bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 51
Isaiah 51
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 50
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 52 →
1
Chauta akunena kuti: “Tcherani khutu inu amene mufuna kupulumuka, inu amene mufuna kuti ndikuthandizeni. Taganizani za thanthwe kumene mudasemedwa, ku nkhuti ya miyala kumene adakukumbani.
2
Taganizani za Abrahamu, bambo wanu ndi Sara amene adakubalani. Pamene ndinkamuitana Abrahamu, adaalibe mwana. Koma ndidamudalitsa, ndidampatsa ana, ndipo ndidachulukitsa zidzukulu zake.
3
Ndidzatonthoza mtima Ziyoni, ndidzaŵatonthoza mtima okhala ku mabwinja ake. Ngakhale dziko lake ndi chipululu, ndidzalisandutsa ngati Edeni. Ngakhale dziko lake ndi thengo, ndidzalisandutsa ngati munda wa Chauta. Kumeneko anthu adzakondwa ndi kusangalala, adzaimba nyimbo zondilemekeza ndi zondithokoza.
4
“Mverani, inu anthu anga, tcherani khutu, inu mtundu wanga. Malamulo adzachokera kwa Ine, ndipo chilungamo changa chidzaunikira anthu onse.
5
Ndidzabwera mofulumira kudzaombola anthu anga, nthaŵi yanga ya kuŵapulumutsa ili pafupi. Ine mwiniwakene ndidzalamulira mitundu ya anthu onse. Maiko akutali akundidikira kuti ndibwere, akundiyembekeza ndi chikhulupiriro kuti ndidzaŵapulumutse.
6
Yang'anani mlengalenga, yang'anani dziko lapansi. Mlengalenga udzazimirira ngati utsi, dziko lapansi lidzatha ngati chovala, ndipo anthu ake onse adzafa ngati ntchentche. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya, ndipo kuwombola kwanga kudzakhala kwa nthaŵi zonse.
7
“Mverani, inu amene mukudziŵa chilungamo, inu amene mukusunga malamulo anga mumtima mwanu. Musachite mantha anthu akamakudzudzulani, musataye mtima akamakulalatirani.
8
Anthu otereŵa adzatha ngati nsalu yodyewa ndi njenjete, adzatha ngati thonje lodyewa ndi mbozi. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya, kuwombola kwanga kudzakhala kwa nthaŵi zonse.”
9
Dzambatukani, Inu Chauta, dzambatukani! Valani dzilimbe. Dzambatukani monga momwe munkachitira masiku amakedzana, nthaŵi ya mibadwo yakale. Kodi sindinu uja mudaduladula Rahabu, chilombo cham'nyanja chija, ndi kubaya chinjoka cham'nyanja chija?
10
Kodi sindinu amene mudaumitsa nyanja yaikulu ija, madzi ozama kwambiri? Kodi sindinu amene mudapanga njira pa madzi, kuti amene mudaŵapulumutsa aoloke pouma.
11
Amene mudaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa. Chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pankhope pao. Adzakhala ndi chikondwerero ndi chisangalalo. Chisoni ndi kubuula zidzatha.
12
Chauta akunena kuti, “Ineineyo ndine amene ndimakutonthozani mtima. Kodi ndinu yani kuti muziwopa munthu woti adzafa, mwanawamunthu amene angokhala nthaŵi yochepa ngati udzu?
13
Kodi ndinu yani kuti muziiŵala Chauta, Mlengi wanu, amene adayalika zakuthambo, ndi kuika maziko a dziko lapansi? Kodi ndinu yani kuti nthaŵi zonse muziwopa ukali wa anthu okuzunzani, amene angofuna kukuwonongani? Ukali wa anthu okuzunzaniwo tsopano uli kuti?
14
Am'ndende adzaŵamasula posachedwa. Sadzafa, sadzaloŵa m'manda, ndipo chakudya sichidzaŵasoŵa konse.
15
Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndimavundula nyanja, kotero kuti mafunde ake amakokoma. Dzina langa ndine Chauta Wamphamvuzonse.
16
Ndidaika mau anga m'kamwa mwanu, ndipo ndidakutetezani ndi dzanja langa. Ndidayalika zakuthambo, ndi kukhazika maziko a dziko lapansi. Ndidauza anthu a ku Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ ”
17
Dzuka, dzuka, imirira, iwe Yerusalemu. Wamwa chikho chachilango chimene Chauta adakupatsa ali wokwiya. Chikhocho nchochititsa chizwezwe, ndipo iwe udachigugudiza.
18
Palibe wina wokutsogolera mwa ana amene udaŵabala. Palibe ndi mmodzi yemwe wokugwira pa dzanja mwa ana amene udaŵalera.
19
Mavuto akugwera paŵiri: dziko lako lasakazika ndi kuwonongeka, ndipo anthu ako apululuka ndi njala ndi nkhondo. Ndani angakumvere chifundo? Ndani angakutonthoze mtima?
20
Ana ako akomoka, ali ngundangunda pa miseu yonse ngati mphoyo zokodwa mu ukonde. Kwaŵagwera kukwiya kwa Chauta ndi kudzudzula kwake.
21
Nchifukwa chake imva iwe amene ukuvutika, iwe amene waledzera, koma osati ndi vinyo.
22
Chauta, Ambuye ako, Mulungu wako, amene amakutchinjiriza, akunena kuti, “Ona, ndakulanda chikho chochititsa chizwezwe chija. Chikhocho, chimene ndidakupatsani ndili wokwiya, sudzachimwanso.
23
Chikhocho ndidzachipereka kwa okuzunza, amene adaakuuza kuti, ‘Gona pansi, tikuyende pamsana.’ Msana wako adauyesa pansi popondapo, adauyesa mseu woti ayendepo.”
← Chapter 50
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 52 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66