bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 13
Numbers 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 14 →
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanani limene ndikupatsa Aisraele. Pa fuko lililonse utume munthu mmodzi, amene ali mtsogoleri m'fukolo.”
3
Choncho Mose adaŵatuma kuchokera ku chipululu cha Parani, monga momwe Chauta adaalamulira, ndipo onsewo anali atsogoleri a Aisraele.
4
Maina ao ndi aŵa: m'fuko la Rubeni, adatuma Samuwa mwana wa Zakuri.
5
M'fuko la Simeoni, adatuma Safati mwana wa Hori.
6
M'fuko la Yuda, adatuma Kalebe mwana wa Yefune.
7
M'fuko la Isakara, adatuma Igala mwana wa Yosefe.
8
M'fuko la Efuremu, adatuma Hoseya mwana wa Nuni.
9
M'fuko la Benjamini, adatuma Paliti mwana wa Rafu.
10
M'fuko la Zebuloni, adatuma Gadiele mwana wa Sodi.
11
M'fuko la Yosefe (ndiye kuti m'fuko la Manase) adatuma Gadi mwana wa Susi.
12
M'fuko la Dani, adatuma Amiyele mwana wa Gemali.
13
M'fuko la Asere, adatuma Seturi mwana wa Mikaele.
14
M'fuko la Nafutali, adatuma Nabi mwana wa Vofusi.
15
M'fuko la Gadi, adatuma Geuwele mwana wa Maki.
16
Ameneŵa ndiwo maina a anthu amene Mose adaŵatuma kukazonda dziko. Ndipo Hoseya mwana wa Nuni, Mose adamutcha dzina loti Yoswa.
17
Mose adaŵatuma kukazonda dziko la Kanani, naŵauza kuti, “Pitani cha ku Negebu, ndipo mukakwere dziko lamapirilo.
18
Mukaone dzikolo kuti ndi lotani, ndipo ngati anthu am'dzikomo ngamphamvu kapena opanda mphamvu, ngati ngoŵerengeka kapena ambiri.
19
Mukaone ngati dziko limene akukhalamolo ndi labwino kapena loipa, ngati mizinda imene amakhalamo ndi yamahema kapena yamalinga.
20
Mukaonenso ngati dzikolo ndi lolemera kapena losauka, ndipo ngati nkhalango zilimo kapena ai. Mulimbe mtima, ndipo mukabwere ndi zipatso zina zam'dzikomo.” Imeneyo inali nyengo yopsa mphesa zoyamba.
21
Choncho adapita kukazonda dzikolo kuyambira ku chipululu cha Zini mpaka ku Rehobu pafupi ndi chipata cha Hamati.
22
Adadzera njira ya ku Negebu nakafika ku Hebroni, kumene kunkakhala Ahimani, Sesai ndi Talimai, zidzukulu za Aanaki. (Adamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziŵiri asanamange Zowani ku Ejipito.)
23
Ndipo adafika ku chigwa cha Esikolo, nathyolako nthambi yokhala ndi tsango limodzi la mphesa, ndipo aŵiri mwa iwowo adainyamula mopika. Adatengakonso makangaza ndi nkhuyu.
24
Malowo adaŵatcha chigwa cha Esikolo, chifukwa cha tsango lamphesa limene anthu aja adathyola kumeneko.
25
Patapita masiku makumi anai, anthu aja adabwerako kumene adakazonda dziko kuja.
26
Adabwera kwa Mose ndi Aroni ndi kwa mpingo wa Aisraele m'chipululu cha Parani ku Kadesi. Adasimbira Mose ndi Aroni ndi mpingo wonse za ulendo wao naŵaonetsa zipatso za ku dzikolo.
27
Adaŵauza kuti, “Tidakafika kudziko kumene inu mudatituma. Dzikolo ndi lamwanaalirenji, zipatso zake ndi izi.
28
Komatu anthu am'dzikomo ngamphamvu, mizinda yao ndi yozingidwa ndi malinga, ndiponso ndi yaikulu kwambiri. Kuwonjezera pamenepo, tidaonanso zidzukulu za Aanaki kumeneko.
29
Aamaleke amakhala m'dziko lakumwera. Ahiti, Ayebusi ndi Aamori amakhala m'dziko lamapiri. Akanani amakhala m'mphepete mwa nyanja ndi m'mphepete mwa mtsinje wa Yordani.”
30
Koma Kalebe adaŵakhalitsa chete anthu pamaso pa Mose, nati, “Tiyeni tipite nthaŵi yomwe ino, tikalande dzikolo, chifukwa tingathe kuligonjetsa.”
31
Tsono anthu aja amene adaapita naye limodziŵa adati, “Sitingathe kukalimbana nawo anthuwo, poti ngamphamvu kopambana ife.”
32
Choncho adasimbira Aisraelewo zoipa za dzikolo zimene adakaziwona, adati, “Dziko limene tidakalizondalo ndi dziko limene limaononga anthu ake. Ndipo anthu onse amene tidaŵaona kumeneko ngaataliatali.
33
Tidaonanso ziphona, (zidzukulu za Aanaki). Ifeyo tinkaoneka ngati ziwala, ndipo iwonso ankatiwona ngati ziwala.”
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36