bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 33
Isaiah 33
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 34 →
1
Tsoka kwa iwe woonongawe, iwe amene sadakuwononge. Tsoka iwe wonyengawe, amene wina aliyense sadakunyenge. Iwe ukadzaleka kuwononga, adzakuwononga, ukadzaleka kunyenga, adzakunyenga.
2
Mutichitire chifundo, Inu Chauta, tikukhulupirira Inu. Mutitchinjirize ndi dzanja lanu lamphamvu tsiku ndi tsiku, ndipo mutipulumutse pa nthaŵi yamavuto.
3
Mukatulutsa liwu lanu longa bingu, mitundu ya anthu imathaŵa. Inu mukadzambatuka, mitundu ya anthu imabalalika.
4
Amakundika zokunkha monga m'mene zimachitira ziwala. Anthu amalumphira zofunkhazo monga m'mene limachitira dzombe.
5
Chauta ndi wolemekezeka kwambiri, pakuti akukhala pamwamba pa zonse. Adzadzaza mzinda wa Ziyoni ndi chilungamo ndi ungwiro.
6
Adzakupatsani mtendere wokhazikika pa nthaŵi yanu. Adzakuninkhaninso chipulumutso chachikulu, luntha lambiri ndi nzerunso zambiri. Kuwopa Chauta ndiko kumapezetsa chuma chimenechi.
7
Anthu ao olimba mtima akufuula m'miseu, akazembe odzayesa kudzetsa mtendere akulira kwamphamvu.
8
M'miseu yaikuluikulu muli zii, palibe odzeramo. Zipangano zaphwanyidwa, mboni zanyozedwa, ndipo palibenso kulemekezana.
9
Dziko likulira ndipo likunka lilikutha. Nkhalango za ku Lebanoni zafota, ndipo chigwa chachonde cha Saroni chasanduka chipululu. Mitengo ya ku dera la Basani ndi ya ku phiri la Karimele ikuyoyoka masamba.
10
Chauta akunena kuti, “Tsopano ndichitapo kanthu, ndiwonetsa mphamvu zanga, ndipo ndidzakhala wolemekezeka kwambiri.
11
Inu mumaganiza zachabechabe, ndipo zonse zimene mumachita nzopandapake. Zotuluka m'kamwa mwanu zili ngati moto umene udzakuwonongani inu nomwe.
12
Anthu a mitundu ina adzakhala ngati miyala yotenthedwa popanga njereza, adzakhala ngati minga yodula, yotenthedwa pamoto.
13
“Inu amene muli kutali, imvani zimene ndachita. Inu amene muli pafupi, dziŵani mphamvu zanga.”
14
Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha, anthu osasamala za Mulungu akunjenjemera. Akunena kuti, “Ndani mwa ife angathe kupirira m'moto woonongawo? Ndani mwa ife angathe kukhalamo m'moto wosatha?”
15
Angathe kutero ndi amene amachita zolungama ndi kulankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga, amene amakutumula manja ake kuti angagwire chiphuphu, amene amatseka makutu kuti angamve mau opangana za kupha anzao, amene amatsinzina kuti angaone zoipa.
16
Munthu wotere adzakhala pa malo otetezedwa. Kothaŵirako iye kudzakhala ku malinga am'matanthwe. Chakudya azidzalandira, ndipo madzi sadzamsoŵa.
17
Nthaŵi imeneyo mudzayang'ana mfumu yooneka mokongola, ndipo mudzaona dziko labwino lotambasukira kutali.
18
Mumtima mwanu muzidzalingalira zimene zinkakuwopsani kale. Muzidzati, “Ali kuti wokhometsa msonkho uja?”
19
Simudzaonanso anthu amwano aja amene chilankhulo chao nchosadziŵika, chachilendo ndi chosamveka.
20
Onani Ziyoni, mzinda wa zokondwerera zathu zachipembedzo. Maso anu adzaona Yerusalemu, mzinda wamtendere, hema losasunthika. Zikhomo zake sizidzazuka, ndipo zingwe zake sizidzaduka.
21
Kumeneko Chauta adzatiwonetsa ulemerero wake. Adzakhala malo a mitsinje yaikulu ndi yaing'ono. Ngalaŵa zankhafi sizidzapitapo, ndipo zombo zazikulu sizidzayendapo.
22
Pakuti Chauta ndiye muweruzi wathu. Chauta ndiye wotilamula, Chauta ndiye mfumu yathu, ndiye amene adzatipulumutsa.
23
Zingwe za zombo za adani athu zamasuka, sizingathe kulimbitsa mlongoti wake, ndipo matanga ake sangathe kufunyuluka. Tsono zofunkha zathu zidzakhala zochuluka kwambiri, kotero kuti pogaŵana, ndi opunduka omwe adzalandirako.
24
Palibe ndi mmodzi yemwe m'dzikomo wodzanena kuti, “Ndikudwala,” ndipo anthu onse akumeneko machimo ao adzakhululukidwa.
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 34 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→