiru wake sudzamchoka.
23
Udziwitsitse zoweta zako zili bwanji, samalira magulu ako;
24
pakuti chuma sichili chosatha; kodi korona alipobe mpaka mibadwomibadwo.
25
Amatuta udzu, msipu uoneka, atchera masamba a kumapiri.
26
Anaankhosa akuveka, atonde aombolera munda;
27
mkaka wa mbuzi udzakukwanira kudya; ndi a pa banja lako ndi adzakazi ako.
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31