bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 24
Isaiah 24
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 25 →
1
Zoona, Chauta adzaononga dziko lapansi ndi kulisandutsa chipululu. Adzalisakaza, nadzamwaza anthu ake onse.
2
Aliyense adzaona zimodzimodzi: ansembe ndi anthu, akapolo aamuna ndi ambuyao aamuna, adzakazi ndi ambuyao aakazi, ogula ndi ogulitsa, obwereka ndi oŵabwereka, ndiponso okongola ndi okongoza.
3
Dziko lapansi lidzaonongedwa kwathunthu, lidzasakazikiratu, pakuti Chauta wanena zimenezi.
4
Dziko likulira ndipo likufota. Dziko lonse lapansi likuvutika ndipo likuuma. Mlengalenga ukuvutika pamodzi ndi dziko lapansi.
5
Anthu aipitsa dziko lapansi posatsata malamulo a Mulungu, ponyoza mau ake, ndipo pophwanya chipangano chamuyaya chimene Iye adapangana nawo.
6
Nchifukwa chake Mulungu watemberera dziko lapansi, anthu am'dzikomo akuzunzika chifukwa cha machimo ao. Iwo amalizika, ndipo atsala ndi oŵerengeka okha.
7
Mphesa zikuuma, ndipo vinyo akusoŵa. Aliyense amene ankasangalala ali ndi chisoni.
8
Kulira kokometsera kwa ting'oma tao kwatha, phokoso la anthu osangalala latha, zeze wosangalatsa uja wati zii.
9
Anthu saimbanso pomwa vinyo, akamamwa zaukali zimaŵaŵa m'kamwa mwao.
10
Mu mzinda wachisokonezo uja zonse zaonongedwa, nyumba iliyonse yatsekedwa, kotero kuti palibe wotha kuloŵamo.
11
Anthu akufuula m'miseu chifukwa cha kusoŵa kwa vinyo. Chimwemwe chonse chatheratu, palibenso chisangalalo pa dziko lonse lapansi.
12
Mzinda wasanduka bwinja, zipata zake zagumuka.
13
Zimenezi ndizo zimene zidzachitikire mtundu uli wonse wa pa dziko lapansi. Kudzakhala ngati khunkha la olivi ndi khunkha la mphesa, pamene kholola latha.
14
Koma otsala aja adzafuula ndi kuimba mokondwa. Akuzambwe adzatamanda ukulu wa Chauta.
15
Nchifukwa chake inu akuvuma, tamandani Chauta. Anthu okhala m'mphepete mwa nyanja, yamikani Ambuye, Mulungu wa Israele.
16
Kuchokera ku maiko akutali tilikumva nyimbo zotamanda, zoyamika Wolungama uja. Koma ine ndikuti: Ndatheratu, ndatheratu! Tsoka kwa ine! Onyenga akupitirizabe ndipo kunyenga kwao kukupitabe m'tsogolo.
17
Inu anthu a dziko lapansi, zoopsa, mbuna ndi misampha zikukudikirani.
18
Aliyense wothaŵa phokoso la zoopsazo adzagwa m'mbuna, ndipo wotuluka m'mbunamo adzakodwa mumsampha. Kudzagwa mvula yachigumula ndipo maziko onse a dziko adzagwedezeka.
19
Dziko lapansi lidzathyokathyoka, lidzang'ambika kwathunthu ndi kugwedezeka kwamphamvu.
20
Dziko lapansi lidzadzandira ngati munthu woledzera, lidzagwedezeka ngati chisimba nthaŵi ya mkuntho. Dziko lapansi lalemedwa ndi zoipa zake, lidzagwa ndipo silidzaukanso.
21
Tsiku limenelo Chauta adzalanga kumwamba zamphamvu zakumwamba, ndipo pansi pano mafumu a pansi pano.
22
Mulungu adzasonkhanitsa mafumu onse pamodzi, ngati am'ndende amene ali m'dzenje. Adzaŵatsekera m'ndende, ndipo patapita nthaŵi yaitali, adzalangidwa.
23
Mwezi udzanyala, ndipo dzuŵa lidzachita manyazi, pakuti Chauta Wamphamvuzonse adzakhala mfumu. Adzalamulira pa phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→