bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 20
Numbers 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 21 →
1
Pa mwezi woyamba, mpingo wonse wa Aisraele udafika ku chipululu cha Zini, ndipo anthuwo adakhala ku Kadesi. Miriyamu adafera kumeneko naikidwa komweko.
2
Kumeneko kunalibe madzi oti mpingowo umwe. Tsono anthu adasonkhana pamodzi naukira Mose ndi Aroni.
3
Anthuwo adayamba kukangana ndi Mose, adati, “Kukadakhala bwino tikadafera pamodzi ndi abale athu aja amene adafa pamaso pa Chauta.
4
Chifukwa chiyani mwafikitsa mpingo wa Chauta kuchipululu kuno, kuti ife tifere kuno pamodzi ndi zoŵeta zathu?
5
Ndipo chifukwa chiyani mudatitulutsa m'dziko la Ejipito ndi kutifikitsa ku malo oipa ano? Kuno sikumera tirigu kapena mitengo ya mikuyu, kapena mitengo ya mipesa, kapenanso mitengo ya makangaza, ndipo kulibe ndi madzi akumwa omwe.”
6
Apo Mose ndi Aroni adachoka pa msonkhano uja, napita ku khomo la chihema chamsonkhano, ndipo adadziponya pansi. Pomwepo ulemerero wa Chauta udaŵaonekera.
7
Tsono Chauta adauza Mose kuti,
8
“Tenga ndodo, ndipo iwe ndi mbale wako Aroni musonkhanitse mpingo, tsono ulamule thanthwe kuti litulutse madzi, anthu akuwona. Motero udzaŵatulutsira madzi m'thanthwe anthuwo, ndipo udzamwetsa mpingo wonsewo ndi zoŵeta zao zomwe.”
9
Pamenepo Mose adatenga ndodo imene inali pamaso pa Chauta, monga momwe Iyeyo adamlamulira.
10
Tsono Mose ndi Aroni adasonkhanitsa mpingo wonse pamodzi kuthanthweko nauza anthuwo kuti, “Imvani anthu opandukanu. Kodi tichite kukutulutsirani madzi m'thanthwemu?”
11
Apo Mose adakweza dzanja lake, namenya thanthwe kaŵiri ndi ndodo yake. Pompo mudatuluka madzi ambiri, ndipo mpingo wonsewo udamwa pamodzi ndi zoŵeta zomwe.
12
Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Popeza kuti simudandikhulupirire, ndipo simudasonyeze pamaso pa Aisraele kuti ndine woyera, simudzaŵaloŵetsa anthuŵa m'dziko limene ndaŵapatsa.”
13
Ameneŵa ndiwo madzi a ku Meriba kumene Aisraele adakangana ndi Chauta, ndipo Chauta adadziwonetsa pakati pa anthuwo kuti ndi woyera.
14
Ali ku Kadesi, Mose adatuma amithenga kwa mfumu ya ku Edomu kuti akanene kuti, “Abale anu Aisraele akuti, ‘Mukudziŵa mavuto onse amene atigwera,
15
Pajatu makolo athu adaapita ku Ejipito, ndipo tidakhala kumeneko zaka zambiri. Aejipito adatizunza ife ndi makolo athu.
16
Titalira kwa Chauta, adamva kulira kwathu, natuma mngelo amene adatitulutsa m'dziko la Ejipitolo. Tsopano tili kuno ku Kadesi, mzinda umene uli m'malire a dziko lanu.
17
Mutilole tsono tidzere m'dziko mwanu. Sitidzera m'minda mwanu kapena m'mipesa mwanu. Ndipo sitidzamwa madzi a m'zitsime zanu. Tidzangodzera mu mseu wanu waukuluwo basi, mpaka titadutsa dziko lanu.’ ”
18
Koma Edomu adayankha kuti, “Musadzere kuno, kuti ndingafike kudzakubayani ndi lupanga.”
19
Aisraele adamuuza kuti, “Ife tidzangodzera mu mseu waukulu mokhamo. Ngati ife ndi zoŵeta zathu timwako madzi anu, tidzalipira. Mungotilola kuti tidutse chabe.”
20
Koma Edomu adaŵayankha kuti, “Simudutsa ai.” Pamenepo Edomu adatuluka ndi gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu kukalimbana ndi Aisraele.
21
Motero Edomu sadavomere kuti Aisraele adutse m'dziko mwake. Ndipo Aisraele adadzera njira ina.
22
Tsono mpingo wonse wa Aisraele udanyamuka ku Kadesi kuja nukafika ku phiri la Horo.
23
Ku phiri limenelo, limene lili m'malire a dziko la Edomu, Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,
24
“Aroni saloŵa nao m'dziko limene ndidapatsa Aisraele. Adzafa, chifukwa choti nonse aŵirinu simudamvere lamulo langa ku madzi a ku Meriba kuja.
25
Utenge Aroni pamodzi ndi Eleazara mwana wake, ukwere nawo pamwamba pa phiri la Horo.
26
Kumeneko umvule Aroni zovala zaunsembe ndi kuveka mwana wake Eleazara. Ndipo Aroni adzafera komweko.”
27
Mose adachitadi zimene Chauta adamlamula. Atatu onsewo adakwera phiri la Horo, mpingo wonse ukupenya.
28
Apo Mose adamuvula Aroni zovala zake zaunsembe, naveka Eleazara mwana wake. Ndipo Aroni adafera pamwamba pa phiri pomwepo. Tsono Mose ndi Eleazara adatsika phiri.
29
Pamene mpingo udamva kuti Aroni wamwalira, mpingo wonse wa Israele udalira maliro a Aroni masiku makumi atatu.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36