bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 10
Isaiah 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 11 →
1
Tsoka kwa amene amapanga malamulo opanda chilungamo, ndi kwa alembi amene amalemba zongovutitsa anzao.
2
Pakutero amapotoza malamulo poweruza amphaŵi mosalungama. Amaŵalanda zoŵayenerera anthu anga osauka, amafunkha za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye!
3
Kodi mudzatani pa tsiku lachilango pofika namondwe wochokera kutali? Kodi mudzathaŵira kwa yani kuti akuthandizeni? Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?
4
Kudzatsala nkungozyolika mwamanyazi pakati pa anthu ogwidwa kapena kufa pamodzi ndi ophedwa. Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke chifukwa cha zonsezi, ndipo mkono wake uli chisamulirecho kufuna kuŵalanga.
5
Chauta akuti, “Tsoka kwa mfumu ya ku Asiriya, mkwapulo wa ukali wanga, ndodo ya mkwiyo wanga.
6
Ndikumtuma kwa mtundu wosasamala za Mulungu, ndipo ndikumlamula kuti apite kwa anthu amene ndaŵakwiyira, kuti akafunkhe ndi kukalanda chuma chao chonse, ndi kuŵaponderezera pansi ngati matope am'miseu.”
7
Koma mfumu ya ku Asiriya sikudziŵa zimenezi ndipo mtima wake sukuganiza choncho. Mtima wake uli pa kuwononga ndi kupulula mitundu yochuluka ya anthu.
8
Iye akuti: “Kodi atsogoleri anga onse ankhondo si mafumu okhaokha?
9
Ine ndagonjetsa mizinda iyi: Kalino, Karikemisi, Hamati, Aripadi. Ndagonjetsanso Samariya ndi Damasiko.
10
Ine ndidakantha mafumu a anthu opembedza mafano, amene mafano ao ndi aakulu kupambana a ku Yerusalemu ndi a ku Samariya.
11
Ndiye ndingalephere kuwononga Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake omwe, monga momwe ndidachitira Samariya ndi mafano ake?”
12
Ambuye atamaliza ntchito yao yolanga onse pa phiri la Ziyoni ndiponso ku Yerusalemu, adzalanganso mfumu ya ku Asiriya, chifukwa cha kudzitama kwake ndi kunyada kwake.
13
Pakuti mfumuyo ikuti, “Ndachita zimenezi ndi mphamvu zanga ndiponso ndi nzeru zanga, pakuti kumvetsa nkwanga. Ndachotsa malire a mitundu ya anthu, ndipo ndafunkha chuma chao. Ndaŵatsitsa amene anali pa mipando yaufumu.
14
Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu, monga momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame. Monga momwe anthu amatolera mazira osiyidwa, ndimo m'mene Ine ndidasonkhanitsira dziko lonse lapansi. Ndipo panalibe mbalame ndi imodzi yomwe yoti mapiko phephere-phephere, kapena yoti kukamwa yasa kapena yolira kuti psepsepse.”
15
Koma Chauta akuti: “Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Kodi sowo ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Ndiye kukhala ngati kuti mkwapulo ukuzunguza munthu, kapena ndodo yanyamula munthu!”
16
Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adzatumiza matenda oondetsa kwa ankhondo amphamvu a mfumu ya ku Asiriya. Ndipo mfumuyo kunyada kwake kudzapsa ndi moto wosazimika.
17
Mulungu, Kuŵala kwa Israele, adzakhala ngati moto. Mulungu, Woyera Uja wa Israele, adzakhala ngati malaŵi a moto. Motowo udzaŵatentha ndi kuŵapsereza ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.
18
Adzaononga nkhalango yaikulu ndi nthaka yachonde. Zidzaonongeka m'kati ndi kunja kwake, ndipo zidzakhala ngati munthu wodwala amene akuwonda.
19
Mitengo yotsalira yam'nkhalangomo idzakhala yochepa kwambiri, yoti ndi mwana yemwe nkuiŵerenga.
20
Tsiku limenelo otsalira a ku Israele, opulumuka a m'banja la Yakobe, sadzadaliranso anthu amene adaŵakantha, koma ndithu adzadalira Chauta, Woyera Uja wa Israele.
21
Otsalira adzabwerera, otsalira a m'banja la Yakobe, adzabwereradi kwa Mulungu wamphamvu.
22
Iwe Israele, ngakhale anthu ako achuluke ngati mchenga wakunyanja, otsalira oŵerengeka okha ndiwo adzabwerere. Chiwonongeko chalamulidwa, chidzaonetsa chilungamo chosefukira.
23
Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adzaononga ndithu dziko lonse monga momwe adalamulira.
24
Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, akunena kuti, “Inu anthu anga okhala ku Ziyoni, musaŵaope Aasiriya pamene akukanthani ndi ndodo, nakumenyani ndi zibonga zao, monga m'mene Aejipito ankachitira.
25
Patsala pang'onong'ono kuti uthe mkwiyo wanga pa inu, koma ndidzaŵakwiyira iwonso mpaka kuŵaononga.
26
Ine, Chauta Wamphamvuzonse, ndidzaŵakwapula monga momwe ndidakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu. Ndi ndodo yanga ndidzaŵalanga, monga momwe ndidalangira Aejipito panyanja paja.
27
Tsiku limenelo ndidzakusanjulani katundu wa Aasiriya pa mapewa anu, ndi goli lao m'khosi mwanu, golilo lidzathyoka chifukwa cha kunenepa.”
28
Adani aja akudza afika ku Aiyati. Apyola ku Migironi, aikiza katundu wao ku Mikimasi.
29
Adzera pa mpata uja, nagona ku Geba usiku. Anthu a ku Rama akunjenjemera, a ku Gibea, mzinda wa Saulo, athaŵa.
30
Lirani mokweza, inu anthu a ku Galimu! Tcherani khutu, inu anthu a ku Laisa! Yankhani, inu a ku Anatoti.
31
Anthu a ku Madimena akuthaŵa, a ku Gebimu akubisala.
32
Lero lomwe lino adaniwo adzaima ku Nobu, adzagwedeza mikono yao kuwopseza anthu a ku phiri la Ziyoni, phiri la Yerusalemu.
33
Koma Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adzaŵadula ngati nthambi za mtengo. Akuluakulu adzagwetsedwa, odzikweza adzatsitsidwa.
34
Chauta adzaŵadula monga momwe anthu amadulira ndi nkhwangwa mitengo ya m'kati mwa nkhalango. Iwo adzagwa monga momwe imagwera ngakhale mitengo yaikulu ya ku Lebanoni.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→