bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 32
Numbers 32
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 33 →
1
Ana a Rubeni ndi ana a Gadi anali ndi ng'ombe zambiri. Adaona dziko la Yazere ndi dziko la Giliyadi kuti linali ndi malo oyenera kuŵeterako ng'ombe.
2
Choncho ana a Gadi ndi ana a Rubeni aja adabwera kwa Mose, kwa wansembe Eleazara ndi kwa atsogoleri a mpingo, naŵauza kuti,
3
“Midzi ya Ataroti, Diboni, Yazere, Nimira, Hesiboni, Eleyale, Sibima, Nebo ndi Beoni,
4
dziko limene Chauta adagonjetsera Aisraele, ndi dziko loyenera kuŵeterako ng'ombe, ndipo atumiki anufe tili ndi ng'ombe.
5
Ngati mwatikomera mtima, mutipatse dzikoli atumiki anufe, kuti likhale lathu. Musatipititse patsidya pa Yordani.”
6
Koma Mose adafunsa ana a Gadi ndi ana a Rubeni kuti, “Kodi abale anu azikamenya nkhondo, inu mutangokhala kuno?
7
Chifukwa chiyani mufuna kuŵatayitsa mtima Aisraele, kuti asakaloŵe m'dziko limene Chauta adaŵapatsa?
8
Makolo anu adachita zotero, pamene ndidaŵatuma kuchokera ku Kadesi-Baranea, kuti akaone dziko.
9
Iwo atapita ku chigwa cha Esikolo, nakaona dzikolo, adatayitsa mtima Aisraele, pakuŵauza kuti asakaloŵe m'dziko limene Chauta adaŵapatsa.
10
Tsono pa tsiku limenelo Chauta adapsa mtima, ndipo adalumbira kuti,
11
‘Ndithudi palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu otuluka m'dziko la Ejipito, kuyambira wa zaka makumi aŵiri ndi wopitirirapo, amene adzaone dziko limene ndidalonjeza kuti ndidzapatsa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, chifukwa sadanditsate kwathunthu.
12
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaone dzikolo, kupatula Kalebe yekha mwana wa Yefune, Mkenizi uja, ndi Yoswa mwana wa Nuni, chifukwa iwoŵa ndiwo adatsata Chauta kwathunthu.’
13
Chauta adaŵapsera mtima Aisraele, ndipo adaŵayendetsa m'chipululu muja zaka makumi anai, mpaka udatha mbadwo wonse umene udachimwira Chauta.
14
Tsopano inu mwaloŵa m'malo mwa makolo anu, inu mbadwo watsopano wa anthu ochimwa, ndipo mukufuna kuti muwonjezere mkwiyo woopsa wa Chauta pa Aisraele.
15
Pakuti ngati muleka kumtsata, Iye adzasiyanso anthu m'chipululu, ndipo inu mudzaonongetsa anthu onseŵa.”
16
Tsono iwo adasendera kwa Mose namuuza kuti, “Poyamba mutilole kuti timange kuno makola a nkhosa zathu, ndi mizinda yoti ana athu azikhalamo.
17
Pambuyo pake tidzatenga zida zankhondo ndi kutsogolera Aisraele mpaka titakaŵafikitsa ku malo ao. Koma ana athu adzakhala m'mizinda yamalinga, chifukwa choopa anthu a m'dziko muno.
18
Sitidzabwerera kwathu mpaka Mwisraele aliyense atalandira choloŵa chake.
19
Ife ndiye sitidzalandira nao choloŵa chathu patsidya pa Yordanipo kapena patsogolo pake, chifukwa choti talandira choloŵa chathu tsidya lino la Yordani, kuvuma kuno.”
20
Choncho Mose adauza anthuwo kuti, “Muchite izi: mutenge zida pamaso pa Chauta ndi kupita ku nkhondo.
21
Aliyense mwa inu atenge zida, ndipo aoloke mtsinje wa Yordani pamaso pa Chauta ndi kupirikitsa adani ake patsogolo pake,
22
mpaka kugonjetsa dzikolo pamaso pa Chauta. Mukatero, pambuyo pake mudzabwerera kuno, chifukwa mudzakhala mutagwirira ntchito Chauta ndi Aisraele. Pamenepo dziko lino lidzakhala lanu pamaso pa Chauta.
23
Koma ngati simuchita choncho, mwachimwira Chauta, ndipo dziŵani kuti tchimo lanu lidzakutsatani.
24
Mangani mizinda ya ana anu, ndi makola a nkhosa zanu, koma muchitedi zimene mwalonjeza.”
25
Tsono ana a Gadi ndi ana a Rubeni adayankha Mose kuti, “Atumiki anu adzachitadi monga momwe inu mbuyathu mwalamulira.
26
Ana athu ndi akazi athu atsala ku mizinda ya Giliyadi, pamodzi ndi nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu zomwe.
27
Koma atumiki anufe, tiwoloka aliyense atatenga zida, kukamenya nkhondo pamaso pa Chauta, monga momwe inu mbuyathu mwalamulira.”
28
Choncho Mose adalamula wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mabanja a mafuko a Aisraele kuti,
29
“Ngati ana a Gadi ndi a Rubeni onse amene angathe kutenga zida kuti akamenye nkhondo pamaso pa Chauta. Adzaoloka nanu mtsinje wa Yordani, nadzagonjetsa dziko lili patsogolo panulo, mudzaŵapatse dziko la Giliyadi kuti likhale lao.
30
Koma akapanda kuwoloka nanu, atatenga zida zankhondo, adzalandira chuma chao pakati panu m'dziko la Kanani.”
31
Ndipo zidzukulu za Gadi ndi za Rubeni zidayankha kuti, “Ife atumiki anu tidzachita zomwe Chauta watiwuza.
32
Tidzaoloka titatenga zida zankhondo pamaso pa Chauta, ndi kuloŵa m'dziko la Kanani, koma chuma cha choloŵa chathu chidzatsala ndi ife konkuno ku tsidya lino la Yordani.”
33
Pomwepo Mose adapatsa ana a Gadi ndi a Rubeni ndiponso theka la fuko la Manase, mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dziko lonse pamodzi ndi mizinda ndi milaga yake, ndiye kuti mizinda yonse ya m'dziko lonselo.
34
Ana a Gadi adamanga mizinda ya Diboni, Ataroti, Aroere,
35
Atiroti-Sofani, Yazere, Yogobeha,
36
Betenimira ndi Beteharani. Yonseyo inali yozingidwa ndi malinga. Ndipo adamanganso makola a nkhosa.
37
Ana a Rubeni adamanga mizinda ya Hesiboni. Eleyale, Kiriyataimu,
38
Nebo, Baala-Meoni (dzina ili lidasinthidwa) ndi Sibima. Mizinda imene adamangayo adaitcha maina ena.
39
A fuko la Makiri, mwana wa Manase, adapita kukalanda dziko la Giliyadi napirikitsa Aamori amene ankakhala m'dzikomo.
40
Mose adapatsa Makiri mwana wa Manase dziko la Giliyadi, ndipo Makiriyo adakhala m'dziko limenelo.
41
Yairi wa fuko la Manase adapita kukalanda midzi ina naitcha Havoti-Yairi.
42
Noba adapita kukalanda mzinda wa Kenati pamodzi ndi midzi yake, ndipo adautcha Noba, kutengera dzina lake.
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 33 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36