bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 16
Numbers 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 17 →
1
Kora mwana wa Izara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, ndiponso Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, pamodzi ndi Oni mwana wa Peleti, adzukulu a Rubeni,
2
adakopa anthu. Adaukira Mose, iwowo pamodzi ndi atsogoleri a Aisraele 250, osankhidwa ndi anthu pa msonkhano, anthu otchuka.
3
Onsewo adasonkhana pamodzi ndipo adaukira Mose ndi Aroni, naŵauza kuti, “Inu mwankitsa nazo. Mpingo wonse ndi woyera, munthu aliyense mumpingomo ndi wa Chauta, ndipo Chauta ali pakati pathu. Chifukwa chiyani tsono mukudziyesa opambana pa msonkhano wa Chauta?”
4
Mose atamva zimenezi, adagwada napemphera,
5
kenaka adauza Kora pamodzi ndi gulu lake lonse kuti, “Maŵa m'maŵa, Chauta atiwonetse amene ali wakewake, ndiponso amene ali woyera mtima, ndipo adzamuuza kuti abwere pafupi naye. Munthu amene Mulungu amsankheyo, adzamufikitsa pafupi.
6
Tsono iwe Kora, pamodzi ndi gulu lako lonse, muchite izi: mutenge zofukizira lubani,
7
muikemo moto, ndipo muthiremo lubani maŵa pamaso pa Chauta. Munthu amene Chauta amsankheyo, ndiye woyera wake. Inu Alevi, ndinu amene mwamkitsa nazo.”
8
Mose adauza Kora kuti, “Imvani tsono inu Alevi.
9
Kodi simukukhutira nazo zakuti Mulungu wa Israele adakupatulani mu mpingo wa Israele, kuti mubwere pafupi ndi Mulungu kudzatumikira m'Chihema chake, ndipo kuti muime pamaso pa msonkhano ndi kuŵatumikira anthuwo?
10
Ndiponso kodi Mulungu adakulolani kuti mubwere pafupi ndi Iye, inu pamodzi ndi abale anu Alevi, amene ali nanu? Kodi mukukhumbiranso ndi unsembe womwe?
11
Tsono kutereku nkukangana ndi Chauta, pamene iwe ndi gulu lako mwasonkhana chotere. Kodi Aroni ndiye yani kuti muzimuukira?”
12
Apo Mose adatuma munthu kukaitana Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu. Ndipo iwo adati, “Ife sitibwera kumeneko.
13
Kodi zikukucheperani kuti mudatitulutsa ku dziko lamwanaalirenji ku Ejipito, kuti tifere m'chipululu muno? Kodi mukufunanso kuti mukhale mfumu yathu yotilamula?
14
Kuwonjezera apo, simudatiloŵetse m'dziko lamwanaalirenji, ndipo simudatipatse polima kapena minda yamphesa, kuti ikhale choloŵa chathu. Kodi mukufuna kutigwira m'maso? Ife sitibwera kumeneko.”
15
Apo Mose adapsa mtima kwambiri, ndipo adauza Chauta kuti, “Musalandire nsembe za anthu ameneŵa. Sindidaŵalande ndi bulu mmodzi yemwe, ndipo sindidalakwire ndi mmodzi yemwe mwa iwo.”
16
Tsono Mose adauza Kora kuti. “Maŵa iwe pamodzi ndi anthu a gulu lako 250, mubwere ku hema lamsonkhano, iweyo ndi anthu akowo ndi Aroni.
17
Aliyense mwa inu atenge chofukizira lubani, athiremo lubani. Nonsenu mubwere ku chihemacho, aliyense ndi chofukizira chake. Zofukizirazo zikhale 250, ndipo iweyo ndi Aroni mutenge aliyense chakechake.”
18
Choncho munthu aliyense adatenga chofukizira lubani, naikamo moto, ndi kuthiramo lubani, ndipo adakaimirira pa chipata cha chihema chamsonkhano, pamodzi ndi Mose ndi Aroni.
19
Kora adasonkhanitsa mpingo wonse pa chipata cha chihema chamsonkhano moyang'anana ndi Mose ndi Aroni. Ndipo ulemerero wa Chauta udaonekera mpingo wonsewo.
20
Ndipo Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,
21
“Chokani pakati pa mpingowu kuti ndiwononge onse nthaŵi imodzi.”
22
Apo iwo adadziponya pansi, nati, “Inu Mulungu, Chauta mwini moyo wa anthu onse, kodi mukwiyira mpingo wonse chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi?”
23
Chauta adauza Mose kuti,
24
“Uza mpingo kuti achoke pafupi ndi mahema a Kora, Datani ndi Abiramu.”
25
Tsono Mose adapita kwa Datani ndi Abiramu, ndipo akuluakulu a Aisraele adamtsatira.
26
Mose adauza mpingowo kuti, “Ndapota nanu, chokani pakati pa mahema a anthu oipaŵa, ndipo musakhudze chinthu chao chilichonse, kuti angakuphereni kumodzi chifukwa cha zoipa zao.”
27
Choncho anthuwo adachokapo pafupi ndi mahema a Kora, Datani ndi Abiramu. Pamenepo Datani ndi Abiramu adatuluka naima pakhomo pa mahema ao pamodzi ndi akazi ao, ana ao ndi makanda ao.
28
Tsono Mose adati, “Pano muzindikira kuti ntchito zonse ndikuchitazi, adandituma ndi Chauta, si za m'mutu mwanga ai.
29
Anthu aŵa akafa monga m'mene amafera anthu onse, Mulungu osaŵalanga, ndiye kuti Chauta sadanditume ai.
30
Koma Chauta akachita chinthu china chachilendo, nthaka ikayasama ndi kuŵameza iwowo pamodzi ndi zinthu zao zonse, natsikira kumanda ali moyo, mpamene mudziŵe kuti anthu ameneŵa anyoza Chauta.”
31
Mose atangomaliza kulankhula mau ameneŵa, nthaka idang'ambika pamene padaali iwopo.
32
Nthakayo idayasama ndi kuŵameza onsewo pamodzi ndi mabanja ao ndiponso anthu onse a gulu la Kora ndi zinthu zao zonse.
33
Motero iwowo adaloŵa m'manda ali moyo, pamodzi ndi zinthu zao zonse. Nthaka idaŵatsekera pansi, motero adazimirira pakati pa msonkhano wonse.
34
Pomwepo Aisraele onse amene anali pafupi adathaŵa, atamva anthuwo akulira. Ankati, “Tiyeni tithaŵe kuti nthakayi ingatimeze nafenso.”
35
Tsono padayaka moto wochokera kwa Chauta ndipo udapsereza anthu 250 amene ankafukiza lubani aja.
36
Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti,
37
“Uza Eleazara, mwana wa wansembe Aroni, kuti achotse zofukizira lubani zija m'motomo, ndipo motowo aumwazire kutali.
38
Zofukizira za anthu amene aphedwa chifukwa cha kuchimwa kwao nzoyera. Zofukizirazo azisule chophimbira pa guwa, poti azipereka pamaso pa Chauta, nchifukwa chake nzoyera. Motero zidzakhala chizindikiro kwa Aisraele onse.”
39
Choncho wansembe Eleazara adatenga zofukizira zamkuŵa zija zimene adadzapereka anthu amene adapsa ndi moto aja. Adazisula chophimbira pa guwa,
40
kuti zikhale chikumbutso kwa Aisraele, kuti munthu aliyense amene sali wansembe, amene sali mmodzi mwa zidzukulu za Aroni, asayandikire kudzafukiza lubani pamaso pa Chauta, kuti zingamgwere zonga zimene zidagwera Kora ndi gulu lake. Zonse zidachitika monga momwe Chauta adauzira Eleazara kudzera mwa Mose.
41
Koma m'maŵa mwake mpingo wonse wa Aisraele udaŵiringulira Mose ndi Aroni kuti, “Inu mwapha anthu a Chauta.”
42
Pamene mpingo udasonkhana kuti uukire Mose ndi Aroni, anthuwo adatembenuka ndi kuyang'ana ku chihema chamsonkhano. Tsono adangoona mtambo utaphimba chihemacho, ndipo ulemerero wa Chauta udaonekera.
43
Mose ndi Aroni adabwera patsogolo pa chihema chamsonkhano,
44
ndipo Chauta adauza Moseyo kuti,
45
“Choka pakati pa gulu la anthuli, kuti ndiŵaononge onse nthaŵi imodzi.” Aŵiriwo adadziponya pansi.
46
Mose adauza Aroni kuti, “Tenga chofukizira lubani chako, ndipo uikemo moto wa pa guwa ndi kuthiramo lubani. Upite nacho msanga kumene kuli gulu la anthuko, ndipo uŵachitire mwambo wopepesera machimo ao. Inde, mkwiyo wa Chauta watsika, ndipo mliri wayamba kale.”
47
Choncho Aroni adatenga chofukizira, nathamangira pakati penipeni pa msonkhano. Ndipo adangoona mliri utayamba kale pa anthuwo. Tsono adathira lubani, nachita mwambo wopepesera machimo a anthuwo.
48
Aroni adakaima pakati pa anthu akufa ndi amoyo aja, ndipo mliriwo udaleka.
49
Komabe amene adafa ndi mliriwo anali 14,700, kuwonjeza pa anthu aja amene adafa pa mlandu wa Kora.
50
Pambuyo pake Aroni adabwerera kwa Mose ku chipata cha chihema chamsonkhano, mliriwo utaleka.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36