bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 3
Numbers 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 4 →
1
Nayi mibadwo ya Aroni ndi Mose pa nthaŵi imene Chauta adalankhula ndi Mose pa phiri la Sinai.
2
Maina a ana a Aroni naŵa: Nadabu mwana wake wachisamba, Abihu, Eleazara ndi Itamara.
3
Ameneŵa ndiwo maina a ana a Aroni, ansembe odzozedwa amene iye adaŵasankha kuti azitumikira pa ntchito yaunsembe.
4
Koma Nadabu ndi Abihu adafa pamaso pa Chauta pamene adapereka moto wosaloledwa pamaso pa Chauta m'chipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana, ndipo choncho Eleazara ndi Itamara adatumikira pa ntchito yaunsembe pa nthaŵi imene Aroni bambo wao anali moyo.
5
Chauta adauza Mose kuti,
6
“Bwera nawo anthu a fuko la Levi, ndipo uŵapereke kwa wansembe Aroni kuti azimtumikira.
7
Azigwirira ntchito iyeyo ndi mpingo wonse, pakhomo pa chihema chamsonkhano, monga momwe amachitira potumikira m'Chihema cha Mulungu.
8
Aziyang'anira zipangizo zonse za m'chihema chamsonkhano, ndipo azigwirira Aisraele ntchito potumikira m'Chihema cha Mulungu.
9
Aleviwo uŵapereke kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna. Uŵapereke kwathunthu kwa iyeyo, kuŵachotsa pakati pa Aisraele.
10
Umusankhe Aroni ndi ana ake, kuti azitumikira pa ntchito yaunsembe. Koma wina aliyense akayandikira pafupi, aphedwe.”
11
Chauta adauza Mose kuti,
12
“Pakati pa Aisraele, ndaŵapatula Alevi, m'malo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa, amene amatsekula mimba ya mai wake. Aleviwo ndi anga,
13
pakuti ana onse aamuna oyamba kubadwa ndi anga. Pa tsiku lija lomwe ndidapha ana onse aamuna oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, ndidadzipatulira ana onse oyamba kubadwa a m'dziko la Israele, ana a anthu ndi a nyama omwe. Onsewo ndi anga, Ine ndine Chauta.”
14
Chauta adauza Mose m'chipululu cha Sinai kuti,
15
“Uŵerenge ana aamuna a Levi potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Uŵerenge wamwamuna aliyense kuyambira wa mwezi umodzi ndi wopitirirapo.”
16
Choncho Mose adaŵaŵerenga potsata mau a Chauta monga momwe adamlamulira.
17
Maina a ana a Leviwo ndi aŵa: Geresoni, Kohati ndi Merari.
18
Tsono ana a Geresoni potsata mabanja ao naŵa: Labini ndi Simei.
19
Ana a Kohati potsata mabanja ao ndi aŵa: Amuramu, Izara, Hebroni ndi Uziyele.
20
Ndipo ana a Merari potsata mabanja ao ndi aŵa: Mali ndi Musi. Ameneŵa ndiwo mabanja a Levi potsata banja la makolo ao.
21
Alibini ndi Asimei anali mabanja otuluka mwa Geresoni. Ameneŵa ndiwo anali mabanja a Ageresoni.
22
Chiŵerengero chao potsata kuchuluka kwa amuna onse, kuyambira mwana wamwamuna wa mwezi umodzi ndi wopitirapo, chinali 7,500.
23
Mabanja a Geresoni ankamanga zithando zao kumbuyo kwa chihema cha Mulungu mbali yakuzambwe.
24
Eliyasafu mwana wa Laele ndiye anali mtsogoleri wa banja la makolo a Ageresoni.
25
Ndipo ntchito imene ana a Geresoni adapatsidwa m'chihema chamsonkhano inali yosamala chihema cha Mulungu, pamodzi ndi chophimbira chake, nsalu yochinga pakhomo pa chihema chamsonkhano,
26
nsalu zochingira bwalo, nsalu zochingira khomo la bwalo lozungulira chihema cha Mulungu ndi guwa lansembe, ndiponso zingwe zake. Ankagwira ntchito zonse zokhudza zimenezi.
27
Aamuramu, Aizari, Ahebroni ndi Auziyele, anali mabanja otuluka mwa Kohati. Ameneŵa ndiwo amene anali mabanja a Akohati.
28
Potsata chiŵerengero cha amuna onse kuyambira mwana wamwamuna wa mwezi umodzi ndi wopitirirapo, onse anali 8,600, amene ankagwira ntchito m'malo opatulika.
29
Mabanja a ana a Kohati ankamanga zithando zao kumwera kwa chihema cha Mulungu,
30
pamodzi ndi Elizafani, mwana wa Uziyele, amene anali mutu wa mabanja a Akohati,
31
Ndipo ntchito imene iwo adapatsidwa inali yosamala Bokosi lachipangano, tebulo, choikaponyale, maguwa, zipangizo za m'malo opatulika zimene ansembe ankagwirira ntchito, pamodzi ndi nsalu yochingira. Ankagwira ntchito zonse zokhudza zimenezi.
32
Tsono Eleazara mwana wa wansembe Aroni, ndiye amene anali mkulu wa atsogoleri a Alevi, ndiponso amene ankayang'anira iwo amene ankasamala malo opatulika.
33
Amali ndi Amusi anali mabanja otuluka mwa Merari. Ameneŵa ndiwo amene anali mabanja a Merari.
34
Chiŵerengero chao potsata kuchuluka kwa amuna onse, kuyambira mwana wamwamuna wa mwezi umodzi ndi wopitirirapo, chinali 6,200.
35
Ndipo munthu amene anali mutu wa mabanja a Merari anali Zuriyele mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga zithando zao kumpoto kwa chihema cha Mulungu.
36
Ntchito imene ana aamuna a Merari adapatsidwa, inali yosamala mitengo ya malo opatulika monga: nsichi zake, mizati yake, masinde ake ndi zina zonse zoyendera limodzi ndi zimenezo. Ankayang'anira ntchito zonse zokhudza zimenezi.
37
Ankasamalanso mizati yozungulira bwalo ndi masinde ake, ndiponso zikhomo zake ndi zingwe zake.
38
Amene ankamanga zithando zao patsogolo pa chihema cha Mulungu kuvuma kotulukira dzuŵa, kutsogolo kwa chihema chamsonkhano, anali Mose ndi Aroni pamodzi ndi ana ake a Aroni. Iwoŵa adaŵapatsa udindo wosamala kayendetsedwe ka chipembedzo m'malo opatulika, zonse zimene ankayenera kuchita m'malo mwa Aisraele. Munthu wina aliyense wofika pafupi ankayenera kuphedwa.
39
Alevi onse amene Mose pamodzi ndi Aroni adaŵerenga potsata mabanja ao, Chauta ataŵalamula kutero, ndiye kuti amuna onse kuyambira a mwezi umodzi ndi opitirirapo, anali 22,000.
40
Chauta adauza Mose kuti, “Uŵerenge ana achisamba onse aamuna a Aisraele, kuyambira a mwezi umodzi ndi opitirirapo, potchula maina ao.
41
Tsono unditengere Alevi m'malo mwa ana achisamba onse pakati pa Aisraele, utengenso ng'ombe za Alevi m'malo mwa ana onse oyamba kubadwa pakati pa ng'ombe za Aisraele, Ine ndine Chauta.”
42
Choncho Mose adaŵerenga ana onse achisamba, monga Chauta adamlamula.
43
Ndipo ana onse achisamba aamuna, potsata chiŵerengero cha maina ao, kuyambira a mwezi umodzi ndi opitirirapo, adakwanira 22,273.
44
Chauta adauza Mose kuti,
45
“Utenge Alevi m'malo mwa ana onse achisamba pakati pa Aisraele, utengenso ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe za Aisraele. Aleviwo ndi anga, Ine ndine Chauta.
46
Pofuna kuwombola ana achisamba 273 a Aisraele amene aposa chiŵerengero cha amuna a fuko la Levi,
47
utenge masekeli asiliva asanu pa munthu aliyense. Masekeliwo akhale olingana ndi masekeli asiliva a ku malo opatulika kumene sekeli imodzi ikwanira magera makumi aŵiri.
48
Upatse Aroni pamodzi ndi ana ake aamuna ndalama zimenezi, kuti zikhale mtengo woombolera Aisraele a chiŵerengero chopitirira chija.”
49
Choncho Mose adatenga ndalama zoombolera zija kwa Aisraele amene chiŵerengero chao chidapitirira chiŵerengero cha amene adaomboledwa ndi Alevi.
50
Adatenga ndalama zasiliva kwa ana achisamba a Aisraele okwanira 1,365, molingana ndi kaŵerengedwe ka masekeli asiliva a ku Chihema cha Mulungu.
51
Ndipo Mose adapereka ndalama zoombolerazo kwa Aroni ndi kwa ana ake, potsata mau amene Chauta adalamula Mose.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36