bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 19
Numbers 19
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 20 →
1
Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,
2
“Lamulo limene Chauta wapereka nali: Muuze Aisraele kuti abwere ndi msoti wa ng'ombe wofiira, wosapunduka, wopanda chilema, ndiponso umene sudasenzepo goli chiyambire.
3
Muupereke kwa wansembe Eleazara, kenaka anthu atuluke nawo kunja kwa mahema, ndipo auphe pamaso pake.
4
Tsono wansembe Eleazara atengeko magazi a ng'ombeyo ndi chala chake, ndipo awaze magaziwo kumaso kwa chihema chamsonkhano kasanunkaŵiri.
5
Ng'ombeyo aitenthe, Eleazara akupenya. Chikopa chake, nyama yake, magazi ake pamodzi ndi ndoŵe yake, azitenthe zonsezo.
6
Wansembe atenge mtengo wa mkungudza, kachitsamba ka hisope ndi kansalu kamlangali, ndipo zonsezo aziponye m'moto m'mene ng'ombe ija ikunyekamo.
7
Tsono wansembe achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, pambuyo pake aloŵe m'mahema. Koma wansembeyo adzakhale woipitsidwa mpaka madzulo.
8
Munthu amene atentha ng'ombeyo achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma adzakhalebe woipitsidwa mpaka madzulo.
9
Munthu amene ali wosaipa pa zachipembedzo ndiye aole phulusa la ng'ombelo, ndipo aliike kunja kwa mahema pa malo aukhondo pa zachipembedzo. Asungire mpingo wa Aisraele phulusalo, kuti aziika m'madzi oyeretsera zonyansa pa zachipembedzo. Mwambo umenewu ndi wochotsera tchimo.
10
Munthu amene aola phulusa la ng'ombe achape zovala, koma iyenso adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Limeneli likhale lamulo lamuyaya kwa Aisraele ndi kwa mlendo wokhala pakati pao.
11
“Amene akhudza mtembo wa munthu wina aliyense, akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri.
12
Asambe ndi madzi oyeretsera aja pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri kuti ayere, ndipo adzamuyeretsadi. Koma akapanda kusamba pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri kuti ayere, sadzayera.
13
Munthu aliyense wokhudza munthu wakufa, ndipo sadziyeretsa, munthu ameneyo akuipitsa Chihema cha Chauta, choncho adzachotsedwa m'dziko la Aisraele. Akhale woipitsidwa chifukwa sadawazidwe madzi aja oyeretsera pa zachipembedzo, ndi woipitsidwabe ameneyo.
14
“Pamene munthu afera m'hema, lamulo lake nali: munthu aliyense amene aloŵa m'hemamo, ndipo aliyense amene ali m'hema, akhale woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri.
15
Ndipo chiŵiya chilichonse chopanda chivundikiro nchoipitsidwa.
16
Munthu aliyense amene akhudza munthu wophedwa ndi lupanga panja, kapena mtembo, kapena fupa la munthu wakufa, kapenanso manda, akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri.
17
Woipitsidwayo amtengereko m'mbiya phulusa la nsembe yopsereza yopepesera machimo, ndipo aonjezemo madzi abwino atsikulo.
18
Tsono munthu wosaipitsidwa atenge kachitsamba ka hisope ndi kukaviika m'madzi aja, ndipo awaze madziwo pa hema, pa zipangizo zake zonse, pa anthu amene anali m'menemo, ndi pa munthu amene adakhudza fupa la munthu wakufa, kapena munthu wophedwa, kapena chikulu mtembo kapena manda.
19
Munthu wosaipitsidwayo awaze madzi munthu woipitsidwa uja, pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Atawazidwa madzi choncho pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, achape zovala zake, asambe thupi lonse, ndipo madzulo ake adzakhala woyeretsedwa.
20
“Koma munthu woipitsidwa akapanda kudziyeretsa, ameneyo achotsedwe pakati pa msonkhano, pakuti waipitsa malo opatulika a Chauta. Ameneyo ndi woipitsidwa chifukwa sadamuwaze madzi oyeretsera aja.
21
Limeneli likhale lamulo lamuyaya kwa iwo. Munthu amene awaza madzi oyeretserawo, achape zovala zake. Ndipo munthu amene akhudza madzi ochapirawo, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.
22
Chinthu chilichonse chimene munthu woipitsidwa akhudza, chidzakhala choipitsidwa. Ndipo munthu aliyense wokhudza chimenecho, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.”
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36