bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 17
Numbers 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 18 →
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Ulankhule ndi Aisraele kuti akupatse ndodo, fuko lililonse ndodo imodzi. Atsogoleri ao onse akupatse ndodo khumi ndi ziŵiri molingana ndi mafuko a makolo ao. Ulembe dzina la munthu aliyense pa ndodo yake,
3
ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi. Pakuti payenera kukhala ndodo imodzi pa mtsogoleri aliyense wa fuko la makolo ake.
4
Tsono ndodozo uziike m'chihema chamsonkhano patsogolo pa bokosi laumboni pamene ndimakumana nawe.
5
Ndipo ndodo ya munthu amene nditi ndimsankhe idzaphuka. Motero sindidzalola kumvanso maŵiringulo amene Aisraele amachita otsutsana nawe.”
6
Choncho Mose adalankhula ndi Aisraele. Ndipo atsogoleri onse adampatsa ndodozo, mtsogoleri aliyense ndodo imodzi molingana ndi mafuko a makolo ao, ndiye kuti ndodo khumi ndi ziŵiri pamodzi. Ndodo ya Aroni inali pakati pa ndodo zao.
7
Mose adakaziika ndodozo pamaso pa Chauta m'chihema chaumboni.
8
M'maŵa mwake Mose adakaloŵa m'chihema chaumboni. Adangoona ndodo ya Aroni, ya fuko la Levi, itaphuka masamba nkuchitanso maluŵa, ndipo itabala zipatso zakupsa za mtundu wa matowo.
9
Tsono Mose adatulutsa ndodo zonse zija pamaso pa Chauta ndi kuŵaonetsa Aisraele. Ataona, mtsogoleri aliyense adatenga ndodo yake.
10
Apo Chauta adauza Mose kuti, “Kabwezere ndodo ya Aroni patsogolo pa bokosi laumboni. Uisunge kuti ikhale chenjezo kwa anthu oukira aja, kuti aleke kuŵiringulako, kuti angafe.”
11
Mose adachita momwemo. Adatsatadi zomwe Chauta adalamula.
12
Tsono Aisraele adauza Mose kuti, “Tatayika, tonsefe taferatu.
13
Ngati munthu aliyense amene akuyandikira chihema cha Chauta alikufa, ndiye kuti tonsefe ndife akufa.”
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36