bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 8
Numbers 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 9 →
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Uza Aroni kuti, pamene ukuika nyale, uike zisanu ndi ziŵiri, ndipo ziwunikire patsogolo pa choikaponyale.”
3
Aroni adaikadi nyalezo. Adaziika kuti ziwunikire patsogolo pa choikaponyale, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
4
Choikaponyalecho adachipanga motere: chinali chagolide, ndipo kuyambira patsinde pake mpaka ku maluŵa ake, chinali chosula. Adapanga choikaponyalecho potsata chitsanzo chomwe Chauta adaaonetsa Mose.
5
Chauta adauza Mose kuti,
6
“Upatule Alevi pakati pa Aisraele, ndipo uŵayeretse.
7
Kuŵayeretsa kwake uchite motere: uŵawaze madzi oyeretsera machimo ao. Amete m'thupi monse ndi lumo, ndipo achape zovala kuti adziyeretse.
8
Tsono iwowo atenge mwanawang'ombe wamphongo, pamodzi ndi chopereka cha chakudya wosalala wosakaniza ndi mafuta. Iweyo utenge mwanawang'ombe wina wamphongo woperekera nsembe yopepesera machimo.
9
Ubwere ndi Alevi pakhomo pa chihema chamsonkhano, ndipo usonkhanitse mpingo wonse wa Aisraele.
10
Pamene ukuŵapereka Aleviwo pamaso pa Chauta, Aisraele asanjike manja ao pa Alevi.
11
Kenaka Aroni apereke Aleviwo pamaso pa Chauta, kuti akhale chopereka choweyula cha Aisraele, kuti ntchito ya Alevi ikhaledi yotumikira Chauta.
12
Pambuyo pake Alevi asanjike manja ao pamitu ya ng'ombe zamphongo, ndipo iwe upereke kwa Chauta ng'ombe imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Inayo uipereke kuti ikhale nsembe yopsereza, kuchitira mwambo wopepesera machimo a Alevi.
13
Uŵauze Aleviwo kuti azitumikira Aroni ndi ana ake aamuna, ndipo uŵapereke kwa Chauta ngati chopereka choweyula.
14
“Umu ndi m'mene upatulire Alevi pakati pa Aisraele, ndipo adzakhala anga.
15
Pambuyo pake Aleviwo adzaloŵa kuti atumikire m'chihema chamsonkhano, utaŵayeretsa ndi kuŵapereka ngati chopereka choweyula.
16
Ndithudi, iwoŵa aperekedwa kwathunthu kwa Ine pakati pa Aisraele. Ndaŵatenga kuti akhale anga m'malo mwa ana onse oyamba kubadwa, ana achisamba onse a Aisraele.
17
Ana onse oyamba kubadwa pakati pa Aisraele ndi anga, ana a anthu ndi a nyama omwe. Ndidaŵapatula onseŵa kuti akhale anga, pa tsiku limene ndidapha ana onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito.
18
Tsono pakati pa Aisraele ndaŵatenga Alevi m'malo mwa ana onse oyamba kubadwa.
19
Aleviwo ndaŵatenga pakati pa Aisraele ndi kuŵapereka ngati mphatso kwa Aroni ndi ana ake aamuna, kuti azidzatumikira m'malo mwa Aisraele, m'chihema chamsonkhano. Azikachita mwambo wopepesera machimo a Aisraele, kuti mliri ungaŵagwere Aisraele amene ayandikire pafupi ndi malo opatulika.”
20
Umu ndimo m'mene Mose ndi Aroni ndi mpingo wonse wa Aisraele, adaŵachitira Alevi. Aisraele adachitira Aleviwo zonse monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
21
Alevi adadziyeretsa ku zoipa, ndipo adachapa zovala zao. Aroni adaŵapereka kuti akhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta, naŵachitira mwambo wopepesera machimo ao, kuti aŵayeretse.
22
Pambuyo pake Alevi adapita kukagwira ntchito zao m'chihema chamsonkhano, ndipo ankatumikira Aroni ndi ana ake. Choncho Aleviwo adaŵachitira monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
23
Chauta adauza Mose kuti,
24
“Ntchito za Alevi ndi izi: kuyambira anthu a zaka 25 ndi opitirirapo, azipita kukagwira ntchito yotumikira m'chihema chamsonkhano.
25
Akafika zaka makumi asanu aleke ntchito yotumikira, ndipo asatumikirenso.
26
Koma azithandiza abale ao m'chihema chamsonkhano ndi kumayang'anira ntchitoyo, koma asatumikire. Umu ndimo m'mene udzachitire poŵagaŵira ntchito zao Aleviwo.”
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36