bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 28
Numbers 28
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 29 →
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Lamula Aisraele, ndipo uŵauze kuti, ‘Muzisamala kupereka kwa Ine pa nthaŵi yake zopereka zanga, chakudya changa cha nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo londikomera.’
3
Ndipo uŵauzenso kuti, nsembe yotentha pa moto, yoti muzipereka kwa Chauta ndi iyi: Muzipereka anaankhosa aŵiri amphongo a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, kuti akhale nsembe yosalekeza.
4
Mwanawankhosa mmodzi muzimpereka m'maŵa, winayo muzimpereka madzulo.
5
Muziperekanso kilogaramu limodzi la ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta aolivi oyenga bwino okwanira lita limodzi.
6
Imeneyi ndiyo nsembe yopsereza imene idalamulidwa pa phiri la Sinai, kuti itulutse fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta.
7
Chopereka cha chakumwa pa nkhosa iliyonse chikhale yokwanira lita limodzi. Muzithira vinyo waukaliyo m'malo opatulika, kuchipereka kwa Chauta.
8
Mwanawankhosa wina uja muzimpereka madzulo, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa zonga zam'maŵa zija. Imeneyi ikhalenso nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.
9
“Pa tsiku la Sabata muzipereka anaankhosa aŵiri amphongo a chaka chimodzi opanda chilema. Muziperekanso makilogaramu aŵiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ngati chopereka cha chakudya, ndipo muziperekanso chopereka cha chakumwa.
10
Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza ya tsiku la Sabata lililonse, kuwonjezera pa nsembe zopsereza ndi pa zopereka za chakumwa za tsiku ndi tsiku zija.
11
“Pa tsiku loyamba la mwezi uliwonse, muzipereka nsembe yopsereza kwa Chauta. Nsembeyo ikhale ya anaang'ombe aŵiri amphongo, nkhosa imodzi yamphongo, anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi, opanda chilema.
12
Chopereka cha chakudya ikhale ya ufa wosalala wa makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta, pa ng'ombe yamphongo iliyonse. Muperekenso makilogaramu aŵiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa nkhosa yamphongoyo,
13
ndiponso kilogaramu limodzi la ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa mwanawankhosa aliyense. Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza yotulutsa fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta.
14
Chopereka cha chakumwa chikhale cha vinyo wokwanira malita aŵiri pa ng'ombe yamphongo iliyonse, ya vinyo wokwanira lita limodzi ndi theka pa nkhosa yamphongoyo, ndi ya vinyo wokwanira lita limodzi pa mwanawankhosa aliyense. Imeneyi ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse, pa miyezi yonse ya chaka.
15
Aperekenso tonde kuti akhale nsembe yopepesera machimo, yopereka kwa Chauta. Aipereke kuwonjezera pa nsembe zopsereza ndi zopereka za zakumwa za tsiku ndi tsiku.
16
“Tsiku la 14 la mwezi woyamba, ndi la Paska ya Chauta.
17
Ndipo pa tsiku la 15 la mwezi umenewu, ndi tsiku lachikondwerero. Azidya buledi wosafufumitsa masiku asanu ndi aŵiri.
18
Pa tsiku loyamba pazikhala msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito yotopetsa,
19
koma mupereke nsembe yotentha pa moto, nsembe yopsereza ya Chauta. Ikhale ya anaang'ombe aŵiri amphongo, nkhosa yamphongo imodzi ndi anaankhosa asanu ndi aŵiri a chaka chimodzi, opanda chilema.
20
Muperekenso chopereka cha chakudya wosakaniza ndi mafuta. Ufa wake ukhale wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongoyo,
21
ndiponso wa makilogaramu limodzi pa mwanawankhosa aliyense.
22
Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yochitira mwambo wopepesera machimo anu.
23
Muzipereka zimenezi kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zopereka nthaŵi yam'maŵa.
24
Motero pa masiku asanu ndi aŵiri muzipereka tsiku lililonse chakudya cha nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Muchipereke kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija pamodzi ndi zopereka za chakumwa.
25
Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa.
26
“Pa tsiku la zipatso zoyambirira kucha, pamene mukupereka chopereka cha chakudya chatsopano kwa Chauta, pa tsiku la chikondwerero cha masabata, muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa,
27
koma mupereke nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ikhale ya anaang'ombe aŵiri amphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi.
28
Muperekenso chopereka cha chakudya wosakaniza ndi mafuta, wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongoyo,
29
ndiponso wa kilogaramu limodzi pa mwanawankhosa aliyense.
30
Muperekenso tonde mmodzi wochitira mwambo wopepesera machimo anu.
31
Mupereke zimenezi pamodzi ndi zopereka za chakumwa, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija ndi chopereka cha chakudya. Musamale kuti nyamazo zikhale zopanda chilema.
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 29 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36