bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 30
Numbers 30
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 31 →
1
Mose adauza atsogoleri a mafuko a Aisraele kuti, Chauta walamula kuti,
2
“Pamene munthu wamwamuna alumbira kwa Chauta kapena alonjeza kuti adzachitadi zimene walumbira, asaphwanye lonjezo lakelo. Achite molingana ndi zimene adalumbira.
3
Mkazi akakhala mtsikana, nakhalabe m'nyumba ya bambo wake, ndipo alumbira kwa Chauta kuti adzachitadi zina zake zimene walumbira,
4
tsono bambo wake nkumva za kulumbira kwakeko ndi za malonjezo amene walumbira kuti adzachitadi, koma bambo wakeyo osalankhula kanthu, mwanayo achitedi zimene adalumbirazo. Ayenera kuchitadi zonse zimene walonjezazo.
5
Koma bambo wake akamkaniza mwanayo pa tsiku lomwe wamva zimenezo, palibe lamulo lomkakamiza mwanayo kuti achite zimene adalumbirazo ndi zimene adalonjezazo. Chauta adzamkhululukira mwanayo chifukwa choti bambo wake adamkaniza.
6
Ngati mkazi alonjeza kapena alumbira mosaganiza bwino kuti adzachitadi kanthu kena, ndipo pambuyo pake akwatiwa,
7
tsono mwamuna wake nkumva, koma osamuuza kanthu mkaziyo pa tsiku lomwe wamvalo, mkaziyo achitedi zimene walumbirazo, achite ndithu zimene walonjezazo.
8
Koma ngati pa tsiku limene mwamunayo wamva zimenezo, amkaniza, pamenepo ammasula mkaziyo kwa zimene adalumbira ndi kwa zimene adalankhula mosaganiza bwino, ndipo Chauta adzamkhululukira.
9
“Mkazi wamasiye kapena wosudzulidwa akalumbira kapena kulonjeza kuti adzachita kanthu kalikonse, ayenera kukachitadi.
10
“Mkazi wokwatiwa akalonjeza nalumbira kuti adzachitadi zimene walonjeza,
11
tsono mwamuna wake nkumva, koma osamuuza kanthu mkaziyo ndiponso osamkaniza, ayenera kuchitadi zonse zimene adalumbira ndi zonse zimene adalonjeza.
12
Koma pa tsiku limene mwamuna wake wamva zimenezo, akamletsa mkaziyo kuti asachite zimene adalumbirazo, palibe lamulo lomkakamiza mkaziyo kuchita zimene adalumbira kapenanso zimene adalonjeza. Mwamuna wake waletsa, ndipo Chauta adzamkhululukira mkaziyo.
13
Mwamuna wake ali ndi mphamvu za kuvomereza kapena kukana zimene mkaziyo adalumbira kapena zimene adalonjeza zokhudza za kudzilanga.
14
Koma ngati m'maŵa mwake ndi masiku otsatirawo mwamuna wake samkaniza, atamva zimenezo, mkaziyo achitedi zonse zimene adalumbira, kapena zimene adalonjeza. Mwamunayo wavomereza zimenezo, chifukwa choti sadamuuze kanthu mkaziyo pa tsiku limene adamva.
15
Koma mwamunayo akamkaniza patapita kanthaŵi atazimva kale, iyeyo ndiye wochimwa pamalo pa mkaziyo.”
16
Ameneŵa ndiwo malamulo amene Chauta adalamula Mose za mwamuna ndi mkazi wake, ndiponso za bambo ndi mwana wake wamkazi amene akadali mtsikana wokhalabe m'nyumba ya bambo wake.
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 31 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36