bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 15
Numbers 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 16 →
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Uza Aisraele kuti, ‘Mukadzaloŵa m'dziko limene ndidzakupatsenilo,
3
mwina muzidzapereka ng'ombe kapena nkhosa kwa Chauta kuti zikhale nsembe yotentha pa moto, kapena yopsereza, kapena yopembedzera, kuti mukwaniritse zimene mudalonjeza molumbira. Mwina mudzazipereka kuti zikhale nsembe yaufulu kapena nsembe yopereka pa nthaŵi ya zikondwerero zosankhidwa, kuti zikhale nsembe zotulutsa fungo lokomera Chauta.
4
Tsono amene adzabwere ndi zoperekayo, adzapereke kwa Chauta chopereka cha chakudya, cholemera kilogaramu limodzi, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita limodzi.
5
Adzaperekenso vinyo wa chopereka cha chakumwa wokwanira lita limodzi pa mwanawankhosa aliyense, kuwonjezera pa nsembe yopsereza kapena pa nsembe yopembedzera.
6
Ikakhala nkhosa yamphongo, muzipereka chopereka cha chakudya cholemera makilogaramu aŵiri, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita limodzi ndi theka.
7
Pachopereka cha chakumwa, mudzapereka vinyo wokwanira lita limodzi ndi theka, kuti ikhale nsembe yotulutsa fungo lokomera Chauta.
8
Pamene mupereka ng'ombe yamphongo kwa Chauta, kuti ikhale nsembe yopsereza kapena nsembe yopembedzera, kapena kuti zichitikedi zimene mudalumbira, kapena kuti ikhale nsembe yachiyanjano,
9
muperekere kumodzi ndi ng'ombeyo chopereka cha chakudya cholemera makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta okwanira malita aŵiri.
10
Pachopereka cha chakumwa mupereke vinyo wokwanira malita aŵiri, kuti ikhale nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.’
11
“Umu ndimo m'mene zidzachitikire ndi ng'ombe yamphongo iliyonse, kapena nkhosa yamphongo, kapena mwanawankhosa aliyense kapena mwanawambuzi.
12
Zingachuluke chotani nyama zoperekedwazo, muchite choncho ndi nyama iliyonse, mpaka zonse kutha.
13
Mbadwa zonse zizichita motero pamene zikupereka nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.
14
Ngati ndi mlendo amene akhala pakati panu, kapena wina aliyense amene akhala pakati panu pa mibadwo yanu yonse, ndipo afuna kupereka nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta, azichita monga momwe muchitira inu.
15
Kunena za msonkhano wonse, pakhale lamulo limodzi lokha kwa inu ndi kwa alendo amene akhale pakati panu, lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse. Monga momwe muliri inu, alendonso ali momwemo pamaso pa Chauta.
16
Kwa inu ndi kwa mlendo wokhala pakati panu, pakhale lamulo limodzi ndi mwambo umodzi wokha.”
17
Chauta adauza Mose kuti,
18
“Uza Aisraele kuti, ‘Mukadzaloŵa m'dziko m'mene ndidzakufikitsani,
19
ndipo mukamadzadya buledi wam'dzikolo, mudzapereke nsembe kwa Chauta.
20
Pa buledi wanu woyamba, mudzaperekeko mmodzi kuti adzakhale nsembe. Mudzampereke monga momwe mumaperekera zopereka za popunthira tirigu.
21
Muzidzapereka motero kwa Chauta buledi mmodzi mwa buledi wanu woyamba pa mibadwo yanu yonse.’
22
“Koma mwina mutha kulakwa mosadziŵa, osasunga malamulo onse amene Chauta adauza Mose,
23
ndi zonse zimene adakulamulani kudzera mwa Mose, kuyambira tsiku limene Chauta adapereka lamulo mpaka m'tsogolo mwake pa mibadwo yanu yonse.
24
Ngati cholakwacho chidachitika mosadziŵa, mpingo womwe osazindikira, pamenepo mpingo wonsewo upereke mwanawang'ombe wamphongo kuti akhale nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Apereke pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi chakumwa, potsata zimene ndidakulamulani. Aperekenso tonde kuti akhale nsembe yopepesera machimo.
25
Wansembe achite mwambo wopepesera machimo a mpingo wonse wa Aisraele ndipo anthuwo adzakhululukidwa, chifukwa choti adalakwa mosadziŵa. Tsono atabwera ndi zopereka zao ngati nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta, ndiponso ngati nsembe yopepesera machimo, yopereka kwa Chauta, kuti azimpepesa pa cholakwa chao chija,
26
mpingo wonse wa Aisraele udzakhululukidwa pamodzi ndi mlendo yemwe amene akhala pakati pao, poti anthu onse adalakwa mosadziŵa.
27
“Ngati munthu mmodzi alakwa mosadziŵa, apereke mbuzi yaikazi ya chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo.
28
Motero wansembe amchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Chauta munthu wolakwa mosadziŵayo. Akalakwa choncho mosadziŵa, amchitire mwambo wopepesera machimo, ndipo adzakhululukidwa.
29
Mukhale ndi lamulo limodzi pa munthu aliyense amene alakwa mosadziŵa, pa mbadwa iliyonse pakati pa Aisraele ndi pa mlendo amene akhala pakati pao.
30
Koma munthu amene achimwa dala, ngakhale akhale mbadwa kapena mlendo, wanyoza Chauta, ndipo munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.
31
Popeza kuti wanyoza mau a Chauta ndipo waphwanya lamulo la Chauta, amchotseretu munthu ameneyo, tchimo lake lidzamkangamira.”
32
Pamene Aisraele anali m'chipululu muja, adapeza munthu akutola nkhuni pa tsiku la Sabata.
33
Amene adapeza munthuyo akutola nkhuni, adabwera naye kwa Mose ndi Aroni ndi kwa mpingo wonse.
34
Iwo adamponya m'ndende chifukwa choti sankadziŵa bwino zoti amchite.
35
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Munthuyo aphedwe. Mpingo wonse umponye miyala kunja kwa mahema.”
36
Pomwepo mpingo udamtulutsira kunja kwa mahema munthuyo ndi kumupha pomponya miyala, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
37
Chauta adauza Mose kuti,
38
“Lankhula ndi Aisraele, ndipo uŵauze kuti pa mibadwo yao yonse azisokerera mphonje pa ngodya za zovala, ndipo pa mphonje ya ngodya iliyonse asokerepo chingwe chobiriŵira.
39
Mphonje imeneyo muzidzaiyang'ana ndi kumakumbukira malamulo onse a Chauta, kuti muziŵamvera, ndipo musamatsatenso zilakolako zokhota za mtima wanu kapena za maso anu zimene munkazitsata.
40
Choncho mudzakumbukira ndi kugwiritsa ntchito malamulo anga onse, mudzakhala oyera mtima pamaso pa Mulungu wanu.
41
Ine ndine Chauta amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito, kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Chauta.”
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
Recommended Reading
Commentary
Numbers Commentaries
→
Devotional
Numbers Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→