bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 9
Numbers 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 10 →
1
Pa mwezi woyamba wa chaka chachiŵiri Aisraele atatuluka m'dziko la Ejipito, Chauta adauza Mose m'chipululu cha Sinai kuti,
2
“Aisraele azichita Paska pa nthaŵi yake.
3
Muzichita Paska tsiku la 14 la mwezi uno, madzulo ake. Muzichita Paskayo potsata malamulo ake ndi malangizo ake onse.”
4
Choncho Mose adauza Aisraele kuti azichita Paska.
5
Ndipo Aisraele adachita Paska pa mwezi woyamba pa tsiku la 14, madzulo ake, m'chipululu cha Sinai. Adachita Paska monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
6
Panali anthu ena amene anali atadziipitsa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu, kotero kuti sadathe kuchita nao Paska pa tsikulo. Motero adabwerera kwa Mose ndi kwa Aroni pa tsiku lomwelo.
7
Anthuwo adauza Mose kuti, “Ife ndife oipitsidwa chifukwa tidakhudza mtembo wa munthu. Chifukwa chiyani tikuletsedwa kubwera ndi zopereka zathu kwa Chauta pa nthaŵi yake pakati pa anzathu Aisraele?”
8
Mose adayankha kuti, “Dikirani kuti ndimve zimene Chauta alamule za inu.”
9
Chauta adauza Mose kuti,
10
“Uza Aisraele kuti, munthu wina aliyense mwa inu, kapena mwa zidzukulu zanu, akadziipitsa pokhudza mtembo wa munthu, kapena akakhala paulendo, achitebe Paska ya Chauta.
11
Achite pa mwezi wachiŵiri, pa tsiku la 14, madzulo ake. Adye nyama ya Paskayo pamodzi ndi buledi wosafufumitsa ndi ndiwo zoŵaŵa zamasamba.
12
Asasiyeko nyamayo mpaka m'maŵa kapena kuphwanya mafupa ake. Achite Paskayo potsata malamulo ake onse.
13
Koma munthu amene sadadziipitse ndipo sali paulendo, komabe akana kuchita Paska, ameneyo achotsedwe pakati pa Aisraele, chifukwa sadabwere ndi zopereka zake kwa Chauta pa nthaŵi yake. Ameneyo adzalangidwa chifukwa cha tchimo lake.
14
Mlendo akakhala pakati panu, nafuna kuchita nao Paska ya Chauta, nayenso achite Paskayo potsata malamulo ake ndi malangizo ake. Kaya ndinu alendo kapena ndinu mbadwa, nonse mukhale ndi lamulo limodzi lokha.”
15
Pa tsiku limene adamanga malo opatulika, mtambo udaphimba malo opatulikawo, ndiye kuti chihema chaumboni chija. Madzulo aliwonse mpaka m'maŵa mwake, mtambowo unkaphimba malo opatulika uli ndi maonekedwe a moto.
16
Zinkachitika motero mosalekeza. Mtambowo unkaphimba chihema chamsonkhano masana, ndipo usiku unkaoneka ngati moto.
17
Mtambowo ukangokwera kuchoka pachihemapo, Aisraele ankanyamuka ulendo; ndipo pamene mtambowo unkakaima, Aisraele ankamanga mahema ao pamalo pamenepo.
18
Aisraele ankanyamuka ulendo wao Chauta akaŵalamula, ndipo ankamanga mahema ao Chauta akaŵalamula. Nthaŵi yonse pamene mtambowo unali pa chihemacho, iwo ankakhalabe m'mahema.
19
Ngakhale mtambowo ukhale masiku ambiri pamwamba pa chihemacho, Aisraele ankasungabe lamulo la Chauta, ndipo sankanyamuka.
20
Nthaŵi zina mtambowo unkaphimba masiku oŵerengeka, ndipo Aisraele ankakhalabe m'mahema potsata malamulo a Chauta. Tsono ankanyamuka ulendo Chauta akaŵalamula.
21
Nthaŵi zina mtambowo unkangophimba chihemacho kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. M'maŵa mwake mtambowo ukachoka, iwo ankanyamuka ulendo wao. Mwina mtambowo unkaphimba chihema chija tsiku lonse ndi usiku womwe, koma ukangochokapo, iwowo ankanyamuka ulendo wao.
22
Ngakhale mtambowo uphimbe pamwamba pa chihema cha Mulungu nkumakhala pomwepo masiku aŵiri kapena mwezi, kapena chaka, kapena nthaŵi yopitirirapo, Aisraele ankakhalabe m'mahema, ndipo sankanyamuka. Koma mtambowo ukangochokapo, iwo ankanyamuka ulendo.
23
Aisraele ankamanga mahema ao Chauta akaŵalamula, ndipo ankanyamuka ulendo wao Chauta akaŵalamula. Ankasunga lamulo la Chauta, loŵafikira kudzera mwa Mose.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36