bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 25
Numbers 25
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 26 →
1
Pamene Aisraele anali ku Sitimu, anthu aamuna adayamba kuchita dama ndi akazi a ku Mowabu.
2
Akaziwo ankaitana amuna ku nsembe za milungu yao, ndipo amunawo ankadya nawo, ndi kumapembedza milungu yaoyo.
3
Choncho Aisraele adapembedza nao Baala wa ku Peori, ndipo Chauta adaŵapsera mtima Aisraele.
4
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Utenge atsogoleri onse a Aisraele ndipo uŵanyonge poyera pamaso panga, kuti ndileke kukwiyira Israele.”
5
Apo Mose adauza oweruza a Aisraele kuti, “Aliyense mwa inu aphe anthu ake amene adapembedza nao Baala wa ku Peori.”
6
Tsono Mwisraele wina adabwera ndi mkazi Wachimidiyani kubanja kwake, Mose ndi Aisraele onse akupenya, pamene ankalira pakhomo pa chihema chamsonkhano.
7
Finehasi mwana wa Eleazara, mdzukulu wa Aroni, ataona zimenezo, adadzuka nasiya mpingowo, nakatenga mkondo.
8
Ndipo adatsatira Mwisraele uja mpaka kukaloŵa m'chipinda cham'kati, nabaya onse aŵiriwo, Mwisraeleyo pamodzi ndi mkaziyo. Motero mliri udaleka pakati pa Aisraele.
9
Komabe anthu okwanira 24,000 anali atafa kale ndi mliriwo.
10
Chauta adauza Mose kuti,
11
“Finehasi mwana wa Eleazara, mdzukulu wa Aroni, wandiletsa kuti ndisaŵaononge Aisraele, chifukwa choti sadalole kuti wina aliyense apembedze mulungu wina koma Ine, nchifukwa chake sindidaŵaononge ndili wokwiya.
12
Motero umuuze kuti ndikupangana naye tsopano chipangano chamtendere.
13
Ndikupangana naye iyeyu ndi zidzukulu zake zonse, chipangano cha unsembe wamuyaya, chifukwa sadalole kuti anthu aukire Ine Mulungu, ndipo adachita ntchito yopepesera machimo a Aisraele.”
14
Mwisraele amene adaphedwa pamodzi ndi mkazi Wachimidiyani uja anali Zimiri mwana wa Salu, mtsogoleri wa banja la makolo a Asimeoni.
15
Ndipo mkazi Wachimidiyani amene adaphedwayo anali Kozibi mwana wa Zuri, amene anali mtsogoleri wa mbumba ina ya fuko la ku Midiyani.
16
Chauta adauza Mose kuti,
17
“Uŵathire nkhondo Amidiyani, ndiponso uŵaononge
18
chifukwa choti adakuchitani zachabe pokunyengani ku Peori, ndiponso chifukwa cha nkhani ya mlongo wao Kozibi, mwana wamkazi wa mfumu ya ku Midiyani, amene adaphedwa pa nthaŵi ya mliri chifukwa cha zochitika ku Peori zija.”
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36