bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 33
Numbers 33
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 34 →
1
Pamene Aisraele adatuluka m'dziko la Ejipito m'magulu a mafuko ao, Mose ndi Aroni akuŵatsogolera,
2
Mose adalemba maina a malo onse oyambira ulendo ndi chigono chilichonse, monga Chauta adamlamula. Zigono zake potsata malo oyambira ulendo wao zinali motere:
3
Adanyamuka ku Ramsesi pa mwezi woyamba, pa tsiku la 15 la mweziwo. M'maŵa mwake, litapita tsiku la Paska, Aisraele adatuluka m'dziko la Ejipito mokondwa, anthu onse a ku Ejipito akupenya.
4
M'menemo nkuti Aejipitowo akuika maliro a ana ao achisamba amene Chauta adaaŵapha pakati pao. Choncho Chauta adalipsira milungu ya Aejipito.
5
Pambuyo pake Aisraele adanyamuka ku Ramsesi nakamanga mahema ku Sukoti.
6
Adanyamuka ku Sukoti nakamanga mahema ku Etamu, mzinda umene uli m'mbali mwa chipululu.
7
Adanyamuka ku Etamu, nabwerera ku Pihahiroti, mzinda umene uli kuvuma kwa Baala-Zefoni. Ndipo adamanga mahema patsogolo pa Migidoli.
8
Adanyamuka ku Pihahiroti naoloka pakatimpakati pa nyanja, ndipo adaloŵa m'chipululu. Tsono adayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, nakamanga mahema ku Mara.
9
Adanyamuka ku Mara nakafika ku Elimu. Ku Elimuko kunali akasupe khumi ndi aŵiri ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi aŵiri, ndipo adamanga mahema ao kumeneko.
10
Adanyamuka ku Elimu, nakamanga mahema ao m'mbali mwa Nyanja Yofiira.
11
Adanyamuka ku Nyanja Yofiira, nakamanga mahema ao ku chipululu cha Sini.
12
Adanyamuka ku chipululu cha Sini, nakamanga mahema ao ku Dofika.
13
Adanyamuka ku Dofika, nakamanga mahema ao ku Alusi.
14
Adanyamuka ku Alusi, nakamanga mahema ao ku Refidimu kumene kunalibe madzi akumwa.
15
Adanyamuka ku Refidimu, nakamanga mahema ao ku chipululu cha Sinai.
16
Adanyamuka ku chipululu cha Sinai, nakamanga mahema ao ku Kibroti-Hatava.
17
Adanyamuka ku Kibroti-Hatava, nakamanga mahema ao ku Haseroti.
18
Adanyamuka ku Hazeroti, nakamanga mahema ao ku Ritima.
19
Adanyamuka ku Ritima, nakamanga mahema ao ku Rimoni-Perezi.
20
Adanyamuka ku Rimoni-Perezi, nakamanga mahema ao ku Libina.
21
Adanyamuka ku Libina, nakamanga mahema ao ku Risa.
22
Adanyamuka ku Risa, nakamanga mahema ao ku Kehelata.
23
Adanyamuka ku Kehelata, nakamanga mahema ao ku phiri la Sefera.
24
Adanyamuka ku phiri la Sefera, nakamanga mahema ao ku Harada.
25
Adanyamuka ku Harada, nakamanga mahema ao ku Makeloti.
26
Adanyamuka ku Makeloti, nakamanga mahema ao ku Tahati.
27
Adanyamuka ku Tahati, nakamanga mahema ao ku Tera.
28
Adanyamuka ku Tera, nakamanga mahema ao ku Mitika.
29
Adanyamuka ku Mitika, nakamanga mahema ao ku Hasimona.
30
Adanyamuka ku Hasimona, nakamanga mahema ao ku Meseroti.
31
Adanyamuka ku Meseroti, nakamanga mahema ao ku Beneyakana.
32
Adanyamuka ku Beneyakana, nakamanga mahema ao ku Horo-Hagidigadi.
33
Adanyamuka ku Horo-Hagidigadi, nakamanga mahema ao ku Yotibata.
34
Adanyamuka ku Yotibata, nakamanga mahema ao ku Aborona.
35
Adanyamuka ku Aborona, nakamanga mahema ao ku Eziyoni-Gebere.
36
Adanyamuka ku Eziyoni-Gebere, nakamanga mahema ao m'chipululu cha Zini (ndiye kuti Kadesi).
37
Adanyamuka ku Kadesi, nakamanga mahema ao ku phiri la Hori m'mbali mwa dziko la Edomu.
38
Chauta atamlamula, wansembe Aroni adakwera phiri la Hori nakafera komweko, chaka cha 40 Aisraele atatuluka m'dziko la Ejipito, pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu.
39
Aroniyo anali wa zaka 123 za kubadwa, pamene adamwalira pa phiri la Hori.
40
Mfumu ya ku Aradi, Mkanani amene ankakhala m'dziko la Kanani, adamva kuti Aisraele akubwera.
41
Pambuyo pake iwo adanyamuka ku phiri la Hori, nakamanga mahema ao ku Zalimona.
42
Adanyamuka ku Zalimona, nakamanga mahema ao ku Punoni.
43
Adanyamuka ku Punoni, nakamanga mahema ao ku Oboti.
44
Adanyamuka ku Oboti, nakamanga mahema ao ku Iyeabarimu, m'dziko la Mowabu.
45
Adanyamuka ku Iyimu, nakamanga mahema ao ku Dibonigadi.
46
Adanyamuka ku Dibonigadi, nakamanga mahema ao ku Alimoni-dibulataimu.
47
Adanyamuka ku Alimoni-dibulataimu, nakamanga mahema ao ku mapiri a Abarimu patsogolo pa Nebo.
48
Adanyamuka ku mapiri a Abarimu, nakamanga mahema ao ku zigwa za ku Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani ku Yeriko.
49
Adamanga mahema ao pafupi ndi mtsinje wa Yordani kuyambira ku Beteyesimoti mpaka ku Abele-Sitimu, m'zigwa za Mowabu.
50
Chauta adauza Mose m'zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yordani, kuti,
51
“Uza Aisraele kuti, Pamene muwoloka mtsinje wa Yordani kuti muloŵe m'dziko la Kanani,
52
mudzapirikitse nzika zonse za m'dzikomo pamene mukufika, ndipo mudzaononge miyala yao yozokota ndi kuwononganso mafano ao osungunula. Mudzasakaze akachisi ao onse ku mapiri.
53
Mudzalande dzikolo kuti likhale lanu, ndipo mudzakhale m'menemo, poti ndakupatsani kuti likhale lanu.
54
Mudzalandira dzikolo kuti likhale choloŵa chanu mwamaere, potsata mabanja anu. Fuko lalikulu lilandire choloŵa chachikulu, ndipo fuko laling'ono lilandire choloŵa chaching'ono. Dziko lililonse limene maere agwere munthu, likhale lake la munthuyo. Mudzalandire choloŵa chanu potsata mafuko a makolo anu.
55
Koma mukapanda kupirikitsa nzika zam'dzikomo pamene mukufika, amene mwaŵalola kuti atsalirewo adzakhala ngati zisonga zokubayani m'maso, ndiponso ngati minga m'mbali mwanu, ndipo adzakuvutani m'dziko m'mene mukakhalemo.
56
Tsono ndidzakuchitani inuyo zimene ndinkaganiza kuti ndiŵachite iwowo.”
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 34 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36