bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Numbers 4
Numbers 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 5 →
1
Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,
2
Mwa ana a Levi muŵerenge ana a Kohati, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
3
Muŵerenge amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene angathe kutumikira pa ntchito ya m'chihema chamsonkhano.
4
Ntchito imene ana a Kohati ayenera kugwira m'chihema chamsonkhanomo ndi iyi: azisamala zinthu zopatulika kopambana.
5
Pamene anthu akusamuka pamodzi ndi mahema ao, Aroni pamodzi ndi ana ake aloŵe m'chihema chamsonkhano, amasule nsalu yochinga, ndipo aphimbire Bokosi laumboni.
6
Pambuyo pake ayalepo zikopa zambuzi, ndipo pamwamba pake ayalepo nsalu yobiriŵira, ndi kupisa mphiko m'zigwinjiri zake.
7
Ayale nsalu yobiriŵira pa tebulo la buledi wokhala pamenepo nthaŵi zonse, ndi kuikapo mbale zake, zipande zake zotapira lubani, mabeseni ake, ndi zikho za chopereka cha chakumwa. Aikeponso buledi wokhala pamenepo nthaŵi zonse.
8
Tsono pamwamba pa zimenezo ayalepo nsalu yofiira, ndi kuziphimba zonsezo ndi zikopa zambuzi, ndipo apise mphiko m'zigwinjiri zake.
9
Atenge nsalu yobiriŵira ndi kuphimba choikaponyale, pamodzi ndi nyale zake, mbaniro zake, mbale za phulusa ndi ziŵiya zake zonse za mafuta.
10
Ndipo achiike pamodzi ndi zipangizo zake zonse m'thumba la zikopa zambuzi, ndi kuchiika pa chonyamulira chake.
11
Ayale nsalu yobiriŵira pa guwa lagolide, ndi kuliphimba ndi zikopa zambuzi, ndipo apise mipiko m'zigwinjiri zake.
12
Atenge zipangizo zonse zimene amagwiritsa ntchito m'malo opatulika, aziike m'nsalu yobiriŵira, ndipo aziphimbe ndi zikopa zambuzi, ndi kuziika pa chonyamulira chake.
13
Ataye phulusa lapaguwa, ndipo ayalepo nsalu yofiira.
14
Aikepo ziŵiya zonse zapaguwa zimene amagwiritsira ntchito pamenepo, monga zofukizira lubani, zitsulo zokoŵera nyama, zoolera phulusa ndi mabeseni, kungoti ziŵiya zonse za pa guwalo. Pa zonsezo ayalepo zikopa zambuzi, ndipo apise mipiko m'zigwinjiri zake.
15
Tsono Aroni ndi ana ake, atamaliza kuphimba malo opatulika pamodzi ndi zipangizo zake zonse, pamene anthu akusamuka, ana a Kohati ndiwo abwere kudzanyamula zimenezi, koma asakhudze zinthu zopatulika, kuti angafe. Zimenezi ndizo zinthu za m'chihema chamsonkhano zimene ana a Kohati azinyamula.
16
“Eleazara mwana wa wansembe Aroni, azisamala mafuta a nyale, lubani wonunkhira, chopereka cha chakudya choperekedwa nthaŵi zonse, ndi mafuta odzozera. Aziyang'anira malo opatulika ndi zonse za m'kati mwake, ndiponso chipinda chopatulika kwambiri ndi zipangizo zake.”
17
Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,
18
“Musalole kuti a m'banja la Kohati aonongeke pakati pa Alevi.
19
Kuti Akohatiwo asafe, akayandikira zinthu zopatulika kopambana, Aroni pamodzi ndi ana ake aloŵe, ndipo apatse aliyense mwa Akohatiwo zoti achite ndi zoti anyamule.
20
Koma asaloŵe kukayang'ana zinthu zopatulika mpang'ono pomwe, kuti angafe.”
21
Chauta adauza Mose kuti,
22
“Uŵerengenso ana a Geresoni potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
23
Uŵerenge amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene angathe kutumikira m'chihema chamsonkhano.
24
Zimene mabanja a Geresoni ayenera kuchita, ndiponso zimene ayenera kumanyamula ndi izi:
25
azinyamula nsalu zochinga malo opatulika, chihema chamsonkhano pamodzi ndi chophimbira chake, zikopa zambuzi zophimba pamwamba pake, ndiponso nsalu zochinga pa khomo la chihema chamsonkhano.
26
Azinyamulanso nsalu zochingira bwalo, nsalu yochingira khomo la pa chipata cha bwalo lozungulira malo opatulika ndi guwa, zingwe zake ndi zipangizo zina zonse zofunika. Agwire ntchito zonse zimene aŵapatse.
27
Amene aziyang'anira ntchito zonse za ana a Ageresoni, ndi Aroni pamodzi ndi ana ake. Aziyang'anira zonse zimene ayenera kunyamula, ndi zonse zimene ayenera kuchita. Ndinu amene mudzayenera kuŵafotokozera udindo wa kunyamula zonse zija.
28
Imeneyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Ageresoni m'chihema chamsonkhano, ndipo woyang'anira ntchitoyo akhale Itamara, mwana wa wansembe Aroni.
29
“Uŵerenge ana a Merari potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
30
Uŵerenge amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, aliyense amene angathe kutumikira m'chihema chamsonkhano.
31
Zimene iwo alamulidwa kuti anyamule pa ntchito yao ya m'chihema chamsonkhano nazi: anyamule mitengo ya malo opatulika monga mafulemu ake, mizati yake ndi masinde ake.
32
Anyamulenso mizati yozungulira bwalo, pamodzi ndi zikhomo zake, zingwe zake, kudzanso zipangizo zake zonse, ndi zina zonse zoyendera limodzi ndi zimenezo. Poŵauza zinthu zimene aliyense ayenera kunyamula, uzitchula chinthu chilichonse chimodzichimodzi.
33
Imeneyi ndiyo ntchito ya mabanja a ana a Merari, ndipo ntchito yao yonse ya m'chihema chamsonkhanoyo, aziiyang'anira ndi Itamara, mwana wa wansembe Aroni.”
34
Tsono Mose ndi Aroni, pamodzi ndi atsogoleri a mpingo, adaŵerenga ana a Akohati potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
35
Adaŵaŵerenga anthuwo kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene ankatha kutumikira m'chihema chamsonkhano,
36
ndipo chiŵerengero chao chidakwanira 2,750 potsata mabanja ao.
37
Chimenecho ndicho chinali chiŵerengero cha anthu a m'mabanja a Akohati, onse amene ankatumikira m'chihema chamsonkhano, amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose.
38
Adaŵerenganso ana a Geresoni potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao,
39
kuyambira anthu a zaka makumi atatu mpaka makumi asanu, onse amene ankatha kutumikira m'chihema chamsonkhano.
40
Chiŵerengero chao chidakwanira 2,630 potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
41
Chimenechi ndicho chinali chiŵerengero cha anthu a m'banja a Ageresoni, amene ankatumikira m'chihema chamsonkhano, amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, monga momwe Chauta adaalamulira.
42
Adaŵerenganso ana a Merari potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao,
43
kuyambira anthu a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene ankatha kutumikira m'chihema chamsonkhano.
44
Chiŵerengero chao chidakwanira 3,200 potsata mabanja ao.
45
Ameneŵa ndiwo anthu a m'mabanja a Merari, anthu amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose.
46
Choncho Mose ndi Aroni, pamodzi ndi atsogoleri a Aisraele, adaŵaŵerenga Alevi onsewo potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao.
47
Kuyambira anthu a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene ankatha kugwira ntchito yotumikira ndi yonyamula katundu wa m'chihema chamsonkhano,
48
chiŵerengero chao chidakwanira 8,580.
49
Anthuwo adaŵasankha kuti ena azigwira ntchito yotumikira, ndipo ena azinyamula katundu, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose. Umu ndimo m'mene adaŵaŵerengera anthuwo, monga momwe Chauta adaamlamulira.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36