bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 23
Isaiah 23
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 24 →
1
Nawu ulosi wonena za Tiro. Fuulani mwachisoni, inu oyendetsa zombo za ku Tarisisi! Pakuti mzinda wa Tiro waonongeka, kulibenso nyumba kapena dooko! Zimenezi adazimva pochokera ku Kitimu.
2
Khalani chete, inu anthu okhala m'mphepete mwa nyanja, inu amalonda a ku Sidoni! Amithenga anu adaoloka nyanja, ndipo adayenda pa nyanja zazikulu.
3
Phindu lanu linali tirigu wa ku Sihore, zokolola za ku Nailo, ndipo munkachita malonda ndi anthu a mitundu yonse.
4
Chita manyazi, iwe Sidoni, mzinda wamalinga wakunyanja, chifukwa nyanjayo yalankhula, yanena kuti, “Sindinamvepo zoŵaŵa za kubala, sindinaberekepo ana, ndipo sindinalerepo mwana, wamwamuna kapena wamkazi.”
5
Aejipito adzadzidzimuka ndi kuchita mantha, akadzamva kuti Tiro adaonongeka.
6
Thaŵirani ku Tarisisi, fuulani mwachisoni, inu okhala m'mphepete mwa nyanja.
7
Kodi ndi uwu mzinda wa Tiro wotchukawu, mzinda wakalekale uja? Kodi ndi uwu mzinda uja unkatumiza anthu kuwoloka nyanja kukakhala ku maiko ena?
8
Kodi ndani amene adakonza zimenezi kuti zigwere Tiro, mzinda uja wopereka ukulu kwa anthuwu, umene amalonda ake anali akalonga ndiponso otchuka kwambiri pa dziko lonse lapansi?
9
Chauta Wamphamvuzonse ndiye adakonza zimenezi kuti athetse kunyada kwao, kuti atsitse anthu onse olemekezeka a pansi pano.
10
Mubalalike m'dziko mwanu ngati mtsinje wa Nailo, inu anthu a ku Tarisisi. Palibenso china choti nkukutchinjirizani.
11
Chauta watambalitsa dzanja lake kuloza nyanja ndipo wagwedeza maufumu. Walamula a ku Kanani kuti agwetse malinga ao.
12
Ndipo adati, “Simudzakondwanso, inu anthu a mu mzinda wa Sidoni, mudzapanikizidwa, ndipo ngakhale muthaŵire ku Kitimu, nkumeneko komwe simukapeza mpumulo.”
13
Onani dziko la Ababiloni, anthu ameneŵa palibenso, adatheratu. Aasiriya ndi amene asandutsa Tiro kuti akhale malo a zilombo. Adamanga nsanja zao zankhondo, adagumula malinga ake nasandutsa mzindawo bwinja.
14
Lirani kwambiri, inu oyendetsa zombo a ku Tarisisi, chifukwa mzinda wanu wamalinga wagwetsedwa.
15
Nthaŵi ikubwera pamene Tiro adzaiŵalika pa zaka makumi asanu ndi aŵiri, imene ili ngati nthaŵi ya moyo wonse wa mfumu imodzi. Zitatha zaka zimenezo, Tiro adzakhala ngati mkazi wachiwerewere uja woimbidwa nyimbo ija yakuti:
16
“Tenga zeze wako, uzungulire mzinda, iwe mkazi wachiwerewere woiŵalika. Uimbe zezeyo mokometsera, uimbenso nyimbo zako zija, kuti anthu akukumbukire.”
17
Zitatha zaka makumi asanu ndi aŵiri, Chauta adzachitapo kanthu pa Tiro. Mzindawo udzabwerera ku ganyu wake wakale uja. Ndipo adzachita zachiwerewere ndi maufumu a dziko lonse lapansi.
18
Koma phindu lake ndi malipiro ake adzazipereka kwa Chauta. Sadzachita nazo kaligwiritsa kapena kuzikundika, koma adzazipereka kwa otumikira Chauta, kuti agule zakudya zambiri ndi zovala zokongola.
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→