bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 38
Isaiah 38
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 37
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 39 →
1
Nthaŵi imeneyo mfumu Hezekiya adaadwala, ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya, mwana wa Amozi, adapita kukamuwona, namuuza kuti, “Chauta akuti ukonze zonse bwino lomwe, poti ufa, suchira ai.”
2
Pomwepo Hezekiya adatembenuka nayang'ana ku khoma, nayamba kupemphera kwa Chauta kuti,
3
“Inu Chauta, mukumbukire kuti ndakhala ndikukutumikirani mokhulupirika ndi modzipereka. Ndipo nthaŵi zonse ndinali kuchita zokukomerani.” Atatero adayamba kulira ndi mtima woŵaŵa.
4
Tsono Chauta adalamula Yesaya kuti,
5
“Pitanso kwa Hezekiya, ukamuuze kuti, ‘Ine Chauta, Mulungu wa kholo lako Davide, ndamva pemphero lako, ndipo misozi yako ndaiwona. Nchifukwa chake ndidzakuwonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako.
6
Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzindawu kwa mfumu ya ku Asiriya, ndipo mzindawu ndidzautchinjiriza.’ ”
7
Yesaya adauza Hezekiya kuti, “Chauta adzakupatsani chizindikiro kutsimikiza kuti adzasunga lonjezo lake.
8
Akuti, ‘Chithunzithunzi chimene dzuŵa likuchititsa pa makwerero a Ahazi, ndidzachibweza m'mbuyo makwerero khumi.’ ” Ndipo chithunzithunzicho chidabwereradi m'mbuyo makwerero khumi.
9
Ndakatulo ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda, amene adaadwala kenaka nkuchira:
10
“Ndinkaganiza kuti ndizipita ku dziko la akufa, ndidakali mnyamata wabiriŵiri, ndipo kuti ndidzakhala komweko mpakampaka.
11
Ndinkaganiza kuti pa dziko lino la anthu amoyo, sindidzaonanso Chauta, anthu okhala pansi pano sindidzaŵapenyanso.
12
Moyo wanga walandidwa ndi kuchotsedwa, ngati hema logwetsedwa, ngati nsalu yodulidwa ku makina ake oombera. Kuyambira m'maŵa mpaka usiku mwakhala mukunditsiriza.
13
Usiku wonse mpaka m'maŵa ndinkalira ndi ululu. Munkaphwanya mafupa anga onse, monga umachitira mkango. Kuyambira m'maŵa mpaka usiku mwakhala mukunditsiriza.
14
“Ndinkalira ngati namzeze wovutika, ndinkabuula ngati nkhunda yodandaula. Maso anga adaatopa nkuyang'ana kumwamba. Inu Ambuye, ndili m'mavuto, dzanditetezeni.
15
Kodi ndinganene chiyani? Chauta walankhula nane, ndipo wachita zimenezi ndiye amene. Pa moyo wanga wonse ndidzakhala wovutika, chifukwa cha kuŵaŵa kwa mtima wanga.
16
“Inu Ambuye, anthu amakhala moyo ndi zimenezi, moyo wa mzimu wanga uli mu zomwezo. Mundichiritse ndi kundibwezera moyo.
17
Chimene ndidamvera zoŵaŵa nkuti ndipeze bwino. Mwapulumutsa moyo wanga ku manda, mwataya machimo anga onse kumbuyo kwanu.
18
Akumanda sangathe kukuyamikani, akufa sangathe kukutamandani. Otsikira ku manda sangathe kukukhulupirirani.
19
Amoyo, amoyo okha, ndiwo amakutamandani, monga m'mene ndikuchitira ine tsopanomu. Atate amauza ana ao za kukhulupirika kwanu.
20
“Chauta wandipulumutsa, ndipo tidzamtamanda poimba ndi azeze m'Nyumba mwa Chauta pa moyo wathu wonse.”
21
Pamenepo Yesaya adati, “Anthu atenge ntchintchi yankhuyu, aimate pa chithupsa, ndipo mfumu Hezekiya adzachira.”
22
Tsono mfumu Hezekiya adafunsa kuti, “Kodi chizindikiro chake nchiyani chotsimikizira kuti ndidzapita ku Nyumba ya Chauta?”
← Chapter 37
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 39 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→