bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 37
Isaiah 37
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 36
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 38 →
1
Hezekiya atangomva zimenezi, adang'amba zovala zake mwachisoni, ndipo adavala chiguduli, nakaloŵa m'Nyumba ya Chauta.
2
Tsono adatuma Eliyakimu mkulu wa nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa mfumu, ndiponso ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya, mwana wa Amozi.
3
Iwowo adauza Yesaya mau a Hezekiya onena kuti, “Lero ndi tsiku la mavuto, la chilango ndi la manyazi. Tili ngati mkazi wapathupi amene ali pafupi kubala mwana, koma alibe mphamvu zomubalira mwanayo.
4
Mfumu ya ku Asiriya yatuma kazembe wake wankhondo kudzanyoza Mulungu wamoyo. Makamaka Chauta, Mulungu wanu, wamva kunyoza kumeneku, ndipo adzaŵalanga anthu amene adamunyozawo. Motero muŵapempherere anthu otsalaŵa amene akali ndi moyo.”
5
Pamene Yesaya adamva mau a mfumu Hezekiyawo,
6
adati, “Kauzeni mbuyanu mau a Chauta akuti, ‘Usade nawo nkhaŵa mau ondinyoza a atumiki a mfumu ya ku Asiriya.
7
Ndidzaika mumtima mwa mfumuyo ganizo lina lakuti, ikadzangomva mphekesera, idzaumirizidwa kubwerera ku dziko lake, ndipo Ine ndidzamphetsa kwao komweko.’ ”
8
Kazembe wankhondo uja adamva kuti mfumu ya ku Asiriya ija inachoka ku Lakisi, ndipo inali kuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina. Motero anapita kumeneko kukakambirana nayo.
9
Tsono pamene mfumu ya ku Asiriya idamva kuti mfumu Tirihaka wa ku Etiopiya akubwera kudzachita nayo nkhondo, idatumanso amithenga kwa mfumu Hezekiya ndi mau onena kuti,
10
“Mulungu wako amene ukumkhulupirirayo asakunyenge pokulonjeza kuti Yerusalemu sadzagwa m'manja mwa ine mfumu ya ku Asiriya.
11
Wakhala ulikumva zimene mafumu a ku Asiriya adaŵachita maiko onse, kuti adaŵaononga kotheratu. Tsono iweyo ndiye nkupulumuka?
12
Makolo anga adaononga mizinda ya Gozani, Harani ndi Rezefe. Ndipo adapha anthu a ku Edeni amene ankakhala ku Telasara. Kodi milungu ya anthu a mitundu inawo idaŵapulumutsa?
13
Nanga mafumu a m'mizinda ya Hamati, Aripadi, Sefaravaimu, Hena ndi Iva, ali kuti?”
14
Mfumu Hezekiya adalandira kalata kwa amithenga aja, naiŵerenga. Pomwepo adapita ku Nyumba ya Chauta, naika kalatayo m'menemo pamaso pa Chauta,
15
ndipo adapemphera kuti,
16
“Inu Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pamwamba pa akerubi, inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lonse lapansi. Mudalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi.
17
Tsono Inu Chauta, tcherani khutu, mumve. Inu Chauta tsekulani maso, muwone. Mumve mau onse amene Senakeribu adalankhula, onyoza Inu Mulungu wamoyo.
18
Inu Chauta, zoonadi mafumu a ku Asiriya adaononga anthu a mitundu ina yonse, nasandutsa maiko ao chipululu.
19
Adatentha milungu yao imene siinali milungu konse, koma mafano amitengo ndi amiyala opangidwa ndi anthu, nchifukwa chake adaiwononga.
20
Ndiye Inu Chauta, Mulungu wathu, mutipulumutse ife kwa munthu ameneyu, kuti mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziŵe kuti Inu nokha, Chauta, ndiye Mulungu.”
21
Tsono Yesaya, mwana wa Amozi, adatumiza kwa mfumu Hezekiya mau ochokera kwa Chauta, Mulungu wa Israele, oyankha pemphero lake lija lonena za Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya.
22
Poitsutsa za mfumuyo Chauta adati, “Mzinda wa Ziyoni ukukunyoza ndi kukuseka, iwe Senakeribu, mzinda wa Yerusalemu ukupukusa mutu kumbuyo kwako monyodola.
23
“Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira yani? Kodi ndani amene wamufuulira ndi kumuyang'ana monyada? Si wina ai, koma Woyera uja wa Israele!
24
Udatuma atumiki ako kudzanyoza Ine, ndipo udati, ‘Ndi magaleta anga ochuluka ndidakwera mapiri ataliatali, ndidafika mpaka pa nsonga za mapiri a ku Lebanoni. Ndidagwetsa mitengo yake ya mkungudza yaitali kwambiri, ndiponso mitengo yake ya paini yabwino koposa. Ndidaloŵanso m'kati mwake mwenimweni, mwankhalango yake yoŵirira kwabasi.
25
Ndidakumba zitsime ku maiko achilendo ndi kumwamo madzi. Ndi mapazi anga ndidapondereza ndi kuumitsa mitsinje ya ku Ejipito.’
26
“Koma Ine Chauta ndikuti, Kodi sudamvepo kuti zimenezi ndidazikonzeratu kalekale? Ndidaaziganiziratu masiku amakedzana. Tsopano ndazichitadi. Iweyo kwako kunali kungogwetsa mizinda yamalinga ndi kuisandutsa miyulu ya miyala.
27
Anthu amene ankakhala kumeneko anali opanda mphamvu, ankada nkhaŵa, ndipo adaasokonezeka. Anali ngati mbeu zam'munda, ngati udzu wanthete. Anali ngati udzu wapadenga, umene mphepo imauumitsa usanakule nkomwe.
28
“Koma Ine ndimadziŵa zonse za iwe pamene ukukhala pansi, pamene ukuyenda kwina ndi kubwerako, ndiponso pamene ukundikwiyira.
29
Chifukwa chakuti udandikwiyira, ndipo kudzitukumula kwako kudamveka kwa Ine, ndidzakola mphuno yako ndi mbedza, ndi kuika chitsulo m'kamwa mwako. Ndidzakubweza pokuyendetsa m'njira yomwe udadzera pobwera.”
30
Tsono Yesaya adauza mfumu Hezekiya kuti, “Chizindikiro cha zimene zidzachitika ndi ichi: Chaka chino mudzadya tirigu wa mphulumukwa. Chaka chamaŵa mudzadya tirigu wongodzimerera. Tsono chaka chamkucha mudzabzala tirigu ndi kukolola, mudzaoka mitengo yamphesa nkudya zipatso zake.
31
Anthu a m'banja la Yuda amene adzatsalire, adzapezanso bwino, ngati zomera zimene zazimitsa mizu pansi ndi kubala zipatso poyera.
32
Ku Yerusalemu kudzafumira anthu otsala, ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka. Changu cha Chauta Mphambe chidzachitadi zimenezi.
33
“Zimene akunena Chauta za mfumu ya ku Asiriya, ndiizi, akuti, ‘Sadzaloŵa mu mzinda umenewu, sadzaponyamo muvi ndi umodzi womwe. Ankhondo ake azishango sadzafika pafupi ndi mzinda umenewu, ndipo sadzauzinga ndi mtumbira wankhondo.
34
Adzabwerera potsata njira yomwe adaadzera pobwera, ndipo sadzaloŵa mu mzinda umenewu. Ine Chauta ndatero.
35
Ine ndidzautchinjiriza ndi kuuteteza mzinda umenewu chifukwa cha ulemerero wanga, ndiponso chifukwa cha chipangano changa chimene ndidachita ndi Davide mtumiki wanga.’ ”
36
Mngelo wa Chauta adapita ku zithando zankhondo za Aasiriya, naphako asilikali 185,000. M'maŵa mwake anthu adangoona asilikaliwo ali ngundangunda, atafa onsewo.
37
Tsono Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, adachoka ndi kubwerera kwao, nakakhala ku Ninive.
38
Tsiku lina pamene ankapembedza m'nyumba ya Nisiroki, mulungu wake, ana ake aŵiri, Adrameleki ndi Sarezere, adamupha ndi malupanga ao, nathaŵira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarahadoni, mwana wake wina, adaloŵa ufumu m'malo mwake.
← Chapter 36
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 38 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→