bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 46
Isaiah 46
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 45
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 47 →
1
Nayu Beli wapendekeka, Nebo waŵerama! Mafano ameneŵa a Babiloni aŵaika pa abulu ndi ng'ombe. Zinthu zimene kale munkanyamula ndinu, tsopano mukuziika ngati katundu wolemera pamsana pa nyama zotopa.
2
Nyamazo zikuŵerama ndi kufuna kugwa naye katunduyo, sizikutha kumpulumutsa. Izo zomwe zikupita ku ukapolo.
3
“Mundimvere, inu zidzukulu za Yakobe, inu nonse otsala a m'nyumba ya Israele. Ndakhala ndikukusamalani chibadwire chanu, ndidakunyamulani kuyambira m'mimba mwa amai anu.
4
Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.
5
“Kodi Ine mungandifanizire ndi yani, kapena kundilinganiza ndi yani? Kodi mungandiyerekeze ndi yani, kuti Ine ndi iyeyo tikhale ofanana?
6
Anthu ena amatsekula zikwama zao namatulutsamo golide, ndipo amayesa siliva pa masikelo. Amalemba mmisiri wosula, ndipo iye amaŵapangira milungu. Kenaka iwowo amagwada pansi, namaipembedza milunguyo.
7
Amainyamula pa mapewa ao, naisenza. Amaikhazika pamalo pake nikhala pomwepo, ndipo singathe kusuntha pamalo pakepo. Wina aliyense akapemphera kwa milunguyo, siyankha, kapena kumpulumutsa ku mavuto ake.
8
“Mukumbukire zimenezi ndi kuganizapo, muzilingalire, inu ochimwanu.
9
Mukumbukire zamakedzana zija. Mulungu ndine ndekha, palibenso wina ai. Ndithudi, Mulungu ndine, ndipo palibenso wina wonga Ine.
10
Ndidaneneratu zakumathero kuchokera pa chiyambi pomwe. Kuyambira kalekale ndidaloseratu zimene zidakali zosachitikabe. Ndidaanena kuti, ‘Maganizo anga sadzalephera, ndidzachitadi zonse zimene ndidafuna kuchita.’
11
Ndikuitana chiwombankhanga kuchokera kuvuma, ndiye kuti munthu wofumira ku dziko lakutali, amene adzapherezetsa zimene ndikufuna kuchita. Zimene ndalankhula, ndidzazifitsa, zimene ndafuna kuchita ndidzazichitadi.
12
“Mundimvere, inu ouma mitunu, inu amene muli kutali ndi chipulumutso.
13
Tsiku la chipulumutso ndalisendeza pafupi, layandikira, sindidzachedwa kukupulumutsani. Ndidzapulumutsa Ziyoni, ndipo ndidzapatsa dziko la Israele ulemerero.”
← Chapter 45
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 47 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→