bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 10
Numbers 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 11 →
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Upange malipenga aŵiri asiliva, uchite kusula. Uziimba malipengawo poitana mpingo, ndi pochoka pa mahema.
3
Akaliza aŵiri onsewo, mpingo wonse usonkhane kwa iwe pa chipata cha chihema chamsonkhano.
4
Koma akangoliza limodzi lokha, atsogoleri a mafuko a Aisraele ndiwo asonkhane kwa iwe.
5
Mukaliza lipenga lochenjeza, anthu a m'mahema akuvuma ayambepo ulendo.
6
Mukaliza lipenga lochenjeza kachiŵiri, anthu a m'mahema akumwera ayambepo ulendo. Muziŵalizira lipenga lochenjezalo nthaŵi zonse akamanyamuka ulendo.
7
Pamene mpingo wonse uyenera kusonkhana pamodzi, mulize lipenga, koma musalize lipenga lochenjeza.
8
Ana a Aroni, ansembe aja, ndiwo aziliza malipenga. Ntchito ya malipengayi ndi lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse.
9
Pamene mukukamenya nkhondo m'dziko mwanu ndi adani amene akukuzunzani, nthaŵi imeneyo mulize malipenga ochenjeza, kuti Chauta wanu akukumbukeni, ndipo adzakupulumutsani kwa adani anu.
10
Pa tsiku lanu losangalala, pa masiku osankhidwa a zikondwerero zanu, ndi pa masiku oyamba a miyezi, mulize malipenga pamene mukupereka nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu zachiyanjano. Malipengawo adzakuthandizani kumkumbukira Mulungu wanu. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.”
11
Pa chaka chachiŵiri, mwezi wachiŵiri, tsiku la 20, mtambo udachoka pa chihema chaumboni.
12
Tsono Aisraele adanyamuka ulendo wao m'magulumagulu kuchokera ku chipululu cha Sinai. Mtambowo udakaima m'chipululu cha Parani.
13
Kameneka kanali koyamba kuti Aisraele anyamuke, Chauta atalamula kudzera mwa Mose.
14
Otsata mbendera ya zithando za fuko la Yuda ndiwo adayamba kunyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Nasoni mwana wa Aminadabu.
15
Mtsogoleri wa gulu la fuko la Isakara anali Netanele mwana wa Zuwara.
16
Mtsogoleri wa gulu la fuko la Zebuloni anali Eliyabu mwana wa Heloni.
17
Anthu atagwetsa chihema cha Mulungu, ana a Geresoni ndi ana a Merari, oyenera kunyamula chihema cha Mulungu, adanyamuka ulendo wao.
18
Pambuyo pake otsata mbendera ya zithando za fuko la Rubeni adanyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Elizuri mwana wa Sedeuri.
19
Mtsogoleri wa gulu la Asimeoni anali Selumiele mwana wa Zurishadai.
20
Mtsogoleri wa gulu la fuko la Agadi anali Eliyasafu mwana wa Deuwele.
21
Tsono Akohati atasenza zinthu zopatulika, adanyamuka. Malo opatulika anali atamangidwiratu iwowo asanafike.
22
Otsata mbendera ya zithando za fuko la Efuremu adanyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Elisama mwana wa Amihudi.
23
Mtsogoleri wa gulu la fuko la Manase anali Gamaliele mwana wa Pedazuri.
24
Mtsogoleri wa fuko la Abenjamini anali Abidani mwana wa Gideoni.
25
Potsiriza otsata mbendera ya zithando za Adani amene anali kumbuyo kwa anthu a mahema onse, adanyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Ahiyezere mwana wa Amishadai.
26
Mtsogoleri wa gulu la fuko la Asere anali Pagiyele mwana wa Okarani.
27
Mtsogoleri wa gulu la fuko la Nafutali anali Ahira mwana wa Enani.
28
Umenewu ndiwo mndandanda wa kayendedwe ka Aisraele, pamene ankanyamuka ulendo wao m'magulumagulu.
29
Mose adauza Hobaba, mwana wa Reuele Mmidiyani, mpongozi wake uja, kuti, “Tikupita ku malo amene Chauta adati, ‘Ndidzakupatsani.’ Tiyeni tipite limodzi, ndipo tidzakuchitirani zabwino, pakuti Chauta walonjeza Aisraele zinthu zabwino.”
30
Koma iye adayankha kuti, “Sindipita nao, ndipita kwathu kwa abale anga.”
31
Ndipo Mose adati, “Musatisiye, ndapota nanu, poti inu mukudziŵa kumene tingamange mahema m'chipululu muno, ndipo mudzakhala maso athu.
32
Mukapita nao, zilizonse zimene Chauta adzatichitire, ife tidzakuchitirani zomwezo.”
33
Choncho adanyamuka ku phiri la Chauta, nayenda ulendo wa masiku atatu. Bokosi lachipangano la Chauta lidatsogola, nayenda nalo ulendo wa masiku atatu, kuti akapeze malo oti anthu onse aja akapumuleko.
34
Mtambo wa Chauta unkaŵaphimba masana, nthaŵi iliyonse pamene ankanyamuka pamahemapo.
35
Nthaŵi iliyonse pamene Bokosi lachipangano linkanyamuka, Mose ankati, “Dzambatukani, Inu Chauta, muŵamwaze adani anu. Onse odana nanu athaŵe akakuwonani.”
36
Mtambowo ukaima, Mose ankati, “Inu Chauta, bwererani kwa Aisraele anu amene ali zikwi zosaŵerengeka.”
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36