bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 21
Numbers 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 22 →
1
Mfumu Yachikanani ya ku Aradi imene inkakhala kumwera, itamva kuti Aisraele akubwera, kudzera njira ya ku Atarimu, idathira nkhondo Aisraelewo, nigwirako ena ukapolo.
2
Tsono Aisraele adalumbira kwa Chauta kuti, “Ngati muŵapereka anthu ameneŵa m'manja mwathu, ife tidzaonongeratu mizinda yao.”
3
Chauta adamvera mau a Aisraelewo naŵaperekadi Akanani aja m'manja mwao. Aisraele adaŵaonongeratu Akananiwo pamodzi ndi mizinda yao yomwe. Choncho malowo adaŵatcha kuti Horoma.
4
Aisraele adanyamuka ku phiri la Horo nadzera njira ya ku Nyanja Yofiira, kuzungulira dziko la Edomu. Koma pa njira adayamba kunyong'onyeka.
5
Anthu aja adayamba kuŵiringulira Mulungu ndiponso Mose, adati, “Chifukwa chiyani mudatitulutsa m'dziko la Ejipito kuti tidzafere m'chipululu muno? Pakuti kuno kulibe ndi chakudya chomwe ngakhalenso madzi, ndipo chakudya chachabechi chatikola.”
6
Tsono Chauta adatumiza njoka za ululu wonga moto pakati pa anthu aja, ndipo zidaŵaluma, kotero kuti Aisraele ambiri adafa.
7
Ndipo anthu adabwera kwa Mose, namuuza kuti, “Pepani tidachimwa poti tidakangana ndi Chauta ndi inu nomwe. Mupemphere kwa Chauta kuti atichotsere njokazi.” Choncho Mose adaŵapempherera anthuwo.
8
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Upange njoka yamkuŵa, ndipo uipachike pa mtengo. Aliyense wolumidwa akangoiyang'ana njokayo, adzakhala moyo.”
9
Choncho Mose adapanga njoka yamkuŵa, naipachika pa mtengo. Ndiye ankati wina aliyense njoka ikamuluma, munthuyo akayang'ana njoka yamkuŵa ija, ankakhala moyo.
10
Aisraele adanyamukanso, nakamanga mahema ao ku Oboti.
11
Ndipo adachoka ku Oboti nakamanga ku Iyeabarimu m'chipululu choyang'anana ndi Mowabu, kuvuma.
12
Atachoka kumeneko, adakamanga m'chigwa cha Zeredi.
13
Kuchokera kumeneko adakamanga patsidya pa mtsinje wa Arinoni umene uli m'chipululu chochokera ku malire a dziko la Amori. Mtsinje wa Arinoni umene ndiwo malire a Mowabu, uli pakati pa dziko la Mowabu ndi dziko la Amori.
14
Nchifukwa chake buku la nkhondo za Chauta limanena kuti, “Mzinda wa Waheba uli ku Sufa, ku zigwa za Arinoni,
15
ku matsitso a zigwa amene afika mpaka ku Ari, nakhudza malire a dziko la Mowabu.”
16
Kuchokera kumeneko adapitirira mpaka ku malo oti Beeri. Chimenecho chinali chitsime chimene Chauta adaalozera Mose namuuza kuti, “Uŵasonkhanitse pamodzi anthuwo, ndipo ndidzaŵapatsa madzi.”
17
Tsono Aisraele adaimba nyimbo iyi yakuti, “Tulutsa madzi ako, chitsime iwe, ife tiŵaimbira nyimbo!
18
Chitsime chimene adakumba mafumu, chimene atsogoleri omveka a anthu adakumba, adakumba ndi ndodo zao zaufumu ndiponso ndi ndodo zao zoyendera.” Kuchokera kuchipululu, Aisraele adafika ku Matana,
19
kuchokera ku Matana adafika ku Nahaliyele, kuchokera ku Nahaliyele adafika ku Bamoti.
20
Kuchokera ku Bamoti adafika ku chigwa cha m'dziko la Mowabu, kudzera njira ya pamwamba pa phiri la Pisiga, loyang'anana ndi chipululu cham'munsi.
21
Tsono Aisraele adatuma amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, kukanena kuti,
22
“Mutilole kuti tidzere m'dziko mwanumo. Sitidzadzera m'minda mwanu, kapena m'mipesa mwanu. Sitidzamwa madzi a m'chitsime chanu. Tidzangotsata mseu wanu waukulu mpaka titadutsa dziko lanulo.”
23
Koma Sihoni sadalole kuti Aisraele adutse dziko lake. Adasonkhanitsa anthu ake onse pamodzi, napita kukamenyana nkhondo ndi Aisraele kuchipululu, ndipo adafika ku Yahazi, namenyana ndi Aisraele.
24
Ndipo Aisraele adamgonjetsa ndi lupanga, nalanda dziko lake kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki, kufikira m'malire a dziko la Aamori, chifukwa malirewo anali otchinjirizidwa.
25
Aisraele adalanda mizinda yonseyi nakhala m'mizinda yonse ya Aamori, ku Hesiboni ndi m'midzi yake yonse.
26
Hesiboni unali mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, amene adaamenyana ndi mfumu yakale ya Amowabu, ndipo adamlanda dziko lake lonse mpaka ku mtsinje wa Arinoni.
27
Nchifukwa chake oimba ndakatulo amati, “Bwerani ku Hesiboni, mzindawu umangidwenso, tiyeni timange mzinda wa Sihoni kuti ukhazikikenso.
28
Moto udabuka ku Hesiboni. Malaŵi a moto adatuluka mu mzinda wa Sihoni. Moto udaononga Ari mzinda wa ku Mowabu, udapserezeratu mapiri a kumtunda kwa Arinoni.
29
Tsoka kwa iwe Mowabu, mwatha inu anthu opembedza Kemosi. Ana ake aamuna waasandutsa othaŵathaŵa, ana ake aakazi waasandutsa akapolo, akapolo a Sihoni mfumu ya Aamori.
30
Choncho zidzukulu zao zidatha nkufa, kuyambira ku Hesiboni mpaka ku Diboni, ndipo tidaŵaononga mpaka ku Nofa, pafupi ndi Medeba.”
31
Motero Aisraele adakhala m'dziko la Aamori.
32
Mose adatuma anthu kuti akazonde Yazere. Ndipo Aisraele adagwira midzi yake, napirikitsa Aamori amene anali kumeneko.
33
Tsono adabwerera, nadzera njira ya ku Basani. Ogi mfumu ya ku Basaniko adatuluka kukalimbana nawo. Iyeyo pamodzi ndi anthu ake onse adakamenyana nawo nkhondo ku Ederei.
34
Koma Chauta adauza Mose kuti, “Usamuwope. Ndampereka m'manja mwako pamodzi ndi anthu ake onse ndi dziko lake lomwe. Ndipo umchite zomwe udachita Sihoni mfumu ya Aamori amene ankakhala ku Hesiboni.”
35
Choncho Aisraele adapha Ogi, ana ake aamuna ndi anthu ake onse, kotero kuti panalibe ndi mmodzi yemwe amene adatsalira, ndipo adalanda dziko lakelo.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36