bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 23
Numbers 23
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 24 →
1
Balamu adauza Balaki kuti, “Mundimangire maguwa asanu ndi aŵiri pano, ndipo mundikonzere ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri.”
2
Balaki adachitadi monga momwe adamuuzira Balamu. Ndipo Balaki pamodzi ndi Balamu adapereka ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo pa guwa lililonse.
3
Apo Balamu adauza Balaki kuti, “Imani pafupi ndi nsembe yanu yopsereza, tsono ine ndipite, mwina mwake Chauta abwera kudzakumana nane. Chilichonse chimene andiwonetse ndidzakuuzani.” Choncho adapita pamwamba pa phiri.
4
Mulungu adakumana ndi Balamu, ndipo Balamuyo adati, “Ndakonza maguwa asanu ndi aŵiri, ndipo pa guwa lililonse ndaperekapo ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo.”
5
Tsono Chauta adauza Balamu kuti “Bwerera kwa Balaki, ukamuuze izi! Izi”
6
Balamu adabwerera kwa Balaki, nampeza iyeyo pamodzi ndi akalonga onse a Amowabu ataima pafupi ndi nsembe yake yopsereza.
7
Apo Balamu adayamba kulankhula mau auneneri, adati, “Balaki mfumu ya ku Mowabu yandiitana kuchokera ku Aramu, ku mapiri akuvuma, kuti, ‘Bwerani, dzatemberereni Yakobe m'malo mwanga, bwerani mudzamfunire Israele zoipa.’
8
Koma ine ndingathe bwanji kumtemberera amene Mulungu sadamtemberere? Ndingathe bwanji kumufunira zoipa amene Chauta sadamfunire zoipa?
9
Pamene ndikuŵaona kuchokera pamwamba pa phiri, pamene ndikuŵayang'ana kuchokera ku mapiri, ndikuwona anthu okhala paokha, osadziŵerengera kumodzi ndi mitundu ina.
10
Ndani angathe kuŵerenga zidzukulu, zidzukulu za Yakobe zochuluka ngati fumbi, kapena kuŵerenga ngakhale chimodzi mwa zigawo zinai za fuko lonse la Israele? Lekeni ine ndife imfa ya anthu amene mudaŵalungamitsa, matsiriziro anga akhale onga a anthu amenewo.”
11
Balaki adafunsa Balamu kuti, “Mwandichitira zotani? Suja ndidakuitanani kuti mudzatemberere adani anga, koma m'malo mwake mwangoŵadalitsa.”
12
Iye adayankha kuti, “Kodi sindiyenera kulankhula zokhazo zimene Chauta adaika m'kamwa mwanga?”
13
Balaki adamuuzanso kuti, “Tiyeni tipite limodzi ku malo ena kumene mungathe kuŵaona Aisraelewo. Mukangoona okhawo amene ayandikira pafupi, koma simukaona onse. Tsono muŵatemberere m'malo mwanga, mutaima pamenepo.”
14
Adapita naye ku munda wa Zofimu pamwamba pa phiri la Pisiga, namangapo maguwa asanu ndi aŵiri, ndipo adapereka nsembe ya ng'ombe yamphongo ndi nsembe ya nkhosa yamphongo pa guwa lililonse.
15
Balamu adauza Balaki kuti, “Imani pano pafupi ndi nsembe yanu yopsereza, ine ndipite ndikakumane ndi Chauta apo.”
16
Chauta adakumana naye Balamu namuuza kuti, “Bwerera kwa Balaki, ndipo umuuze izi! Izi!”
17
Tsono adabwerera kwa Balaki, ndipo adangoona akuimirira pafupi ndi nsembe yake yopsereza, ali ndi akalonga a ku Mowabu aja. Balaki adamufunsa kuti, “Nanga Chauta wakuuzani zotani?”
18
Apo Balamu adayamba kulankhula mau auneneri, adati, “Dzukani, Balaki, ndipo mumve, mundimvere inu mwana wa Zipori.
19
Mulungu sali ngati munthu kuti angathe kunama, si munthu kuti angathe kusintha maganizo ake. Kodi sadzachitadi zomwe adanena? Kapena sadzachitadi zimene adalankhula?
20
Ndithu, ndalandira lamulo kuti ndidalitse. Iye wadalitsa, ndipo ine sindingathe kusintha kanthu.
21
Iye sadaone choipa mwa Yakobe, sadaone chovuta mwa Israele. Chauta wao ali nawo, ndipo pakati pao pali kufuula kuti Iye ndi mfumu yao.
22
Mulungu adaŵatulutsa m'dziko la Ejipito, ali ndi mphamvu zonga za njati.
23
Zanyanga sizingamchite kanthu Yakobe, zamaula sizingathe kulimbana ndi Israele. Tsono anthu polankhula za Yakobe ndi za Israele adzati, ‘Onani zimene Mulungu wachita.’
24
Onani Aisraele, kudzuka kwanu kuli ngati kwa mkango waukazi, kudzambatuka kwanu kuli ngati kwa mkango waumuna, umene sugona pansi mpaka utagwira nyama ndi kuidya ndi kumwa magazi ake a nyama yojiwayo.”
25
Balaki adauza Balamu kuti, “Musaŵatemberere, ndipo musaŵadalitse.”
26
Koma Balamu adafunsa Balakiyo kuti, “Kodi sindidakuuzeni kuti ndiyenera kuchita zonse zimene Chauta wandiwuza?”
27
Balaki adauza Balamu kuti, “Tiyeni limodzi tipite ku malo ena. Mwina mwake zidzamkondwetsa Mulungu kuti muŵatemberere m'malo mwanga, mutaima pamenepo.”
28
Choncho Balaki adatenga Balamu, napita naye pamwamba pa phiri la Peori loyang'anana ndi chipululu cham'munsi.
29
Tsono Balamu adauza Balaki kuti, “Mundimangire maguwa asanu ndi aŵiri pano, ndipo mundikonzere ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri.”
30
Balaki adachitadi monga momwe adamuuzira Balamu, napereka ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo pa guwa lililonse.
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36