bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 14
Numbers 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 15 →
1
Pamenepo mpingo wonse udafuula kwambiri, ndipo anthu adalira usiku umenewo.
2
Aisraele onse adayamba kuŵiringulira Mose ndi Aroni. Mpingo wonse udaŵauza kuti, “Kukadakhala bwino tikadangofera ku Ejipito, kapena m'chipululu mommuno.
3
Chifukwa chiyani Chauta akutiloŵetsa m'dziko limenelo kuti tikaphedwe pa nkhondo? Akazi athu adzatengedwa ku ukapolo pamodzi ndi ana athu. Kodi sikukadakhala bwino koposa kuti tibwerere ku Ejipito?”
4
Ndipo adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tisankhe mtsogoleri kuti tibwerere ku Ejipito.”
5
Mose ndi Aroni adadziponya pansi pamaso pa mpingo wonse wa Aisraele.
6
Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, amene adaali m'gulu la anthu okazonda dziko lija, adang'amba zovala zao.
7
Ndipo adauza mpingo wonse wa Aisraele uja kuti, “Dziko limene tidakalizondalo ndi labwino kwambiri.
8
Ngati Chauta amatikonda, adzatiloŵetsa m'dziko lamwanaalirenjilo ndi kutipatsa kuti likhale lathu.
9
Koma musagalukire Chauta. Musaope anthu a m'dzikolo chifukwa tidzaŵaononga. Iwowo alibe oŵatchinjiriza, koma ife Chauta ali nafe, musaŵaope.”
10
Koma mpingo wonse udaati uŵaponye miyala. Pomwepo ulemerero wa Chauta udaonekera Aisraele onse m'chihema chamsonkhano.
11
Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi anthu ameneŵa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzaleka liti kusandikhulupirira, ngakhale aone zizindikiro zimene ndachita pakati pao?
12
Ndidzaŵapha ndi mliri ndi kuŵalanda choloŵa chao, ndipo iwe ndidzakusandutsa mtundu waukulu ndi wamphamvu kupambana iwoŵa.”
13
Koma Mose adayankha Chauta kuti, “Zimenezitu Aejipito adzazimva, pakuti ndinu amene mudaŵatulutsa anthu ameneŵa m'dziko la Ejipito.
14
Tsono Aejipito azidzasimbira anthu a m'dziko muno. Iwo amva kale kuti Inu Chauta muli pakati pa anthu ameneŵa. Inu Chauta mumaŵaonekera maso ndi maso, ndipo mtambo wanu umaŵaphimba. Masana mumaŵatsogolera ndi mtambo, usiku mumaŵatsogolera ndi moto.
15
Tsopano mukaŵapha onse anthu ameneŵa, mitundu ina imene yamva mbiri yanu idzati,
16
‘Chauta waŵaphera m'chipululu anthuŵa, chifukwa choti sadathe kuŵaloŵetsa m'dziko limene adalumbira kuti adzaŵapatsa kuti likhale lao.’
17
Tsono ndikukupemphani, Chauta muwonetse kuti mphamvu zanu nzazikulu monga mudalonjezera kuti,
18
‘Chauta ndi wosakwiya msanga, ndi wodzaza ndi chifundo chosasinthika, ndi wokhululukira ochimwa ndi opalamula. Koma sadzaleka kulanga ochimwa, amalanga ana a mbadwo wachitatu ndi wachinai chifukwa cha kuchimwa kwa makolo ao.’
19
Ndikukupemphani kuti muŵakhululukire kuchimwa kwao anthu ameneŵa kaamba ka chifundo chanu chachikulu ndi chosasinthika, ndiponso chifukwa mwakhala mukuŵakhululukira anthu ameneŵa kuyambira ku Ejipito mpaka tsopano lino.”
20
Chauta adati, “Ndaŵakhululukira chifukwa cha mau ako.
21
Koma ndikulumbira kuti pali Ine ndemwe ndiponso malinga nkuti dziko lonse lapansi ndi lodzaza ndi ulemerero wa Chauta,
22
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaloŵe m'dzikolo. Anthu ameneŵa adaona ulemerero wanga ndi zizindikiro zanga zimene ndidachita ku Ejipito ndi m'chipululu muno, komabe adandipenekera kakhumi konse osamvera mau anga.
23
Palibe amene adzaone dziko limene ndidalonjeza makolo ao molumbira kuti ndidzaŵapatsa. Mwa amene adandikana palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaliwone dzikolo.
24
Koma Kalebe mtumiki wanga, chifukwa ali ndi mtima wosiyana ndi ena, ndipo wanditsata ndi mtima wonse, ndidzamloŵetsa m'dziko limene adapitamolo, ndipo zidzukulu zake zidzalandira dzikolo kuti likhale lao.
25
Tsono popeza kuti Aamaleke ndi Akanani amakhala m'zigwa, maŵa mubwerere, muyambepo ulendo wopita ku chipululu, mudzere ku Nyanja Yofiira.”
26
Chauta adafunsa Mose ndi Aroni kuti,
27
“Kodi anthu oipa chotereŵa, adzaleka liti kundiŵiringulira? Ndamva maŵiringulo ao amene akundichitira.
28
Uŵauze kuti, Chauta akunena kuti, ‘Zimene mwanena, Ine ndamva, ndipo ndi zimene ndidzakuchitani.
29
Mitembo yanu idzakhala ili mbwee m'chipululu muno. Anthu onse, kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, amene adandiŵiringulira,
30
palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaloŵe m'dziko limene ndidalumbira kuti mudzaloŵamo, kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.
31
Ana anu amene munkati adzagwidwa mu ukapolo, ndidzaŵaloŵetsa m'dzikomo, ndipo adzalidziŵa dziko limene inu mukunyozalo.
32
Koma enanu, mitembo yanu idzakhala ili mbwee m'chipululu mommuno.
33
Ana anu adzakhala abusa m'chipululu akungoyendayenda zaka makumi anai, ndipo adzasauka chifukwa cha kusakhulupirika kwanu, mpaka inuyo mutatha ndi kufa m'chipululu.
34
Padzapita zaka makumi anai mukulangidwa chifukwa cha zolakwa zanu, kuŵerenga chaka chimodzi pa tsiku lililonse la masiku makumi anai aja amene munkazonda dziko. Mudzadziŵa kuwopsa kwake kwa kukangana ndi Ine.’
35
Ine Chauta ndanena. Ndithudi, ndidzachitadi zimenezi kwa anthu onse oipaŵa, amene agwirizana kuti andiwukire. M'chipululu mommuno ndimo m'mene athere, ndipo afera mommuno.”
36
Anthu amene Mose adaŵatuma kuti akazonde dziko aja atabwerako, ena adayamba kuutsa mitima ya anthu kuti aukire Mose pakuŵauza zoipa za dzikolo.
37
Anthu onsewo amene ankasimba zoipa za dzikolo, adafa ndi mliri pamaso pa Chauta.
38
Koma mwa anthu amene adapita kukazonda dziko aja, Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune ndiwo adatsala amoyo.
39
Mose adaŵafotokozera Aisraele mau onseŵa, ndipo anthu adalira kwambiri.
40
Adalaŵirira m'mamaŵa, ndipo adakwera cha ku dziko lamapiri, nati “Ife pano takonzeka kukwera mpaka kukafika ku malo amene Chauta adatilonjeza. Ndithu tachimwadi.”
41
Koma Mose adati, “Chifukwa chiyani mukunyoza lamulo la Chauta, poti zimenezo sizidzatheka?
42
Musapite, kuti mungaphedwe pamaso pa adani anu, pakuti Chauta sali nanu.
43
Kumeneko Aamaleke ndi Akanani ali m'tsogolo mwanu, ndipo mudzaphedwa pa khondo. Chauta sadzakhala nanu, chifukwa choti mwaleka kumtsata.”
44
Koma iwo adapitabe osasamala, nakwera ku dziko lamapiri, ngakhale kuti sadatsakane ndi Bokosi lachipangano cha Chauta, kapena ndi Mose, pochoka pamahemapo.
45
Tsono Aamaleke ndi Akanani, amene ankakhala m'dziko lamapirilo, adatsika ndipo adaŵagonjetsa, ndi kuŵapirikitsa mpaka ku Horoma.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36