bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 36
Isaiah 36
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 35
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 37 →
1
Chaka cha 14 cha ufumu wa Hezekiya, mfumu ya ku Yuda, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya adathira nkhondo mizinda yonse yamalinga ya ku Yuda, nailanda.
2
Pambuyo pake mfumu ya ku Asiriyayo idatuma kazembe wake wankhondo kuchokera ku Lakisi, kuti apite ndi gulu lalikulu lankhondo kwa Hezekiya ku Yerusalemu. Tsono kazembeyo adaima pafupi ndi ngalande yamadzi yochokera ku dziŵe lakumtunda, pa mseu waukulu wopita ku malo a mmisiri woyeretsa nsalu.
3
Anthu atatu adatuluka mu mzinda nakakumana naye. Anthu ake ndi aŵa: mkulu woyang'anira nyumba ya mfumu, dzina lake Eliyakimu mwana wa Hilikiya, Sebina mlembi wa bwalo, ndi Yowa mwana wa Asafu, wolemba zochitika.
4
Kazembe wankhondo uja adaŵauza kuti akanene kwa Hezekiya mau aŵa: “Mfumu yaikulu, mfumu ya ku Asiriya ikuti, ‘Chimene chikulimbitsa chikhulupiriro chako motere nchiyani?
5
Kodi ukuganiza kuti mau okha nkulingana ndi luso ndi mphamvu pa nkhondo? Kodi tsono ukudalira yani kuti uzindigalukira?
6
Makamaka ukuyembekeza kuti Ejipito adzakuthandiza. Koma kuteroko kuli ngati kukhulupirira bango lothyoka limene litha kum'baya munthu m'manja ataliyesa ndodo yoyendera. Ndimo m'mene mfumu ya ku Ejipito imamchitira aliyense woidalira.
7
“Kapena undiwuza kuti mumakhulupirira Chauta Mulungu wanu.” Kodi si Mulungu yemweyo amene akachisi ake ndi maguwa ake, Hezekiya adaŵathetsa, nauza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, “Muzipembedza pa guwa ili la ku Yerusalemu?”
8
Tiye tsono utembezane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: Ndidzakupatsa akavalo okwanira zikwi ziŵiri ngati iwe ungathe kupeza anthu ake okwerapo.
9
Ungathe bwanji kupambana ngakhale mmodzi yekha mwa akazembe ang'onoang'ono a mbuye wanga, pamene ukukhulupirira Aejipito, kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo?
10
Ndiponso kodi sukudziŵa kuti ndi Chauta amene wandibweretsa kuno, ndidzathire nkhondo dziko lino ndi kuliwononga? Chautayo ndiye adachita kundiwuza kuti ndilimbane nalo ndi kuliwononga dziko lino.’ ”
11
Pamenepo Eliyakimu, Sebina ndi Yowa adauza kazembeyo kuti, “Pepani, mutilankhule m'Chiaramu atumiki anufe, poti timachimvetsa. Musatilankhule m'Chiyuda, pakuti anthu onse ali pakhomaŵa alikumva.”
12
Koma kazembe uja adati, “Kodi mukuganiza kuti mfumu yanga idandituma kuti ndilankhule mau ameneŵa kwa inu nokha ndi kwa mfumu yanu basi? Iyai, ndikulankhulanso kwa anthu amene akhala pakhomowo, amene adzayenera kudya ndoŵe yao yomwe ndi kumwa mkodzo wao womwe, monga momwe mudzachitire inuyo.”
13
Tsono kazembe uja adaimirira nafuula m'Chiyuda kuti, “Mverani mau a mfumu yaikulu, mfumu ya ku Asiriya.
14
Mfumuyo ikuti, ‘Musalole kuti Hezekiya akunyengeni, chifukwa sadzatha kukupulumutsani.
15
Asakukakamizeni kuti mudalire Chauta pokuuzani kuti mosapeneka konse Chauta wanuyo adzakupulumutsani, ndipo kuti mfumu ya ku Asiriya sidzalanda mzinda wanuwu.
16
Musamumvere Hezekiya. Mfumu ya ku Asiriya ikukulamulani kuti mutulukemo mumzindamo, ndipo muigonjere. Mukatero, aliyense mwa inu azidzadya mphesa ndi nkhuyu zake ndi kumamwa madzi a m'chitsime chake,
17
mpaka nthaŵi imene mfumuyo idzakutengeni kupita nanu ku dziko lolingana ndi lanuli, dziko la mwana alirenji.
18
Ndiye inu chenjerani, Hezekiya asakupusitseni pokuuzani kuti Chauta adzakupulumutsani. Mwa milungu ya anthu a mitundu ina, kodi alipo ndi mmodzi yemwe amene adapulumutsapo dziko lake kwa mfumu ya ku Asiriya?
19
Kodi milungu ya Hamati ndi Aripadi ili kuti tsopano? Nanga milungu ya Sefaravaimu ili kuti? Kodi milunguyo idaupulumutsa mzinda wa Samariya kwa mbuye wanga?
20
Kodi ndi iti mwa milungu ya maikoŵa imene idapulumutsapo maiko ake kwa mfumu yathu, kuti inu muziti Chauta nkupulumutsa Yerusalemu kwa mfumu yathuyo?’ ”
21
Koma anthu adangokhala chete osayankhapo kanthu, chifukwa mfumu Hezekiya adaaŵalamula kuti, “Musamuyankhe ai.”
22
Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya amene ankayang'anira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo, ndi Yowa mwana wa Asafu, wolemba zochitika, adang'amba zovala zao mwachisoni, ndipo adapita kwa mfumu Hezekiya nakamuuza zimene kazembe wa ku Asiriya uja adaalankhula.
← Chapter 35
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 37 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→