bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 2
Numbers 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 3 →
1
Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,
2
“Aisraele, pomanga zithando, aliyense azimanga pafupi ndi mbendera yake imene ili ndi zizindikiro za banja la kholo lake. Azimanga moyang'anana ndi chihema chamsonkhano, tsono mochizungulira.
3
Amene amange kuvuma, kotulukira dzuŵa, akhale a mbendera ya zithando za fuko la Yuda, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Yudalo ndi Nasoni, mwana wa Aminadabu,
4
ndipo ankhondo ake ngokwanira 74,600.
5
Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Isakara. Mtsogoleri wa fuko la Isakaralo ndi Netanele mwana wa Zuwara,
6
ndipo ankhondo ake ngokwanira 54,400.
7
Tsono pabwere fuko la Zebuloni, limene mtsogoleri wake ndi Eliyabu mwana wa Heloni,
8
ndipo ankhondo ake ngokwanira 57,400.
9
Gulu lonse lathunthu la ku zithando za Yuda, poŵerenga magulu atatu onseŵa, ndi 186,400. Iwowo azikhala patsogolo poyenda.
10
“Mbali yakumwera kuzikhala mbendera ya zithando za fuko la Rubeni, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Rubeni ndi Elizuri mwana wa Sedeuri,
11
ndipo ankhondo ake ngokwanira 45,500.
12
Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Simeoni, limene mtsogoleri wake ndi Selumiele mwana wa Zurishadai,
13
ndipo ankhondo ake ngokwanira 59,300.
14
Tsono pabwere fuko la Gadi, limene mtsogoleri wake ndi Eliyasafu, mwana wa Deuwele,
15
ndipo ankhondo ake ngokwanira 45,650.
16
Chiŵerengero chathunthu cha anthu a m'zithando za Rubeni, poŵerenga magulu atatu onseŵa, ndi 151,450. Iwo akhale a gulu lachiŵiri poyenda.
17
“Pamenepo mpamene anyamule chihema chamsonkhano, chifukwa zithando za Alevi zimakhala pakati pa zithando zina. Monga momwe adamangira zithando zao, ndimo aziyendera, gulu lililonse pamalo pake motsatira mbendera yake.
18
“Mbali yakuzambwe kuzikhala mbendera ya zithando za fuko la Efuremu, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Efuremulo ndi Elisama mwana wa Amihudi,
19
ndipo ankhondo ake ngokwanira 40,500.
20
Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Manase, limene mtsogoleri wake ndi Gamaliele mwana wa Pedazuri,
21
ndipo ankhondo ake ngokwanira 32,200.
22
Tsono pabwere fuko la Benjamini, limene mtsogoleri wake ndi Abidani mwana wa Gideoni,
23
ndipo ankhondo ake ngokwanira 35,400.
24
Chiŵerengero chathunthu cha anthu a m'zithando za Efuremu, poŵerenga magulu atatu onseŵa, ndi 108,100. Iwo akhale a gulu lachitatu poyenda.
25
“Mbali yakumpoto kuzikhala mbendera ya zithando za fuko la Dani, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Danilo ndi Ahiyezere mwana wa Amishadai,
26
ndipo ankhondo ake ngokwanira 62,700.
27
Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Asere, limene mtsogoleri wake ndi Pagiyele mwana wa Okarani,
28
ndipo ankhondo ake ngokwanira 41,500.
29
Tsono pabwere fuko la Nafutali, limene mtsogoleri wake ndi Ahira mwana wa Enani,
30
ndipo ankhondo ake ngokwanira 53,400.
31
Chiŵerengero chathunthu cha anthu a m'zithando za Dani ndi 157,600. Iwo akhale a gulu lotsiriza poyenda motsatira mbendera zao.”
32
Ameneŵa ndiwo Aisraele monga momwe adaŵaŵerengera potsata banja la makolo ao. Anthu onse a m'zithandomo anali 603,550 amene adaŵaŵerenga m'magulumagulu.
33
Koma Alevi sadaŵaŵerengere kumodzi ndi Aisraele, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
34
Umu ndi m'mene adachitira Aisraele. Iwo adachita zonse monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Adamanga zithando zao pafupi ndi mbendera zao. Choncho adanyamuka ulendo wao aliyense pa banja lake, potsata banja la makolo ao.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36