bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 24
Numbers 24
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 25 →
1
Pamene Balamu adaona kuti zinali zokondwetsa Chauta kuti adalitse Aisraele, sadapite monga nthaŵi zina zija kukafunsa kuti adziŵe zimene Mulungu akufuna, koma adangotembenuka nayang'ana ku chipululu.
2
Adaona Aisraele ali m'mahema mwao, fuko lililonse pa lokha. Tsono mzimu wa Mulungu udatsika pa iye,
3
ndipo adayamba kulankhula mau auneneri, adati, “Mau a Balamu mwana wa Beori, mau a munthu amene maso ake ndi otsekuka,
4
munthu amene akumva mau a Mulungu, munthu amene akuwona Mphambe m'masomphenya, munthu amene akugwa pansi, koma maso ali chipenyere.
5
Mahema ako, iwe Yakobe, nyumba zako, iwe Israele, si kukoma kwake!
6
Anthu ako ali ngati zigwa zofika patali, ali ngati minda ya m'mbali mwa mtsinje, ali ngati khonje amene Chauta adabzala, ali ngati mitengo ya mkungudza yomera m'mbali mwa madzi.
7
Madzi adzasefukira m'zotungira zao, ndipo mbeu zao zidzakhala ndi madzi ambiri, mfumu yao idzakhala yotchuka kupambana Agagi, ndipo ufumu wake udzakwezedwa.
8
Mulungu adaŵatulutsa m'dziko la Ejipito. Ali ndi mphamvu zonga za njati, adzapha mitundu ya adani ao, adzaswa mafupa ao ndi kuŵaboola ndi mivi yao.
9
Adamyata, nagona pansi ngati mkango ngati mkango wamphongo kapena waukazi. Kodi amuutse ndani? Ndi wodala munthu amene aŵadalitsa, ndi wotembereredwa munthu amene aŵatemberera.”
10
Apo Balaki adapsera mtima Balamu, ndipo adaomba m'manja. Tsono Balakiyo adauza Balamu kuti, “Paja ndidakuitanani kuti mudzatemberere adani anga, ndipo inu mwaŵadalitsa katatu konseka.
11
Nchifukwa chake, chokani, kazipitani kwanu. Ndidaakuuzani kuti ndidzakupatsani mphotho, koma Chauta wakana kuti muilandire mphothoyo.”
12
Balamu adafunsa Balaki kuti “Kodi amithenga anu amene mudaŵatuma kwa ine aja, sindidaŵauze kuti,
13
‘Ngakhale Balaki andipatse nyumba yake yodzaza ndi siliva ndi golide, sindidzatha kuchita zosiyana ndi zimene Chauta wandiwuza. Sindidzachita zabwino kapena zoipa mwa kufuna kwanga. Ndidzalankhula zimene Chauta adzandiwuze?’ ”
14
Balamu adauza Balaki kuti, “Tsopano ndikupita kwa anthu anga. Bwerani kuno, ndikudziŵitseni zimene Aisraeleŵa adzaŵachite anthu anu masiku akudzaŵa.”
15
Ndipo adayambapo kulankhula mau auneneri adati, “Mau a Balamu mwana wa Beori, mau a munthu amene maso ake ndi otsekuka,
16
munthu amene akumva mau a Mulungu, ndipo akudziŵa nzeru zake za Wopambanazonse, munthu amene akuwona Mphambe m'masomphenya, munthu amene akugwa pansi, koma maso ake ali chipenyere.
17
Ndikupenya mtsogolo, ndipo ndikuona mtundu wa Israele. Mfumu yonga nyenyezi idzatuluka mwa Yakobe, ndodo yaufumu idzadzuka mwa Israele, idzatswanya atsogoleri a Mowabu, ndipo idzagonjetseratu mtundu wa Seti.
18
Dziko la Edomu lidzalandidwa, Seiri mdani wake adzagonjetsedwa, pamene Aisraele adzakhala akupambanabe.
19
Mwa Yakobe mudzatuluka mfumu yolamulira, imene idzaononga otsala mu mzinda.”
20
Tsono Balamu adayang'ana Amaleke, ndipo adayamba kulankhula nati, “Mtundu wa Amaleke udaali wopambana mitundu ina yonse, koma potsiriza pake udzaonongeka.”
21
Kenaka adayang'ana Akeni, tsono adayamba kulankhula nati, “Ngakhale malo amene mukukhalawo ngopanda zovuta, monga chisa chomangidwa pa thanthwe,
22
komabe mudzaonongeka inu ana a Kaini, mudzakhala mu ukapolo wa Asuri nthaŵi yaitali.”
23
Adayamba kulankhulanso nati, “Kalanga ine, ndani akhale moyo, Mulungu akachita zimenezi?
24
Zombo zidzabwera kuchokera ku Kitimu, zidzaononga Asuri ndi Eberi. Kitimu nayenso adzaonongeka.”
25
Tsono Balamu adanyamuka nabwerera kwao. Balaki nayenso adapita kwao.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36