bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 49
Isaiah 49
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 48
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 50 →
1
Mverani inu anthu a ku maiko a m'mphepete mwa nyanja, tcherani khutu, inu anthu akutali. Chauta adandiitana ndisanabadwe, adanditchula dzina ndidakali m'mimba mwa amai anga.
2
Adasandutsa pakamwa panga kuti pakhale ngati lupanga lakuthwa. Adanditchinjiriza ndi dzanja lake. Adandisula ngati muvi wakuthwa, nandibisa m'phodo mwake.
3
Adandiwuza kuti, “Iwe Israele ndiwe mtumiki wanga. Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.”
4
Koma ndidati, “Ndagwira ntchito yopanda phindu. Ndangoononga mphamvu zanga pachabe.” Komabe zondiyenerera zili m'manja mwa Chauta, mphotho yanga ili m'manja mwa Mulungu wanga.
5
Chauta ndi amene adandiwumba m'mimba mwa amai anga kuti ndikhale mtumiki wake, kuti ndibweze fuko la Yakobe kwa Iye, ndipo kuti ndisonkhanitse Aisraele pafupi ndi Iye. Choncho ndimalemekezeka m'maso mwa Chauta, ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga.
6
Chautayo akunena kuti, “Nchinthu chochepa kwambiri kuti ukhale mtumiki wanga, kuti udzutse mafuko a Yakobe ndi kuŵabweza kwao Aisraele amene adapulumuka. Ndidzakusandutsa kuŵala kounikira mitundu ina ya anthu, kuti chipulumutso changa chikafike mpaka ku mathero a dziko lapansi.”
7
Chauta, Mpulumutsi ndi Woyera uja wa Israele, akulankhula ndi wonyozedwa kwambiri uja, wodedwa ndi mitundu ina ya anthu, kapolo wa mafumu ankhanza. Akunena kuti, “Mafumu adzaimirira mwaulemu poona iwe, akalonga nawonso adzadziponya pansi chafufumimba. Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Chauta, amene ali wokhulupirika, Woyera uja wa Israele, amene adakusankhula.”
8
Chauta akunena kuti, “Nthaŵi imene ndidakukomera mtima, ndidakuyankha, ndipo tsiku la chipulumutso ndidakuthandiza. Ndidakusunga ndipo ndidakusandutsa kuti ukhale chipangano kwa anthu, kuti ndilibwezere dziko mwakale ndi kuligaŵagaŵa dziko loonongekali.
9
Ndidzauza am'ndende kuti atuluke, ndi amene ali mu mdima kuti aonekere poyera. Adzapeza chakudya m'mphepete mwa njira, adzapeza busa pa magomo.
10
Sadzamva njala kapena ludzu. Mphepo yotentha kapena dzuŵa sizidzaŵapsereza, chifukwa amene amaŵachitira chifundo adzaŵatsogolera ndi kuŵaperekeza ku akasupe a madzi.
11
Mapiri anga onse ndidzaŵasandutsa njira yoyendamo, ndipo miseu yanga yaikulu ndidzaikonza.
12
Onani, anthu anga adzachokera kutali, ena kumpoto, ena kuzambwe, enanso adzachokera ku Asuwani kumwera.”
13
Imbani mokondwa, inu zolengedwa zamumlengalenga! Fuula ndi chimwemwe, iwe dziko lapansi! Yambani nyimbo, inu mapiri! Chauta watonthoza mtima anthu ake, ndi kuŵamvera chifundo anthu ake ovutika.
14
Koma anthu a ku Ziyoni adati, “Chauta watisiya ife, Ambuye atiiŵala.”
15
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse.
16
Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
17
Amisiri odzakumanganso akubwera mofulumira, ndipo okupasula ndi okuwononga akuchokapo.
18
Uyang'ane pozungulira, uwone zimene zikuchitika. Anthu ako onse akusonkhana, akubwera kwa iwe. Pali Ine ndemwe, Mulungu wamoyo, anthu ako adzakhala chinthu chokukongoletsa. Udzaŵaonetsera monga amachitira mkwati wamkazi.
19
Ndithudi, iwe amene wasanduka bwinja, amene udaasiyidwa ndi kusakazika, tsopano udzaŵachepera anthu odzakhala mwa iwe. Ndipo amene adakuwononga aja adzaŵapirikitsira kutali ndi iwe.
20
Ana ako obadwa pa nthaŵi yako yachisoni adzakuneneranso m'khutu mwako kuti, ‘Dziko likutichepera, utikulitsire malo oti tizikhalapo.’
21
Tsono iwe udzadzifunsa kuti, ‘Kodi ndani adandiberekera ana aŵa? Ana anga onse adamwalira ndipo sindidanthenso kukhala ndi ana ena. Ndidaali ku ukapolo, ndidaaiŵalika. Nanga ndani adaŵalera ana ameneŵa? Ndidaatsala ndekha. Nanga ana ameneŵa adachokera kuti?’ ”
22
Ambuye Chauta akunena kuti, “Ndidzakodola anthu a mitundu ina. Ndidzaŵakwezera mbendera kuti adzabwere. Tsono adzabwera nawo ana ako aamuna ataŵatengera m'manja, ndiponso ana ako aakazi, ataŵasenzera pa mapewa.
23
Mafumu adzakhala ngati atate okulerani, akazi a mafumuwo adzakhala ngati amai okuyamwitsani. Adzagwetsa nkhope zao pansi ndi kukuŵeramirani. Adzaseteka fumbi la m'mapazi mwanu modzichepetsa. Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndipo amene amakhulupirira Ine sadzachita manyazi.”
24
Kodi mungathe kuŵalanda ankhondo zofunkha zao? Kodi mungathe kuŵapulumutsa akaidi kwa mfumu yankhalwe?
25
Chauta akuyankha kuti, “Ndithudi, ankhondo adzaŵalanda akaidi ao, ndipo mfumu yankhalwe adzailanda zofunkha zake. Ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu, ndipo ndidzapulumutsa ana anu.
26
Ndidzaumiriza okuzunzani kuti adzadye mnofu wao womwe. Ndipo adzaledzera nawo magazi ao omwe, monga momwe adakachitira ndi vinyo watsopano. Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mpulumutsi wanu, ndine Momboli wanu, Wamphamvu uja wa Yakobe.”
← Chapter 48
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 50 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→