bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 22
Numbers 22
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 23 →
1
Aisraele adanyamuka ulendo nakamanga mahema ao m'zigwa za Amowabu patsidya pa Yordani ku Yeriko.
2
Balaki mwana wa Zipora adaona zonse zimene Aisraele adachita Aamori.
3
Amowabu adaopa anthuwo kwambiri, chifukwa anali ambirimbiri. Amowabu adachitadi mantha ndi Aisraele.
4
Choncho Amowabuwo adauza akuluakulu a ku Midiyani kuti, “Tsopano khamu limeneli libudula zonse zimene zatizungulira, monga momwe ng'ombe zimabudulira udzu wam'munda.” Pamenepo Balaki mwana wa Zipori amene anali mfumu ya Mowabu nthaŵi imeneyo,
5
adatuma amithenga kwa Balamu, mwana wa Beori, ku Petori, pafupi ndi mtsinje wa Yufurate m'dziko la kwao, kuti akamuitane ndi kumuuza kuti, “Anthu ochokera ku Ejipito adzaza dziko lonse, ndipo akuyang'anana ndi ine.
6
Bwerani tsono muŵatemberere anthu ameneŵa m'malo mwanga, poti ngamphamvu kopambana ine. Mwina mwake ndidzatha kuŵagonjetsa ndi kuŵapirikitsa m'dziko mwanga. Pakuti ndikudziŵa kuti amene inu mumamdalitsa, amadalitsidwa, ndipo amene mumamtemberera, amatembereredwa.”
7
Choncho akalonga a ku Mowabu ndi akalonga a ku Midiyani adanyamuka, atatenga ndalama m'manja zokaombedzera. Tsono adafika kwa Balamu namuuza mau a Balaki.
8
Balamu adaŵauza kuti, “Gonani konkuno lero, ndipo ndikubwezerani mau monga momwe Chauta andiwuzire.” Choncho akalonga a ku Mowabu adagona kwa Balamu.
9
Ndipo Mulungu adadza kwa Balamu namufunsa kuti, “Kodi anthu ali ndi iweŵa ndani?”
10
Balamu adayankha kuti, “Balaki mwana wa Zipora mfumu ya Mowabu, watumiza uthenga kudzandiwuza kuti,
11
‘Anthu amene achokera ku Ejipito, adzaza dziko lonse. Bwerani tsono, muŵatemberere m'malo mwanga, mwina mwake ndidzatha kumenyana nawo nkhondo ndi kuŵapirikitsa.’ ”
12
Apo Mulungu adauza Balamu kuti, “Usapite nao, ndipo usaŵatemberere anthuwo, chifukwa ngodalitsidwa.”
13
Tsono Balamu adadzuka m'maŵa, naŵauza akalonga a Balaki aja kuti, “Bwererani ku dziko lakwanu, pakuti Chauta sadandilole kuti ndipite nanu.”
14
Tsono akalonga a Mowabu aja adanyamuka napita kwa Balaki, ndipo adakamuuza kuti, “Balamu wakana kubwera.”
15
Balaki adatumanso akalonga ochuluka ndi olemekezeka kopambana oyamba aja.
16
Iwo adafika kwa Balamu namuuza kuti, “Balaki mwana wa Zipora akunena kuti, ‘Musalole kuti chinthu chilichonse chikuletseni kubwera kwa ine.
17
Ndithudi, ndidzakuchitirani ulemu waukulu, ndipo chilichonse chimene mundiwuze, ndidzachita. Bwerani, mudzatemberere anthu ameneŵa m'malo mwanga.’ ”
18
Koma Balamu adayankha atumiki a Balakiwo kuti, “Ngakhale Balaki akadati andipatse nyumba yake yodzaza ndi siliva ndi golide, sindikadatha kuchita zosiyana ndi zimene Chauta, Mulungu wanga, wandilamula. Sindikadatha kuchepetsa kapena kuwonjeza.
19
Ndiye inu tsono, gonani konkuno usiku uno, monga adachitira anzanu aja, kuti ndidziŵe ngati pali zina zimene Chauta andiwuze.”
20
Ndipo Mulungu adadza kwa Balamu usiku umenewo namuuza kuti, “Ngati anthuwo abwera kudzakuitana, nyamuka upite nao. Koma ukachite zokhazo zimene ndikakulamule.”
21
Choncho Balamu, atadzuka m'maŵa mwake, adaika chishalo pa bulu wake, ndipo adanyamuka pamodzi ndi akalonga aja.
22
Komabe Mulungu adapsa mtima chifukwa choti Balamuyo adapita. Ndipo mngelo wa Chauta adaimirira mu mseu, kuti amtsekere njira. Pamenepo nkuti atakwera bulu, ndipo ali ndi anyamata ake aŵiri.
23
Bulu uja adaona mngelo wa Chauta ataima mu mseu, atasolola lupanga m'manja mwake. Tsono bulu adasiya mseu nakaloŵa m'munda. Apo Balamu adammenya bulu uja kuti abwerere mu mseu.
24
Pambuyo pake mngelo wa Chauta uja adakaimirira m'kanjira kophaphatiza, kodzera pakati pa minda yamphesa, kokhala ndi khoma pa mbali zonse ziŵiri.
25
Buluyo ataona mngelo wa Chauta, adadzipanikiza ku khoma, nakanikiza phazi la Balamu kukhomako. Pomwepo Balamu adamenya buluyo kachiŵiri.
26
Kenaka mngelo wa Chauta adatsogolako nakaimiriranso pa malo ophaphatiza, opanda koti nkutembenukira kumanja kapena kumanzere.
27
Buluyo ataona mngelo wa Chauta, adagona pansi, Balamu ali pamsana pake. Balamu adapsa mtima kwambiri, namenya buluyo ndi ndodo yake.
28
Pamenepo Chauta adatsekula pakamwa pa buluyo, ndipo adalankhula, nafunsa Balamu kuti, “Kodi ndakuchitani chiyani kuti muzindimenya chotere katatu?”
29
Balamu adauza buluyo kuti, “Chifukwa choti ukuseŵera nane, ndikadakhala ndi lupanga m'manja mwanga, ndikadakupha.”
30
Buluyo adafunsanso Balamu kuti, “Kodi sindine bulu wanu amene mwakhala mukundikwera moyo wanu wonse mpaka lero lino? Kodi zimenezi ndidakuchitiranipo nkale lonse?” Balamu adayankha kuti “Iyai.”
31
Pomwepo Chauta adatsekula maso a Balamu, ndipo adaona mngelo wa Chauta ataimirira m'njira, atasolola lupanga m'manja mwake. Tsono Balamu adazyolika, nadziponya pansi.
32
Mngelo wa Chauta adamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wamenya bulu wako chotere katatu? Ndabwera kudzakutsekera njira, chifukwa ulendo wakowu ukundiipira.
33
Bulu wako anandiwona, ndipo anasiya njira katatu konse atandiwona. Akadapanda kusiya njira atandiwona, ndithu ndikadakuphera pomwepo, koma buluyo ndikadamleka kuti akhale moyo.”
34
Balamu adayankha mngelo wa Chauta uja kuti, “Ndachimwa. Sindinalikudziŵa kuti mukunditsekera njira. Nchifukwa chake tsono, ngati zakuipirani, ndibwerera.”
35
Apo mngelo wa Chauta adauza Balamu kuti, “Pita nawo anthuŵa. Koma ukanene zokhazo zimene ndikakuuze.” Choncho Balamu adapitirira ulendo wake pamodzi ndi akalonga a Balaki aja.
36
Balaki atamva kuti Balamu wafika, adatuluka kukamchingamira ku mzinda wina wokhala pafupi ndi mtsinje wa Arinoni, umene umachita malire a dziko la Mowabu, kumapeto kwake kwenikweni.
37
Ndipo Balaki adafunsa Balamu kuti, “Kodi sindidakutumireni mithenga yodzakuitanani? Chifukwa chiyani simudabwere? Kodi sindingathe kukuchitirani ulemu?”
38
Balamu adayankha Balaki kuti, “Inde, ndabwera, koma kodi ndili ndi mphamvu zoti ndilankhule chinthu chilichonse? Ndiyenera kulankhula zokhazo zimene Mulungu andiwuze.”
39
Tsono Balamu adapita limodzi ndi Balaki, nakafika ku Kiriyati-Huzoti.
40
Kumeneko Balaki adapereka nsembe ya ng'ombe ndi nkhosa, natumizako nyama kwa Balamu ndi kwa akalonga amene anali naye aja.
41
M'maŵa mwake Balaki adatenga Balamu, napita naye ku mapiri a Bamoti-Baala, kumene Balamuyo ankatha kuwona mahema onse a Aisraele mpaka ku mathero ake.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36