bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 31
Numbers 31
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 32 →
1
Chauta adauza Mose kuti,
2
“Ulipsire Amidiyani chifukwa cha zimene adachitira Aisraele, tsono pambuyo pake udzafa.”
3
Mose adauza Aisraele kuti, “Amuna ena pakati panupa mutenge zida zankhondo, kuti mukamenyane ndi Amidiyani, kuti Chauta aŵalipsire.
4
Mutumize ku nkhondo anthu chikwi chimodzi pa fuko lililonse la Israele.”
5
Choncho pa anthu a Aisraele ambirimbiri aja, Mose adatumiza anthu chikwi chimodzi pa fuko lililonse, ndipo onse anali 12,000 pamodzi.
6
Mose adaŵatumiza ku nkhondo anthuwo, chikwi chimodzi pa fuko lililonse, pamodzi ndi Finehasi mwana wa wansembe Eleazara, iyeyu atanyamula zipangizo za ku malo opatulika ndi malipenga ochenjeza m'manja mwake.
7
Aisraelewo adamenyana nkhondo ndi Amidiyani, monga momwe Chauta adaalamulira Mose, ndipo adapha amuna onse.
8
Adapha mafumu a ku Midiyani pamodzi ndi anthu ao omwe. Mafumuwo anali Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu asanu a ku Midiyani. Adaphanso ndi lupanga Balamu mwana wa Beori.
9
Ndipo adagwira akazi a ku Midiyani ukapolo, pamodzi ndi ana ao. Adalandanso ng'ombe zao, nkhosa zao, ndi chuma chao chonse.
10
Adatentha mizinda yonse imene iwo ankakhalamo, ndi zithando zao zonse,
11
natenga zonse zimene adalanda kunkhondoko, anthu pamodzi ndi nyama zomwe.
12
Tsono adabwera nawo akapolowo, pamodzi ndi zonse zimene adalandazo, kwa Mose, kwa wansembe Eleazara ndi kwa mpingo wonse wa Aisraele, ku zithando za ku zigwa za Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani ku Yeriko.
13
Mose ndi wansembe Eleazara, pamodzi ndi atsogoleri a mpingo, adakaŵachingamira kunja kwa zithando.
14
Ndipo Mose adakwiyira akulu ankhondowo, atsogoleri olamulira ankhondo zikwi ndiponso atsogoleri olamulira ankhondo mazana, amene ankachokera ku nkhondo.
15
Mose adaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwaŵasiya amoyo akazi onse?
16
Paja akazi ameneŵa adatsata uphungu wa Balamu, nasokeretsa Aisraele kuti asachitenso zokhulupirika pamaso pa Chauta ku Peori kuja, kotero kuti mliri udagwera mpingo wa Chauta.
17
Nchifukwa chake tsono iphani mwana wamwamuna aliyense, ndi mkazi aliyense amene adadziŵapo ndi mwamuna.
18
Koma atsikana amene sadagone ndi mwamuna, muŵasunge akhale anu.
19
Tsono aliyense mwa inu amene wapha munthu, kapena amene wakhudza mtembo, akhale kunja kwa mahema masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, mudziyeretse inuyo pamodzi ndi akapolo anu.
20
Muyeretse chovala chilichonse, chinthu chilichonse chachikopa, chinthu chilichonse chopangidwa ndi ubweya wambuzi, ndi chinthu chilichonse chopangidwa ndi mtengo.”
21
Tsono wansembe Eleazara adauza ankhondo amene adaapita ku nkhondowo kuti, “Lamulo limene Chauta walamula Mose ndi ili:
22
Izi zokha, golide, siliva, mkuŵa, chitsulo, chiwaya ndi mtovu,
23
zonse zimene sizingathe kupsa ndi moto, muziike pa moto, ndipo zidzayeretsedwa. Komabe ziyeretsedwenso ndi madzi oyeretsera, ndipo chilichonse chimene chingathe kupsa ndi moto, muchiviike m'madzi omwewo.
24
Muchape zovala zanu pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, ndipo mudzayeretsedwa. Pambuyo pake muloŵe ku mahema.”
25
Chauta adauza Mose kuti,
26
“Iwe, ndi wansembe Eleazara, pamodzi ndi atsogoleri a mabanja a mpingo, muŵerenge zofunkha zimene adalanda pa nkhondo, anthu pamodzi ndi nyama zomwe.
27
Ndipo mugaŵe zofunkhazo magawo aŵiri, lina la ankhondo amene adaapita ku nkhondo, lina la mpingo wonse.
28
Pa gawo la ankhondowo, mutengeko gawo la Chauta, pa zofunkha mazana asanu aliwonse mutengeko chimodzi, pa akapolo, pa ng'ombe, pa abulu ndi pa nkhosa.
29
Mutenge zimenezo pa gawo la ankhondowo ndipo mupatse wansembe Eleazara, kuti zikhale zopereka zanu kwa Chauta.
30
Ndipo pa gawo la Aisraele, mtengeko chofunkha chimodzi pa zofunkha makumi asanu aliwonse, pa anthu, ng'ombe, abulu, nkhosa ndi pa nyama zonse zoŵeta, ndipo mupatse Alevi amene amayang'anira Chihema cha Chauta.”
31
Tsono Mose ndi wansembe Eleazara adachitadi zomwe Chauta adalamula Mose.
32
Zofunkha zotsala zimene ankhondowo adalanda zinali izi: nkhosa 675,000,
33
ng'ombe 72,000,
34
abulu 61,000,
35
ndi atsikana amene sadagonepo ndi amuna 32,000 pamodzi.
36
Gawo la ankhondo amene adapita ku nkhondo linali nkhosa 337,500,
37
ndipo gawo la Chauta linali nkhosa 675.
38
Ng'ombe zinalipo 36,000, ndipo 72 zinali gawo la Chauta.
39
Abulu analipo 30,500, ndipo 61 anali gawo la Chauta.
40
Anthu analipo 16,000, ndipo 32 anali gawo la Chauta.
41
Mose adapereka kwa wansembe Eleazara gawo limene linali loyenera kulipereka kwa Chauta, monga momwe Chauta adaalamulira Moseyo.
42
Mose adagaŵa zofunkha napatsa Aisraele theka limodzi, kuchotsa pa zofunkha zonse zobwera ndi ankhondo aja.
43
Tsono gawo la Aisraele linali ili: nkhosa 337,500,
44
ng'ombe 36,000,
45
abulu 30,500,
46
ndiponso anthu 16,000.
47
Pa gawo la Aisraelelo, Mose adatengako chofunkha chimodzi pa zofunkha makumi asanu aliwonse, anthu ndi nyama, ndipo adapatsa Alevi amene ankayang'anira Chihema cha Chauta, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
48
Pamenepo akulu a nkhondo amene ankayang'anira ankhondo onse, ndiye kuti atsogoleri olamulira ankhondo zikwi, ndi atsogoleri olamulira ankhondo mazana, adabwera kwa Mose.
49
Adauza Moseyo kuti, “Atumiki anufe taŵerenga ankhondo amene tikuŵalamulira, ndipo palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene akusoŵa.
50
Ndipo ife tabwera ndi zopereka kwa Chauta zimene munthu aliyense adapeza, monga golide, zibangiri, zikono, mphete zosindikizira, ndolo ndi mikanda, kuti achitire mwambo wopepesera machimo athu pamaso pa Chauta.”
51
Apo Mose ndi wansembe Eleazara adalandira golide kwa atsogoleriwo, pamodzi ndi zinthu zonse zosula.
52
Golide yense amene iwo adapereka kwa Chauta kuchokera kwa atsogoleri a ankhondo zikwi, ndi kwa atsogoleri a ankhondo mazana, anali wolemera makilogaramu 200 yense pamodzi.
53
(Ankhondo aja anali atatenga zofunkha, aliyense zakezake.)
54
Tsono Mose ndi wansembe Eleazara adalandira golideyo kwa atsogoleri a ankhondo zikwi ndi a ankhondo mazana, namuika m'chihema chamsonkhano, kuti akhale chikumbutso cha Aisraele pamaso pa Chauta.
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 32 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36