bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 60
Isaiah 60
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 59
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 61 →
1
Iwe Yerusalemu dzuka, ŵala, kuŵala kwako kwayamba. Ulemerero wa Chauta wakuŵalira.
2
Mdima udzaphimba dziko lapansi, mdima wandiweyani udzagwa pa anthu a mitundu ina. Koma iwe, Chauta adzakuŵalira, ulemerero wake udzaoneka pa iwe.
3
Anthu a mitundu ina adzatsata kuŵala kwako, mafumu adzalondola kunyezimira kwako konga dzuŵa limene likutuluka kumene.
4
Yang'ana pozungulira, uwone zimene zikuchitika. Onse akusonkhana kuti abwere kwa iwe. Ana ako aamuna adzabwera kuchokera kutali. Ana ako aakazi adzatengedwa m'manja ngati ana.
5
Udzaona zimenezi, ndipo udzakondwa, mtima wako udzalumpha ndi chimwemwe. Chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe. Chuma cha maiko onse chidzabwera kwa iwe.
6
Kudzafika mtindiri wa ngamira, ngamira zing'onozing'ono, kuchokera ku Midiyani ndi ku Efa. Onse a ku Sheba adzabwera. Adzakhala atatenga golide ndi lubani, ndipo adzatamanda Chauta mokweza mau.
7
Ziŵeto zonse za ku Kedara adzazisonkhanitsa kwanu, nkhosa zamphongo za ku Nabayoti zidzakuthandizani pamene mudzazisoŵa. Zidzaperekedwadi pa guwa ngati nsembe. Choncho Ine Chauta ndidzapatsa Nyumba yanga ulemerero waukulu kupambana kale.
8
Kodi nzinthu zanji zikuti yakaliyakali ngati mitambozi, zikuchita ngati nkhunda zobwerera kumakomo kwakezi?
9
Zimenezo ndi zombo zochokera ku maiko akutali, za ku Tarisisi zili patsogolo. Zikudzatula ana anu amene atenga siliva ndi golide, kuti alemekeze dzina la Chauta, Mulungu wanu, Woyera uja wa Israele, chifukwa Iyeyo adakupatsani ulemerero.
10
Chauta akuuza Yerusalemu kuti, “Alendo adzamanganso malinga ako, ndipo mafumu ao adzakutumikira. Ndidakulanga pamene ndinali wokwiya, koma tsopano ndidzakukomera mtima ndi kukuchitira chifundo.
11
Zipata zako zidzakhala zotsekula nthaŵi zonse. Usana ndi usiku womwe sadzazitseka, kuti choncho anthu a mitundu yonse adzabwere ndi chuma chao kwa iwe, akuyenda pa mdipiti, mafumu ao ali patsogolo.
12
Koma maiko ndi mafumu amene sakutumikira, adzaonongekeratu. Anthu a mitundu imeneyo adzaonongeka kotheratu.”
13
“Mitundu itatu ija ya mitengo ya paini, imene ili yabwino kwambiri m'nkhalango ya ku Lebanoni, adzabwera nayo kuti akongoletsere Nyumba yanga. Motero m'Nyumba m'mene ndimakhala Ine mudzalemekezeka.
14
Ana a amene adaakuzunzapo adzabwera ndipo adzakugwadira kuwonetsa ulemu. Onse amene adaakunyozapo adzakuŵeramira mpaka pansi. Adzakutchula kuti Mzinda wa Chauta, ndiye kuti Ziyoni, mzinda wa Woyera uja wa Israele.”
15
“Ngakhale anthu adakusiya nadana nawe, osadutsanso mwa iwe, ndidzakukuza mpaka muyaya, ndipo udzakhala malo a chimwemwe pa mibadwo ndi mibadwo.
16
Monga mwana woyamwa udzadya chuma cha anthu a mitundu ina, ndipo mafumu ao omwe adzakusamala. Motero udzadziŵa kuti Ine Chauta ndine Mpulumutsi wako, ndipo kuti ndine Momboli wako, Wamphamvu uja wa Yakobe.”
17
“Ndidzakupatsa golide m'malo mwa mkuŵa, m'malo mwa chitsulo ndidzakupatsa siliva, mkuŵa m'malo mwa mtengo, chitsulo m'malo mwa mwala. Okuyang'anira ndidzaŵasandutsa amtendere, okulamulira ndidzaŵasandutsa olungama.
18
Ziwawa sizidzamvekanso. Dziko lako silidzaonongekanso. Ndidzakhala ngati linga lokuteteza, ndipo udzanditamanda chifukwa chokupulumutsa.”
19
“Sipadzafikanso dzuŵa loti likuŵalire masana, kapena mwezi wokuŵalira usiku. Koma Ine Chauta ndiye ndidzakuŵalire mpaka muyaya. Ine Mulungu wako ndiye ndidzakhale ulemerero wako.
20
Chokuunikira ngati dzuŵa sichidzaloŵanso, ndipo chokuunikira ngati mwezi sichidzazimiriranso, chifukwa ndi Chauta amene adzakhala kuŵala kwako mpaka muyaya. Choncho masiku ako olira adzatha.
21
Anthu ako onse adzayenda m'njira zoyenera, ndipo dzikolo lidzakhala lao mpaka muyaya. Anthuwo ndidaŵaika ndine, ndidaŵalenga ndine, kuti aonetse ulemerero wanga kwa onse.
22
Ngakhale kabanja kakang'onong'ono kadzasanduka fuko, ndipo kafuko kakang'onong'ono kadzasanduka mtundu wamphamvu. Ndidzachita zimenezi mofulumira nthaŵi yake itafika. Ine ndine Chauta.”
← Chapter 59
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 61 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→