bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 35
Numbers 35
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 34
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 36 →
1
Chauta adauza Mose m'zigwa za Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani, ku Yeriko, kuti,
2
“Ulamule Aisraele kuti pa choloŵa chaocho, apatseko Alevi mizinda yoti azikhalamo. Ndipo Aleviwo muŵapatsenso mabusa pozungulira mizindayo.
3
Mizindayo idzakhala yao yoti azikhalamo, ndipo mabusa ao adzakhala odyetseramo ng'ombe zao, zoŵeta zao ndi nyama zao zonse.
4
Mabusa a mizindayo amene mudzapatse Aleviwo, adzayambire ku khoma la mzinda, adzatuluke kunja mamita 450, kuzungulira mzindawo.
5
Uyese kunja kwa mzindawo, kuvuma mamita 900, kumwera mamita 900, kuzambwe mamita 900, kumpoto mamita 900, ndipo mzindawo ukhale pakati. Dziko limeneli lidzakhala busa la mizinda yaoyo.”
6
“Mizinda imene mudzapatse Aleviyo idzakhale mizinda isanu ndi umodzi yothaŵirako, kumene muzidzalola kuti munthu wopha mnzake mwangozi athaŵireko. Ndipo mudzaŵapatsenso mizinda ina 42, kuwonjezera pa mizinda imeneyo.
7
Mizinda imene mudzapatse Alevi idzakhale 48 yonse pamodzi, kuphatikizanso ndi mabusa ao.
8
Pamene mukupatula mizinda imeneyi pa choloŵa cha Aisraele, muchotse mizinda yambiri pa mafuko aakulu, ndipo muchotse mizinda pang'ono pa mafuko aang'ono. Fuko lililonse lidzapereka kwa Alevi molingana ndi kukula kwa choloŵa chimene lalandira.”
9
Tsono Chauta adauza Mose kuti,
10
“Uza Aisraele kuti: Pamene muwoloka mtsinje wa Yordani ndi kuloŵa m'dziko la Kanani,
11
mupatule mizinda ina kuti ikhale mizinda yanu yothaŵirako, kumene munthu wopha mnzake mwangozi azithaŵirako.
12
Mizindayo idzakhala malo obisalamo pothaŵa munthu wofuna kubwezera choipa, kuti munthu wopha mnzake mwangoziyo asaphedwe, mpaka akaime pamaso pa mpingo kuti umuweruze.
13
Mizinda imene mudzaperekeyo idzakhala mizinda isanu ndi umodzi yothaŵirako.
14
Mudzapereke mizinda itatu patsidya la kuvuma la mtsinje wa Yordani, ndi mizinda itatu m'dziko la Kanani, kuti ikhale mizinda yothaŵirako.
15
Mizinda isanu ndi umodziyo idzakhala yothaŵirako Aisraele, alendo ndi anthu okhala pakati pao, kuti wina aliyense wopha munthu mnzake mwangozi azithaŵirako.
16
“Koma ngati munthu amenya mnzake ndi chitsulo, mnzakeyo nkufa, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Ndipo wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa.
17
Ngati munthu amenya mnzake ndi mwala, mwala wake woti nkupha munthu, mnzakeyo nafadi, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Tsono wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa.
18
Kapena munthu akamenya mnzake ndi chibonga choti nkupha munthu, mnzakeyo nafadi, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Tsono wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa.
19
Mbale wake wa munthu wakufayo ndiye adzaphe wopha mnzakeyo. Akadzangokumana, wopha mnzakeyo adzamuphe ndi munthu wolipsira magaziyo.
20
Ndipo ngati munthu abaya mnzake chifukwa cha chidani, kapena amulasa ndi chida atamubisalira, mnzakeyo naafa,
21
kapena kumpanda ndi dzanja lake modana naye, mnzakeyo naafa, ndiye kuti amene adamenya mnzakeyo ayenera kuphedwa. Ndi wopha munthu ameneyo. Mbale wa munthu wakufayo ndiye aphe wopha mnzakeyo akangokumana naye.
22
“Koma ngati munthu abaya mnzake mwangozi osati chifukwa cha chidani, kapena alasa mnzake ndi chida osamubisalira,
23
kapena amulasa ndi mwala woti nkupha munthu, koma amlasa osamuwona mnzakeyo,
24
pamenepo mpingo uweruze pakati pa munthu wopha mnzakeyo ndi mbale wa munthu wakufayo, potsata malangizo ameneŵa.
25
Mpingo umpulumutse munthu wopha mnzakeyo m'manja mwa mbale wa munthu wakufayo. Ndipo um'bweze munthuyo ku mzinda wake wothaŵirako kumene adathaŵira. Adzakhala komweko mpaka mkulu wa ansembe onse atamwalira.
26
Koma ngati munthu wopha mnzake mwangoziyo atuluka nthaŵi iliyonse kunja kwa malire a mzinda umene adathaŵiramo,
27
ndipo mbale wa munthu wakufa uja ampeza ali kunja kwa malire a mzindawo, nkupha wopha mnzake uja, sadzapalamula mlandu wopha munthu.
28
Pajatu munthuyo ayenera kukhala mu mzinda umene adathaŵiramo mpaka mkulu wa ansembe onse atamwalira. Koma mkulu wa ansembe onse atamwalira, wopha mnzakeyo angathe kubwerera ku dziko lake.
29
“Zimenezi zikhale malamulo ndi malangizo kwa inu pa mibadwo yanu yonse kulikonse kumene mukakhale.
30
Ngati wina aliyense apha mnzake, wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa, mboni zitapereka umboni wao. Koma munthu asaphedwe pamene munthu mmodzi yekha wapereka umboni.
31
Kuwonjezera apo, musalandire dipo loombolera munthu wopha mnzake amene wapalamula mlandu wopha munthu. Koma munthu ameneyo ayenera kuphedwa ndithu.
32
Ndipo musalandire dipo loombolera munthu amene ali mu mzinda wake wothaŵirako kuti abwerere ndi kukakhala ku dziko lake, mkulu wa ansembeyo asanamwalire.
33
Musaipitse dziko limene mukukhalamolo. Magazi amaipitsa dziko, ndipo nkosatheka kulipirira dziko chifukwa cha magazi amene akhetsedwa m'menemo, kupatula pokhetsa magazi a munthu amene adakhetsa magaziyo.
34
Musaipitse dziko limene mukukhalamo, dziko limene Inenso ndikukhalamo. Paja Ine Chauta ndimakhala pakati pa Aisraele.”
← Chapter 34
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 36 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36