bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 2
Isaiah 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 3 →
1
Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya, mwana wa Amozi, adaziwona m'masomphenya.
2
Pa masiku akudzaŵa phiri la Nyumba ya Chauta adzalisandutsa lalitali koposa mapiri ena onse, lidzangoti joo pamwamba pa magomo onse. Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo.
3
Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta.
4
Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko ambiri. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo.
5
Inu zidzukulu za Yakobe, tiyeni tiyende m'kuŵala kwa Chauta.
6
Inu Mulungu, mwakana anthu anu, zidzukulu za Yakobe. Dziko ladzaza ndi anthu amatsenga akuvuma, ladzazanso ndi olosa a ku Filistiya. Anthu anu akuchita nao miyambo yachilendo.
7
Dziko la anthu anu nlodzaza ndi siliva ndi golide, ndipo chuma chao nchosatha. Dziko lao nlodzaza ndi akavalo, ndipo magaleta ao ankhondo ndi osaŵerengeka.
8
Dziko lao nlodzaza ndi mafano. Iwo amapembedza mafano opanga ndi manja ao, oumba ndi zala zao zomwe.
9
Nchifukwa chake adzaŵachepetsa ndi kuŵatsitsa. Inu Chauta, musaŵakhululukire!
10
Loŵani m'matanthwe, bisalani m'maenje kuti muthaŵe mkwiyo wa Chauta, muthaŵenso ulemerero wa ufumu wake.
11
Kudzikuza kwa anthu kudzatha, kudzitama kwa anthu kudzaonongedwa. Chauta yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo.
12
Chauta Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku, pamene adzatsitsa onse onyada ndi odzitama, ndipo adzagonjetsa onse amphamvu.
13
Adzadula mikungudza yonse ya ku Lebanoni, italiitali kopambana ina yonse. Adzalikha mitengo yonse ya thundu ya ku Basani.
14
Adzasalaza mapiri onse aatali. Adzafafaniza magomo onse okwera.
15
Adzagwetsa nsanja zonse zazitali. Adzagumula malinga onse olimba.
16
Adzamiza zombo zonse za ku Tarisisi. Adzaononga mabwato onse okongola.
17
Kudzikuza kwa anthu kudzatha, kudzitama kwao konse kudzaonongedwa. Chauta yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo.
18
Mafano onse adzatheratu.
19
Anthu adzathaŵira m'mapanga am'matanthwe ndi m'maenje am'nthaka, kuthaŵa mkwiyo wa Chauta, kuthaŵanso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzabwere kudzaopsa dziko lapansi.
20
Tsiku limenelo anthu adzatayira mfuko ndi mileme mafano asiliva ndi agolide, amene adaadzipangira kuti azipembedza.
21
Adzathaŵira m'mapanga am'matanthwe ndi m'ming'alu yam'nthaka, kuthaŵa mkwiyo wa Chauta, kuthaŵanso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzabwere kudzaopsa dziko lapansi.
22
Musakhulupirirenso munthu, poti moyo wake sukhalira kutha. Nanga iye nkumuyesanso kanthu ngati!
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66