bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 12
Numbers 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 13 →
1
Miriyamu ndi Aroni adayamba kumnena Mose chifukwa cha mkazi wachikusi amene Moseyo adamkwatira, poti adakwatiradi mkazi wa ku Kusi.
2
Iwowo adafunsa kuti, “Kodi nzoona kuti Chauta adalankhula kudzera mwa Mose yekha? Kodi sadalankhulenso kudzera mwa ife?” Chauta adazimva zimenezo.
3
Koma Mose anali munthu wofatsa kupambana anthu onse a pa dziko lapansi.
4
Tsono Chauta adauza Mose, Aroni ndi Miriyamu kuti, “Atatu nonsenu mubwere ku chihema chamsonkhano.” Ndipo onse atatuwo adapitadi.
5
Chauta adatsika mu mtambo, naima pakhomo pa hema, ndipo adaitana Aroni ndi Miriyamu, tsono aŵiri onsewo adabweradi.
6
Chauta adati, “Imvani mau anga. Pakakhala mneneri pakati panupa, Ine Chauta ndimadziwonetsa kwa munthuyo m'masomphenya, ndimalankhula naye m'maloto.
7
Koma sinditero ndi mtumiki wanga Mose, amene wakhala woyang'anira anthu anga onse a Israeli.
8
Ndimalankhula naye pakamwampakamwa, momveka osati mophiphiritsa, ndipo amaona ulemerero wanga. Chifukwa chiyani tsono simudaope kumnena Mose, mtumiki wanga?”
9
Pamenepo Chauta adaŵakwiyira, nachokapo.
10
Mtambo utachoka pamwamba pa chihema, Miriyamu adapezeka ali ndi khate lambuu ngati ufa, ndipo Aroni atacheuka, adangoona Miriyamu ali ndi khate.
11
Apo Aroni adauza Mose kuti, “Mbuyanga, musatilange chifukwa choti tachimwa, ndipo tachita zopusa.
12
Musalole kuti Miriyamu akhale ngati mwana wobadwa wakufa, amene thupi lake lili loonongeka kumodzi.”
13
Tsono mokweza mau Mose adauza Chauta kuti, “Mulungu ndikukupemphani kuti mumchiritse Miriyamu.”
14
Koma Chauta adauza Mose kuti, “Bambo wake akadamthira malovu kumaso, kodi Miriyamu sakadachita manyazi masiku asanu ndi aŵiri? Basi, amtsekere kunja kwa mahema masiku asanu ndi aŵiri, ndipo pambuyo pake angathe kumloŵetsanso.”
15
Choncho adamtsekera Miriyamu kunja kwa mahema masiku asanu ndi aŵiri. Ndipo anthu sadathe kunyamuka ulendo wao mpaka Miriyamu atamloŵetsanso.
16
Pambuyo pake anthu aja adanyamuka ku Hazeroti nakamanga mahema ao ku chipululu cha Parani.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36