bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 57
Isaiah 57
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 56
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 58 →
1
Anthu a Mulungu okhulupirira amafa, ndipo palibe amene amasamalako. Anthu okhulupirika amatengedwa, ndipo palibe amene amamvetsa chifukwa chake. Anthu olungama amachotsedwa, kuti tsoka lisaŵagwere,
2
ndipo amafa mwamtendere. Amene ali olungama amapumula bwino pogona pao.
3
Senderani kuno, inu anthu ochita zoipa, pakuti muli ngati zidzukulu zam'chigololo, zochokera m'zadama.
4
Kodi inu mukuseŵera ndi yani? Kodi mukunena yani? Mukunyoza yani? Kodi ochimwa sindinu? Onyenga sindinu?
5
Mumapembedza mafano pa mitengo ya thundu, patsinde pa mtengo wogudira uliwonse. Mumapereka ana anu ngati nsembe m'zigwa, m'ming'alu yam'mathanthwe.
6
Mumatenga miyala yosalala kumadamboko, ndi kumaipembedza ngati milungu. Mumapereka chopereka cha chakumwa kwa iyo, ndi kuperekanso chopereka cha chakudya. Kodi zimenezi zingandikondweretse?
7
Pa phiri lalitali ndi looneka kutali mudakaika bedi kukachita zadama, komwekonso mudakapereka nsembe.
8
M'nyumba mwanu mwaika mafano ku chitseko ndiponso pa mphuthu. Ine mwandisiya, mwavula zovala zanu, mwakwera pa bedi lanu lalikulu ndi zibwenzi zanu zimene mwazilipira kuti mugone nazo. Kumeneko mwakwaniritsa zilakolako zanu zoipa.
9
Mudadzola mafuta ndi zonunkhira zochuluka, ndipo mudapita kukapembedza fano lija la Moleki. Mudachita kutuma nthumwi kutali, mudazituma ngakhale kumanda komwe.
10
Mudatopa nawo mtunda wouyenda, koma osanena kuti, “Ndingoleka!” Mudapezera zina mphamvu, mwakuti simudalefuke konse.
11
“Kodi ndi milungu yanji imene mudaiwona nkuchita nayo mantha, kotero kuti mudandinamiza nkundiiŵaliratu, osalabada konse za Ine? Kodi mwaleka kundiwopa chifukwa choti ndakhala chete pa nthaŵi yaitali?
12
Mukuganiza kuti zimene mumachita nzolungama, koma makhalidwe anu ndidzaŵaonetsa poyera, ndipo mafano sadzakuthandizani.
13
Mukamafuula kufuna chithandizo, mafano anuwo akupulumutseni! Mphepo idzaiyalula milunguyo, mpweya udzaiwulutsa. Koma amene amakhulupirira Ine, adzalandira dziko lokhalamo, ndi kumapembedza pa phiri langa loyera.”
14
Padzamveka mau akuti, “Lambulani, lambulani ndi kukonza mseu. Chotsani chitsa chilichonse pa njira yodzeramo anthu anga.”
15
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
16
“Ndine amene ndidalenga anthu anga ndi kuŵapatsa mpweya wa moyo, motero sindidzapitirira kukangana nawo kapena kuŵakwiyira mpaka muyaya.
17
“Ndidaŵakwiyira chifukwa anali okonda chuma dziŵi. Tsono ndidaŵalanga, ndi kuŵafulatira mokwiya. Koma iwowo adakhalabe ouma mitu, ndipo adapitirira kuchita ntchito zao zoipa.
18
“Ndidaona m'mene ankachitira, komabe ndidzaŵachiritsa. Ndidzaŵatsogolera ndi kuŵatonthoza. Anthu olira nao adzandiyamika ndi milomo yao.
19
Anthu onse akutali ndi apafupi, ndidzaŵapatsa mtendere. Ndidzachiritsa anthu anga.
20
Koma anthu oipa ali ngati nyanja yoŵinduka, yosatha kukhala bata, ndipo mafunde ake amangoponya matope ndi ndere.
21
Palibe mtendere kwa oipa,” akutero Mulungu wanga.
← Chapter 56
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 58 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→