bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 7
Numbers 7
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 8 →
1
Pa tsiku limene Mose adamaliza kumangitsa chihema cha Mulungu, nachidzoza ndi kuchipatula, pamodzi ndi zipangizo zake, adadzozanso guwa lansembe ndi kulipatula pamodzi ndi ziŵiya zake zomwe.
2
Tsiku lomwelo akulu a Aisraele, ndiye kuti atsogoleri a mabanja ndi a mafuko amene ankayang'anira kuŵerenga kuja,
3
adatenga zopereka zao, ndipo adabwera nazo pamaso pa Chauta. Adapereka ngolo zophimbidwa zisanu ndi imodzi ndiponso ng'ombe khumi ndi ziŵiri: atsogoleri aŵiri ngolo imodzi, ndipo mtsogoleri aliyense ng'ombe imodzi. Zimenezo adafika nazo ku chihema cha Chauta.
4
Tsono Chauta adauza Mose kuti,
5
“Ulandire zimenezi kwa anthuwo kuti zithandize potumikira m'chihema chamsonkhano. Uŵapatse Alevi zimenezo, aliyense zoyenera ntchito yake.”
6
Choncho Mose adatenga ngolo ndi ng'ombe zija nazipereka kwa Alevi.
7
Ana a Geresoni adaŵapatsa ngolo ziŵiri ndi ng'ombe zinai potsata ntchito yao.
8
Ana a Merari adaŵapatsa ngolo zinai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu potsata ntchito yao, imene woyang'anira wake anali Itamara, mwana wa wansembe Aroni.
9
Koma ana a Kohati sadaŵapatse kanthu, chifukwa iwowo anali ndi ntchito yosamala zinthu zoyera zimene ankanyamulira pa phewa.
10
Pambuyo pake atsogoleri adabwera ndi zopereka zopatulira guwa pa tsiku lomwe adalidzozalo. Ndipo adafika nazo zopereka zao patsogolo pa guwalo.
11
Apo Chauta adauza Mose kuti, “Atsogoleriwo azibwera ndi zopereka zao zopatulira guwa, mtsogoleri mmodzi pa tsiku.”
12
Nasoni mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda, ndiye adapereka zopereka zake pa tsiku loyamba.
13
Adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wolemera magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, zoperekera za zakudya.
14
Adaperekanso kambale kamodzi kagolide kolemera magaramu 110, kodzaza ndi lubani.
15
Adaperekanso mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
16
Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
17
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali izi: ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Nasoni mwana wa Aminadabu.
18
Netanele mwana wa Zuwara, mtsogoleri wa fuko la Isakara, adapereka zopereka zake pa tsiku lachiŵiri.
19
Zopereka zake zinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, zoperekera za zakudya.
20
Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzadza ndi lubani,
21
mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
22
Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
23
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zisanu zamphongo, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Netanele mwana wa Zuwara.
24
Tsiku lachitatu linali la Eliyabu mwana wa Heloni mtsogoleri wa Azebuloni.
25
Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, zoperekera za zakudya.
26
Adaperekanso kambale kamodzi kagolide kolemera magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
27
mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
28
Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
29
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Eliyabu mwana wa Heloni.
30
Tsiku lachinai linali la Elizuri mwana wa Sedeuri, mtsogoleri wa Arubeni.
31
Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wolemera magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ndi zopereka za zakudya.
32
Adaperekanso kambale kamodzi kagolide kolemera magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
33
mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
34
Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
35
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa amphongo asanu a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Elizuri mwana wa Sedeuri.
36
Tsiku lachisanu linali la Selumiele mwana wa Zurishadai, mtsogoleri wa Asimeoni.
37
Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
38
Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
39
mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
40
Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
41
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Selumiele mwana a Zurishadai.
42
Tsiku lachisanu ndi chimodzi linali la Eliyasafu mwana wa Deuwele mtsogoleri wa Agadi.
43
Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
44
Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
45
mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
46
Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
47
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Eliyasafu mwana wa Deuwele.
48
Tsiku lachisanu ndi chiŵiri linali la Elisama mwana wa Amihudi, mtsogoleri wa Aefuremu.
49
Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
50
Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
51
mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
52
Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
53
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Alisama mwana wa Amihudi.
54
Tsiku lachisanu ndi chitatu linali la Gamaliele mwana wa Pedazuri, mtsogoleri wa Amanase.
55
Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
56
Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
57
mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
58
Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
59
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Gamaliele mwana wa Pedazuri.
60
Tsiku lachisanu ndi chinai linali la Abidani mwana wa Gideoni, mtsogoleri wa Abenjamini.
61
Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
62
Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
63
mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
64
Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
65
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Abidani mwana wa Gideoni.
66
Tsiku lakhumi linali la Ahiyezere mwana wa Amishadai, mtsogoleri wa Adani.
67
Iye adapereka mbale yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
68
Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
69
mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
70
Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
71
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Ahiyezere mwana wa Amishadai.
72
Tsiku la 11 linali la Pagiyele mwana wa Okarani, mtsogoleri wa fuko la Asere.
73
Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
74
Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
75
mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
76
Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
77
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Pagiyele mwana wa Okarani.
78
Tsiku la 12 linali la Ahira mwana wa Enani, mtsogoleri wa Anafutali,
79
Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
80
Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzadza ndi lubani,
81
mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza;
82
tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo.
83
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Ahira mwana wa Enani.
84
Zopereka zopatulira guwa zimene atsogoleri a Aisraele adapereka pa tsiku limene guwalo lidadzozedwa, nazi: adapereka mbale zasiliva khumi ndi ziŵiri, mikhate yasiliva khumi ndi iŵiri, timbale tagolide khumi ndi tiŵiri.
85
Mbale yasiliva iliyonse inkalemera kilogaramu limodzi ndi theka, ndipo mkhate uliwonse unkalemera magaramu 800. Siliva yense wa zipangizo zimenezo, ankalemera makilogaramu 27 ndi theka, potsata muyeso wa ku malo opatulika.
86
Timbale khumi ndi tiŵiri tagolide todzaza ndi lubani timene tinkalemera kalikonse magaramu 110, potsata muyeso wa ku malo opatulika, tonse pamodzi tinkalemera ngati kilogaramu limodzi ndi theka.
87
Nyama zonse zoperekera nsembe zopsereza zinali ng'ombe zamphongo khumi ndi ziŵiri, nkhosa zamphongo khumi ndi ziŵiri, anaankhosa amphongo a chaka chimodzi khumi ndi aŵiri, pamodzi ndi chopereka cha chakudya, ndiponso atonde khumi ndi aŵiri operekera nsembe zopepesera machimo.
88
Ndipo nyama zonse za nsembe zachiyanjano zinali ng'ombe zamphongo 24, nkhosa zamphongo 60, atonde 60, ndi anaankhosa amphongo a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndizo zinali zopereka zopatulira guwa atalidzoza.
89
Tsono Mose ataloŵa m'chihema chamsonkhano kukalankhula ndi Chauta, adamva mau kuchokera pa chivundikiro chokhala pamwamba pa Bokosi laumboni, pakati pa akerubi. Mulungu adalankhula naye.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36