bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 34
Isaiah 34
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 35 →
1
Inu anthu a mitundu yonse, bwerani pafupi kuti mumve, inu anthu onse tcherani makutu! Limvetsere dziko pamodzi ndi zonse zokhalamo, limvetsere dziko lapansi pamodzi ndi zonse zofuma m'menemo.
2
Pakuti Chauta waŵakwiyira anthu a mitundu yonse, waŵapsera mtima magulu ao onse ankhondo, watsimikiza kuti adzaonongedwa, waŵapereka kuti aphedwe.
3
Mitembo ya anthu ao ophedwa adzangoitaya kunja, nimaola ndi kumanunkha, ndipo mapiri adzafiira ndi magazi.
4
Dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi zidzanyenyeka, ndipo mlengalenga udzakulungika monga chimachitira chikopa. Nyenyezi zonse zidzayoyoka monga amachitira masamba a mpesa kapena a mkuyu.
5
Chauta akuti, “Lupanga langa lakhutiratu kumwamba. Si ili likutsika kudzalanga Aedomu, anthu amene ndatsimikiza kuti ndiŵaononga.”
6
Lupanga la Chauta lakhuta magazi, ndipo lakutidwa ndi mafuta. Magazi ake a anaankhosa ndi a mbuzi, ndipo mafuta ake a ku impso za nkhosa zamphongo. Pakuti Chauta ali ndi nsembe mu mzinda wa Bozira, ndiye kuti kuphedwa kwa anthu ambiri m'dziko la Edomu.
7
Pamodzi ndi anthuwo zidzaphedwanso njati ndiponso ng'ombe zamphongo zazing'ono ndi zazikulu zomwe. Dziko lao lidzakhuta magazi, ndipo nthaka yao idzakutidwa ndi mafuta.
8
Imeneyi ndiyo nthaŵi imene Chauta adzalipsira, pamene adzalanga adani a Ziyoni, ndi kuteteza anthu ake.
9
Madzi a m'mitsinje ya ku Edomu adzasanduka phula, ndipo dothi lake lidzasanduka sulufure. Dziko lonse lidzasanduka phula lamoto.
10
Motowo udzayaka usana ndi usiku, ndipo utsi udzafuka kosalekeza. Dziko lidzakhala chipululu pa mibadwo ndi mibadwo, palibe ndi mmodzi yemwe amene adzayendamonso.
11
M'dzikomo muzidzakhala akabaŵi ndi nungu, akadzidzi ndi makwangwala. Chauta adzalisandutsanso dziko loguga ndi lopanda kanthu.
12
Akuluakulu sadzasankhanso mfumu kumeneko, ndipo atsogoleri ake onse adzakhala atachotsedwa.
13
Minga idzamera m'nyumba zake zankhondo zotetezedwa, khwisa ndi mitungwi zidzamera m'malinga mwake. Nkhandwe zizidzayendayenda m'menemo, nthiŵatiŵa zidzapezamo mokhala.
14
Avumbwe adzakumana ndi afisi, nyama zakuthengo zizidzaitanizana. Kumeneko mizimu yoipa yausiku idzafika ndipo idzapeza malo opumulirako.
15
Akadzidzi adzamangako zisa zao, nkuikirako mazira, ndi kuswa ana ao namaŵasamala. Adembo adzasonkhana kumeneko aŵiriaŵiri.
16
Funafunani ndi kuŵerenga m'buku la Chauta. Mwa zolengedwazi palibe chimene chidzasoŵa, ndipo sipadzakhala nchimodzi chomwe chopanda chinzake. Pakuti Chauta walamula kuti zitero, ndipo mzimu wake wazisonkhanitsa pamodzi.
17
Chauta ndiye wagaŵa dzikolo, wapatsa chilichonse chigawo chake. Dzikolo lidzakhala lao mpaka muyaya, ndipo zidzakhala m'menemo pa mibadwo yonse.
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 35 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→