bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 27
Numbers 27
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 28 →
1
Nthaŵi imeneyo kudabwera ana aakazi a Zelofehadi. Iyeyo anali mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, a m'mabanja a Manase mwana wa Yosefe. Ana ake aakaziwo anali aŵa: Mala, Nowa, Hogola, Milika ndi Tiriza.
2
Iwoŵa adakaima pamaso pa Mose, pa wansembe Eleazara, pa atsogoleri, ndiponso pamaso pa mpingo wonse, pakhomo pa chihema chamsonkhano, nati,
3
“Bambo wathu adafera m'chipululu. Iyeyo sanali nao m'gulu la anthu aja amene adasonkhana pamodzi ndi Kora naukira Chauta, iye adafera tchimo lake, koma analibe ana aamuna.
4
Kodi dzina la bambo wathu life chifukwa choti analibe mwana wamwamuna? Mutipatse choloŵa chathu pakati pa abale a bambo wathu.”
5
Mose adapita ndi mlandu umenewu pamaso pa Chauta.
6
Tsono Chauta adauza Mose kuti,
7
“Ana aakazi a Zelofehadiwo akunena zoona. Uŵapatse choloŵa chao pakati pa abale a bambo wao. Uŵapatse choloŵa cha bambo waocho kuti chikhale chao.
8
Ndipo uŵauze Aisraele kuti, ‘Munthu akafa opanda mwana wamwamuna, choloŵa chake chikhale cha mwana wake wamkazi.
9
Akakhala kuti alibe mwana wamkazi, choloŵa chakecho chikhale cha abale ake.
10
Akakhala kuti alibe abale, choloŵa chakecho chikhale cha abale a bambo wake.
11
Bambo wakeyo akakhala wopanda abale, choloŵa chakecho upatse wachibale wake pabanja pakepo, ndipo chidzakhala chake. Ameneŵa akhale malamulo ndi malangizo kwa Aisraele, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.’ ”
12
Chauta adauza Mose kuti, “Ukwere phiri ili la Abarimu, kuti uwone dziko limene ndapatsa Aisraele.
13
Ndipo utaliwona, udzamwalira monga momwe adachitira Aroni mbale wako,
14
chifukwa simudamvere mau anga m'chipululu cha Zini pa nthaŵi imene mpingo udandiwukira ku madzi a Meriba, pamene simudaonetse kuyera kwanga pamaso pao.” (Ameneŵa ndiwo madzi a kasupe wa ku Meriba ku Kadesi, m'chipululu cha Zini.)
15
Mose adapempha Chauta kuti,
16
“Inu Chauta, mwini mpweya wopatsa moyo anthu onse, musankhe munthu kuti aziyang'anira mpingowu.
17
Munthuyo aziŵatsogolera pa nkhondo ndi kuŵalamula, kuti mpingo wanu usamakhale ngati nkhosa zopanda mbusa.”
18
Apo Chauta adauza Mose kuti, “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu amene mzimu wa Mulungu uli mwa iye, ndipo umsanjike manja.
19
Umuimiritse pamaso pa wansembe Eleazara ndi pamaso pa mpingo wonse, tsono umlonge m'malo mwako, iwo akupenya.
20
Umpatseko udindo wako, kuti mpingo wonse wa Aisraele uzimumvera.
21
Tsono adzapite kwa wansembe Eleazara amene adzamdziŵitse zimene Chauta akufuna, pofunsa kwa Urimu ndi Tumimu. Umotu ndi m'mene Iyeyu adzatsogolere ndi kulamula Yoswa ndi mpingo wonse wa Aisraele.”
22
Mose adachitadi monga momwe Chauta adamlamulira. Adamtengadi Yoswa namuimiritsa pamaso pa wansembe Eleazara ndi pamaso pa mpingo wonse.
23
Ndipo adamsanjika manja, nampatsa udindo monga momwe Chauta adamlangizira kudzera mwa Mose.
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36