bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 59
Isaiah 59
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 58
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 60 →
1
Chauta si wosoŵa mphamvu, kuti angalephere kukupulumutsani, ndipo si gonthi, kuti nkupanda kumva zimene mukupempha.
2
Machimo anu adakulekanitsani ndi Mulungu wanu, ndipo Iye wakufulatirani chifukwa cha machimo anuwo. Choncho saamva zimene inu mumanena.
3
Manja anu ali psuu ndi magazi a anthu amene mudapha. Mudadziipitsa ndi machimo anu ambiri. Pakamwa panu palankhula zabodza, pamanena zoipa.
4
Palibe amene amaimba mnzake mlandu molungama, palibe wopita ku bwalo lamilandu moona. Amadalira zopanda pake, amangonena mabodza. Amangolingalira zamphulupulu, nachitadi zoipa zimene akuganiza.
5
Ziwembu zao nzoopsa ngati mazira a mphiri, komanso nzosalimba konse ngati ukonde wa kangaude. Wodya mazira a mphiri amafa. Likasweka dzira limodzi mumatuluka mphiri.
6
Ukonde wa kangaude sangauvale ngati nsalu, chimene anthu amapangacho sangafunde konse. Ntchito zao nzoipa ndipo amakonda kuchita zandeu ndi manja ao.
7
Amathamangira kukachita zoipa, sachedwa kupha anthu osalakwa. Maganizo ao onse ali pa zoipa. Kulikonse kumene amapita amasiyako bwinja, ndiponso amaononga.
8
Kumene kuli iwowo, anthu sapeza mtendere. Zonse zimene amachita nzopanda chilungamo. Amayenda m'njira zokhotakhota, ndipo aliyense woyenda m'njira zimenezo sadzapeza mtendere.
9
Anthu akuti, “Chifukwa cha zonsezo chilungamo chatikhalira kutali, ndipo kukhala aungwiro nkosatheka. Timafunafuna kuŵala, koma timangopeza mdima. Timayembekeza kuti kudzakhala mbee, koma kuli bii.
10
Timapapasapapasa ngati anthu akhungu, tili ngati anthu opanda maso. Timaphunthwa masana ngati usiku. Ndife amoyo ndithu, komabe tili ngati anthu akufa.
11
Tonse timabangula ngati zimbalangondo, ndipo timalira modandaula ngati nkhunda. Timayembekeza kuweruza kolungama, koma sitikupeza. Timadikiranso chipulumutso, koma chili nafe kutali.
12
Inu Chauta, takuchimwirani kwambiri. Machimo athu akutitsutsa, zolakwa zathu zili pa ife, ndipo sitingakanepo nchimodzi chomwe.
13
Takupandukirani, takukanani, Inu Chauta, ndipo takana kukutsatani. Tapanikiza anzathu, takupandukirani Inu. Maganizo athu ndi abodza, mau athu ndi onama.
14
Kuweruza kolungama kwalekeka, ndipo kuchita zaungwiro kwaiŵalika. Zoona sizikupezekanso m'mabwalo a milandu, ndipo chilungamo sichikutha kupezeka kumeneko.
15
Zoona zikusoŵa kumeneko, ndipo wina aliyense akapanda kuchita nawo zoipa, amapeza mavuto.” Chauta adaziwona zimenezi ndipo zidamunyansa kuti palibe chilungamo.
16
Chauta adaona kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe adadabwa kuti palibe wochitapo kanthu. Tsono adapambana ndi mphamvu zakezake, ndipo adadzilimbitsa ndi kulungama kwake.
17
Adavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa, ndipo kumutu kwake adavala chisoti chachipulumutso. Adavala kulipsira ngati mkanjo, ndipo mkwiyo udakhala ngati chofunda chake,
18
Chauta adzalanga adani a anthu ake molingana ndi zochita zao: adzaonetsa ukali kwa omuukira, ndipo adzalipsira adani ake. Adzalanga ngakhale okhala m'maiko akutali.
19
Motero anthu adzaopa Chauta kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe. Iyeyo adzabwera ngati mtsinje waliŵiro, wokankhidwa ndi mphepo yamkuntho.
20
Chauta akuuza anthu ake kuti, “Ndidzabwera ku Yerusalemu kudzapulumutsa a fuko la Yakobe amene adaleka machimo ao.
21
“Ndipo ndidzapangana nawo chipangano chakuti, ‘Kuyambira tsopano mpaka muyaya, mzimu wanga umene uli pa iwe, ndiponso mau anga amene ndidaika m'kamwa mwako, sizidzachokeranso m'kamwa mwako kapena m'kamwa mwa ana ako kapena mwa adzukulu ako mpakampaka.’ ”
← Chapter 58
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 60 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→