bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 14
Isaiah 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 15 →
1
Chauta adzachitira chifundo a m'banja la Yakobe, adzasankhanso Aisraele ndi kuŵalola kuti akhalenso m'dziko lao. Akunja adzabwera kudzakhala nao ndi kuphatikira ku banja la Yakobe.
2
Anthu a mitundu ina adzaperekeza Aisraele ku dziko limene Chauta adaŵapatsa. Kumeneko anthuwo adzakhala otumikira Aisraele ngati akapolo ndi adzakazi. Aisraele adzagwira ukapolo anthu amene kale adaali ambuyao ndi kumalamulira anthu amene kale ankaŵazunza.
3
Chauta adzakupumitsani ku zoŵaŵa ndi mavuto, ndiponso ku ntchito yakalavulagaga imene anthu ankakugwiritsani.
4
Motero mudzanyodola mfumu ya ku Babiloni, mudzati, “Watha bwanji wopsinja uja? Kwatha bwanji kudzikuza kwake kuja?
5
Chauta wathyola mkwapulo wa anthu oipa, wasakaza ndodo yaufumu ya olamulira.
6
Iwowo ankakantha mitundu ya anthu mokwiya pomaŵamenya kosalekeza. Ankalamulira mitundu ya anthu mwaukali ndi kumaŵazunza kosalekeza.
7
Dziko lonse lapansi lapumula, tsopano lakhala bata, ndipo anthu akuimba mokondwa.
8
Mitengo ya paini ikukondwerera kugwa kwa Babiloni. Mikungudza ya ku Lebanoni ikuti, ‘Chigwetsedwere chako pansi, mfumu iwe, palibe wina amene adabwera kudzatigwetsa.’
9
“Kumanda kwatekeseka kuti kukulandire podzafika iwe mfumu ya ku Babiloni. Mandawo adzutsa mizimu ya anthu akufa kuti ikulonjere iwe, adzutsa mizimu ya onse amene adaali atsogoleri pa dziko lapansi. Akuŵaimiritsa pa mipando yao yaufumu onse amene adaali mafumu a mitundu ya anthu.
10
Onsewo adzalankhula, ndipo adzakuuza kuti: ‘Iwenso watheratu mphamvu monga ife! Tsopano tafanana.’
11
Ulemerero wako, pamodzi ndi nyimbo za pa azeze ako, zonse zatha, waloŵa nazo m'manda. Bedi lako ndi mphutsi, chofunda chako ndi nyongolotsi.
12
“Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba, iwe Nthanda, mwana wa Mbandakucha? Wagwetsedwa pansi bwanji, iwe amene unkagonjetsa mitundu ya anthu?
13
Mumtima mwako unkati, ‘Ndidzakwera mpaka kumwamba. Ndidzakhazika mpando wanga waufumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu. Ndidzakhala pampandopo pa phiri la kumpoto kumene imasonkhanako milungu yonse.
14
Ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanafana naye Wopambanazonse.’
15
Koma watsitsidwa m'manda, pansi penipeni pa dzenje.
16
“Anthu akufa akakuwona azidzakupenyetsetsa nkuyamba kulingalira za iwe kuti, ‘Kodi uyu si munthu uja ankanjenjemeretsa dziko lapansi, ndi kugwedeza maufumu?
17
Kodi si ameneyu uja adasandutsa dziko lapansi chipululu ndi kugwetsa mizinda, ndipo sankalola kuti anthu ogwidwa abwerere kwao?’
18
Mafumu onse a mitundu ya anthu akugona mwaulemerero aliyense m'manda akeake.
19
Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako ngati nthambi yoola ndi yonyansa. Mtembo wako waphimbidwa ndi ophedwa amene adabayidwa ndi lupanga, naponyedwa m'dzenje lamiyala. Udzakhala ngati mtembo woponderezedwa.
20
“Sudzaikidwa nao m'manda mwaulemerero, chifukwa chakuti waononga dziko lako, wapha anthu ako. “Zidzukulu za anthu ochita zoipa zisadzakumbukike mpang'ono pomwe.
21
Mukonzekere kupha ana aamuna a mfumuyi, chifukwa cha kulakwa kwa atate ao, kuwopa kuti angadzuke ndi kulanda dziko lapansi ndi kulidzaza dziko lonselo ndi mizinda.”
22
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndidzauthira nkhondo mzinda wa Babiloni. Ndidzathetseratu dzina lake ndi onse otsaliramo. Sipadzapulumuka ana ndi zidzukulu zomwe. Ndatero Ine Chauta.
23
Mzindawo ndidzausandutsa dambo lamatope ndi malo okhalamo akanungu. Ndidzausesa ndi tsache lofafaniza zonse zotsala. Ndatero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”
24
Chauta Wamphamvuzonse walumbira kuti, “Monga momwe ndaganizira, zidzachitikadi choncho, ndipo monga momwe ndatsimikizira zidzakhala momwemo ndithu.
25
“Ndidzaŵaononga Aasiriya m'dziko langa, ndipo ndidzaŵapondereza ndi mapazi pa mapiri anga. Tsono anthu anga ndidzaŵavula goli limene Aasiriya adaŵaveka, ndidzaŵachotsera katundu wolemetsa pa mapewa ao.
26
“Zimenezi ndizo zimene ndagamula kuti zidzachitike pa dziko lonse lapansi. Ndatambalitsa dzanja langa kuti ndilange anthu a mitundu yonse.”
27
Chauta Wamphamvuzonse ndiye watsimikiza kuti zimenezi zichitike, nanga ndaninso angathe kumletsa? Dzanja lake nlotambalitsa, nanga ndaninso angalibweze?
28
Chaka chimene mfumu Ahazi adafa, padamveka ulosi uwu:
29
“Musakondwe inu anthu a ku Filistiya, poona kuti adatha Aasiriya amene adaali ngati ndodo yokumenyani. Mu mtundu wa njoka wamba mudzatuluka mphiri, ndipo mu mtundu wa mphiriyo mudzatuluka chinjoka chaliŵiro chaululu.
30
“Osauka zedi adzapeza chakudya, amphaŵi adzakhala pabwino. Koma mtundu wanu Afilistinu ndidzauwononga ndi njala, ndi otsalira omwe ndidzaŵapha.
31
“Lirani kwamphamvu inu apachipata! Pemphani chithandizo mofuula, inu amumzinda! Njenjemerani ndi mantha nonse Afilisti! Onani fumbi likuchita kuti kodoo kuchokera kumpoto, ndipo mwa ankhondo akubwerawo palibe wamantha.”
32
Kodi tidzaŵayankhanji amithenga a ku Filistiyawo? Tidzati, “Chauta adakhazikitsa kale Ziyoni, ndipo mu mzinda umenewu anthu ake ozunzika amapeza populumukira.”
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66