bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 18
Numbers 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 19 →
1
Pambuyo pake Chauta adauza Aroni kuti, “Iwe pamodzi ndi ana ako ndi banja la makolo ako pamodzi nawe, ndinu amene musenze zotsatira za tchimo lililonse lokhudza malo opatulika kwambiri. Ndipo iwe ndi ana ako, ndinu amene musenze zotsatira za tchimo lililonse lokhudza unsembe.
2
Ubwere nawonso abale ako a fuko la Levi, fuko la kholo lako, kuti azigwira nawe ntchito, azikuthandiza iwe pamodzi ndi ana ako, pamene mukutumikira m'chihema chaumboni.
3
Iwowo adzakutumikirani ndi kugwiranso ntchito zonse zam'chihema. Koma asadzafike pafupi ndi zipangizo za m'malo opatulika kapena guwa, kuti iwowo pamodzi ndi inuyo mungafe.
4
Iwo adzagwira nawe ntchito, ndi kumatumikiranso m'chihema chamsonkhano pa ntchito zonse zam'chihemamo. Ndipo wina aliyense asadzafike pafupi ndi inu.
5
Mudzatumikira pa ntchito za m'malo opatulika ndi pa ntchito za guwa, kuti mkwiyo usaŵagwerenso Aisraele.
6
Ndaŵasankha abale ako, Alevi, pakati pa Aisraele. Iwowo ndi mphatso kwa iwe, aperekedwa kwa Chauta kuti azitumikira m'chihema chamsonkhano.
7
Tsono iwe pamodzi ndi ana ako, muzitumikira pa ntchito zaunsembe, ntchito zonse zokhudza guwa, ndi pa ntchito zonse za m'malo opatulika kwambiri. Ndakupatsa unsembe ngati mphatso yako, koma munthu wina aliyense wofika pafupi, adzaphedwa.”
8
Chauta adauzanso Aroni kuti, “Pa zopereka kwa Ine, ndakupatsa zotsala zimene amasunga, ndiye kuti zinthu zimene Aisraele amapatulira Ine. Ndakupatsa zimenezi kuti zikhale gawo lako ndi la ana ako, kuti zikhale zanu mpaka muyaya.
9
Mwa zopereka zoyera kopambana zimene sadazitenthe pa guwa, zanu zikhale izi: chepereka chonse cha chakudya, nsembe zao zonse zopepesera machimo ndi nsembe zao zonse zopepesera kupalamula, zimene amapereka kwa Ine, zonsezo zikhale zoyera kwa iwe ndi kwa ana ako.
10
Muzidyera ku malo opatulika kopambana. Mwamuna aliyense angathe kudyako. Zimenezi nzoyera kwa inu.
11
Zinanso zanu ndi izi: zopereka zao zamphatso, ndi zopereka zoweyula za Aisraele. Zimenezi ndazipereka kwa iwe, kwa ana ako aamuna, ndi kwa ana ako aakazi amene ali ndi iwe, kuti zikhale zanu mpaka muyaya. Munthu aliyense amene ali wosaipitsidwa angathe kudyako.
12
Ndakupatsani mafuta onse abwino kopambana, vinyo yense ndi mbeu zonse zabwino kwabasi, ndi zipatso zonse zoyamba zimene anthu amapereka kwa Chauta.
13
Mwa zinthu zonse za m'dziko mwako, zipatso zoyambirira kupsa zimene amapereka kwa Chauta, zimenezo zikhale zanu. Munthu aliyense wosaipitsidwa m'nyumba mwanu angathe kudyako.
14
Chinthu chilichonse chimene anthu amapatulira Chauta m'dziko la Israele chikhale chanu.
15
Chinthu chilichonse choyamba kubadwa, kaya ndi munthu kaya nyama, chimene amapereka kwa Chauta, chikhale chanu, Komabe mwana wamwamuna wachisamba muzimuwombola, ndiponso pakati pa nyama zosayenera kuzipereka ku nsembe, mwana wake woyamba kubadwa muzimuwombola.
16
(Muzimuwombola akakhala wa mwezi umodzi). Uike mtengo wake woombolera kuti ukhale ndalama zisanu zasiliva, molingana ndi ndalama za ku malo opatulika.
17
Koma mwanawang'ombe woyamba kubadwa kapena mwanawankhosa woyamba kubadwa, kapenanso mwanawambuzi woyamba kubadwa, musaŵaombole. Amenewo ngoyera. Muwaze magazi ao pa guwa, ndipo mutenthe mafuta ao kuti akhale nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.
18
Koma nyama yake ikhale yako, monga momwe imakhalira nganga yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja.
19
Zopereka zonse zoyera zimene Aisraele amapereka kwa Chauta ndakupatsa iwe, ana ako aamuna ndi ana ako aakazi ali ndi iwe. Zimenezi zikhale zako mpaka muyaya. Chimenechi ndicho chipangano chamuyaya pamaso pa Chauta, chochita ndi iwe ndi ana ako.”
20
Ndipo Chauta adauza Aroni kuti, “Iwe udzakhala wopanda choloŵa m'dziko mwao, ndiponso udzakhala wopanda gawo lililonse pakati pao. Ine ndine gawo lako ndi choloŵa chako pakati pa Aisraele.
21
“Ndaŵapatsa Alevi chachikhumi chilichonse m'dziko la Israele kuti chikhale chigawo chao, chifukwa cha ntchito imene akuigwira m'chihema chamsonkhano.
22
Kuyambira tsopano Aisraele asamafika pafupi ndi chihema chamsonkhano, kuti angachimwe ndipo angafe.
23
Koma Alevi ndiwo amene azitumikira m'chihema chamsonkhano, ndipo adzalangidwa ngati alakwa pa udindo wao. Limeneli likhale lamulo pa mibadwo yanu yonse. Aleviwo asakhale ndi chigawo pakati pa Aisraele.
24
Tsono chachikhumi chimene Aisraele amapereka kwa Chauta, ndapatsa Aleviwo kuti chikhale chigawo chao. Nchifukwa chake ndaŵauza kuti asadzakhale ndi chigawo pakati pa Aisraele.”
25
Chauta adauza Mose kuti,
26
“Uŵauzenso Alevi kuti, ‘Pamene mulandira kwa Aisraele chachikhumi chimene ndakupatsani kuti chikhale chigawo chanu, muperekeko chachikhumi cha chachikhumicho kuti chikhale nsembe kwa Chauta.
27
Ndipo chopereka chanucho chidzaŵerengedwa ngati tirigu woyamba kucha amene anthu amapuntha, ndiponso mphesa zoyamba kucha zimene amapsinya.
28
Choncho inunso muzipereka zopereka zanu kwa Chauta, zotapa pa chachikhumi chilichonse chimene mulandira kwa Aisraele. Pa zimene mwalandirazo mutengeko mphatso ya Chauta, ndipo mupatse wansembe Aroni.
29
Pa mphatso zonse zimene mwalandira, mupatuleko zake za Chauta, ndipo zimene mwapatulazo zikhale zabwino kopambana zina zonse.’
30
Nchifukwa chake uŵauze kuti, ‘Mutaperekako zabwino kopambana zina zonse, zotsalazo muziŵerengere kuti nzanu, monga tirigu woyamba kucha amene anthu amapuntha, ndiponso mphesa zoyamba kucha zimene amapsinya.
31
Mungathe kuzidyera pa malo aliwonse, inuyo ndi a m'banja mwanu. Zimenezo ndi mphotho yanu chifukwa cha ntchito imene mumagwira m'chihema chamsonkhano.
32
Ndipo simudzachimwa mukadya zimenezo, ngati mwapereka kale kwa Chauta zabwino kopambana zina zonse. Motero simudzanyoza zinthu zoyera za Aisraele ndipo simudzafa.’ ”
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36