bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 1
Numbers 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 2 →
1
Chauta adalankhula ndi Mose ku chipululu cha Sinai, m'chihema chamsonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiŵiri, chaka chachiŵiri atatuluka ku dziko la Ejipito, ndipo adamuuza kuti,
2
“Uŵerenge anthu a mpingo wonse wa Aisraele potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Ulembe dzina la munthu wamwamuna aliyense mmodzimmodzi.
3
Iwe ndi Aroni muŵerenge anthu, gulu ndi gulu, a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, ndiye kuti anthu onse a ku Israele amene angathe kumenya nkhondo.
4
Pa fuko lililonse mutenge munthu mmodzi, mtsogoleri wa banja lake, kuti akuthandizeni pa ntchito yanuyo.
5
Maina a anthu okuthandizaniwo ndi aŵa: fuko la Rubeni, akuthandizeni ndi Elizuri mwana wa Sedeuri;
6
fuko la Simeoni, Selumiele mwana wa Zurishadai;
7
fuko la Yuda, Nasoni mwana wa Aminadabu;
8
fuko la Isakara, Netanele mwana wa Zuwara;
9
fuko la Zebuloni, Eliyabu mwana wa Heloni.
10
Mwa ana a Yosefe: fuko la Efuremu, Elisama mwana wa Amihudi; fuko la Manase, Gamaliele mwana wa Pedazuri;
11
fuko la Benjamini, Abidani mwana wa Gideoni;
12
fuko la Dani, Ahiyezere mwana wa Amishadai;
13
fuko la Asere, Pagiyele mwana wa Okarani;
14
fuko la Gadi, Eliyasafu mwana wa Deuwele;
15
fuko la Nafutali, Ahira mwana wa Enani.”
16
Ameneŵa ndiwo anthu amene adasankhidwa mu mpingo, atsogoleri a mabanja ao, akulu a mafuko a Aisraele.
17
Mose ndi Aroni adaŵatenga anthu amene atchulidwaŵa,
18
ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiŵiri, adasonkhanitsa mpingo wonse. Tsono Aisraele adalembetsa maina ao potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Ankalembetsa ndi anthu a zaka makumi aŵiri ndi kupitirirapo, mmodzimmodzi,
19
monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Umu ndi m'mene adaŵerengera anthuwo m'chipululu cha Sinai.
20
Mwa zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wa Yakobe, adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
21
Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Rubeni, adapezeka kuti ali 46,500.
22
Mwa zidzukulu za Simeoni adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
23
Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Simeoni, adapezeka kuti ali 59,300.
24
Mwa zidzukulu za Gadi adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
25
Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Gadi, adapezeka kuti ali 45,650.
26
Mwa zidzukulu za Yuda adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
27
Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Yuda, adapezeka kuti ali 74,600.
28
Mwa zidzukulu za Isakara adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
29
Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Isakara, adapezeka kuti ali 54,400.
30
Mwa zidzukulu za Zebuloni adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
31
Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Zebuloni, adapezeka kuti ali 57,400.
32
Mwa zidzukulu za Yosefe, ndiye kuti anthu a m'fuko la Efuremu, adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
33
Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Efuremu, adapezeka kuti ali 40,500.
34
Mwa zidzukulu za Manase adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
35
Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Manase, adapezeka kuti ali 32,200.
36
Mwa zidzukulu za Benjamini adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
37
Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Benjamini, adapezeka kuti ali 35,400.
38
Mwa zidzukulu za Dani adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
39
Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Dani, adapezeka kuti ali 62,700.
40
Mwa zidzukulu za Asere adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
41
Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Asere, adapezeka kuti ali 41,500.
42
Mwa zidzukulu za Nafutali adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
43
Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Nafutali, adapezeka kuti ali 53,400.
44
Ameneŵa ndiwo anthu amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, mothandizidwa ndi atsogoleri a Aisraele khumi ndi aŵiri amene ankaimirira mafuko ao.
45
Choncho amuna onse a mu Israele otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata banja la makolo ao,
46
adapezeka kuti ali 603,550.
47
Alevi okha sadaŵaŵerengere kumodzi ndi enawo, potsata banja la makolo ao,
48
chifukwa Chauta adaauza Mose kuti,
49
“Fuko la Levi usaliŵerenge ai, anthu ake usaŵalembere kumodzi ndi Aisraele enawo.
50
Uike Aleviwo kuti aziyang'anira chihema changa chaumboni, zipangizo zake ndi zonse zimene zili m'menemo. Azinyamula chihemacho, pamodzi ndi zipangizo zake, ndipo azichisamala. Zithando zao azimange pozungulira chihemacho.
51
Nthaŵi imene anthu akunyamuka ulendo, Alevi ndiwo amene azichitsitsa, ndipo nthaŵi imene anthu aima, Alevi omwewo ndiwo amene azichiimiritsa. Munthu wina aliyense wochiyandikira adzaphedwa.
52
Aisraele azimanga mahema ao m'magulumagulu, aliyense pa chithando chake, ndipo onse azimanga pafupi ndi mbendera yao.
53
Koma Alevi amange mahema ao pozungulira chihema chaumboni, kuti Mulungu asakwiyire mpingo wa Aisraele. Alevi ndiwo amene aziyang'anira chihema chaumbonicho.”
54
Umu ndi m'mene adachitira Aisraele. Adachita zonse monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36