bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Isaiah 41
Isaiah 41
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 40
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 42 →
1
Mulungu akuti, “Mukhale chete ndipo mundimvere, inu maiko a m'mphepete mwa nyanja. Anthu a mitundu yonse akhale ndi mphamvu zatsopano. Asendere ndi kulankhulapo. Tiyeni tikhale pamodzi pa mlandu atiweruze.
2
“Kodi ndani adabweretsa wogonjetsa uja wochokera kuvuma, wonka napambana kulikonse kumene amapita? Ndani amamthandiza kuti apambane anthu a mitundu ina, ndi kugonjetsa mafumu? Lupanga lake limaŵasandutsa anthuwo kukhala ngati fumbi lapansi, uta wake umaŵamwaza ngati mankhusu.
3
Amaŵalondola namayenda mosavutika, m'njira zimene mapazi ake sadayendemo kale.
4
Ndani adachita zimenezi mpaka kuzitsiriza, osakhala amene adayambitsa mitundu yonse ya anthu? Ndi Ineyo, Chauta, amene ndine chiyambi, ndipo ndidzakhalabe yemweyo pakati pa otsiriza.”
5
Anthu a maiko a m'mphepete mwa nyanja aona zimene ndachita ndipo aopsedwa, anthu a pa mathero a dziko lapansi ali njenjenje. Akusendera pafupi, akubwera.
6
Aliyense akuthandiza mnzake, akuuza mbale wake kuti, “Limba mtima.”
7
Mmisiri wa matabwa amalimbikitsa mmisiri wosungunula golide, wosalaza fano ndi nyundo amalimbikitsa wolisanja pa chipala, ndipo ponena za kuwotcherera amati, “Kwachitika bwino.” Kenaka amalikhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwedezeke.
8
Koma iwe Israele mtumiki wanga, iweyo Yakobe amene ndakusankhula, ndiwe mdzukulu wa Abrahamu bwenzi langa.
9
Ndidakutenga kuchokera ku mapeto a dziko lapansi, ndidakuitana kuchokera ku mbali zakutali za dziko. Ndipo ndidzakuuza kuti, “Iwe ndiwe mtumiki wanga, ndidakusankhula, sindidakutaye.”
10
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
11
Motero onse amene akukupsera mtima adzachita manyazi ndi kunyazitsidwa. Amene akumenyana nawe adzakhala ngati salinso kanthu, ndipo adzafa.
12
Udzafunafuna amene amakangana nawe, koma osaŵapeza. Amene amamenyana nawe nkhondo adzakhala ngati salinso kanthu.
13
Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.”
14
Usaope, iwe Yakobe, wofooka ngati nyongolotsi, usachite mantha, iwe Israele, wooneka ngati mtembo, chifukwa Ineyo ndidzakuthandiza. Mpulumutsi wako ndine, Woyera uja wa Israele.
15
Ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu, chatsopano, cha mano akuthwa. Udzanyenya mapiri ndi kuŵaphwanyaphwanya. Magomo udzaŵasandutsa mankhusu.
16
Udzaŵapeta, ndipo adzauluka ndi mphepo nadzamwazika ndi namondwe. Koma iwe udzakondwa chifukwa choti Ine ndine Mulungu wako. Udzapeza ulemerero chifukwa cha Ine, Woyera uja wa Israele.
17
Pamene amphaŵi ndi osauka akufunafuna madzi, koma osaŵapeza, ndipo kum'mero kwao kwangoti gwa ndi ludzu, Ine Chauta ndidzayankha pemphero lao, Ine Mulungu wa Israele sindidzaŵasiya.
18
Ndidzayendetsa mitsinje pakati pa zitunda zouma, ndipo akasupe adzatumphuka m'zigwa. Ndidzasandutsa chipululu kukhala chidziŵe cha madzi, ndi dziko louma kukhala akasupe.
19
M'chipululu ndidzameretsa mkungudza, kasiya, mchisu ndi mtengo wa olivi. M'dziko louma ndidzabzala mitengo ya paini ya mitundu itatu.
20
Choncho anthu adzaona ndi kudziŵa, adzazindikira ndi kumvetsa kuti Chauta ndiye adachita zimenezi, kuti Woyera uja wa Israele ndiye adakonza zimenezi.
21
Chauta akuuza milungu kuti, “Dzafotokozeni mlandu wanu.” Chauta, Mfumu ya Yakobe akuti, “Perekani umboni wanu.
22
Mubwere kuno, mudzatiwuze zam'tsogolo. Mufotokozere bwalo zamakedzana, kuti tiziganizire, ndipo tidziŵe zotsatira zake, kapena mutiwuze zakutsogolo.
23
Tiwuzenitu zimene zidzachitike kutsogolo kuti tidziŵe kuti ndinu milungudi. Chitani zabwino kapena kubweretsa masoka, kuti mutidabwitse ndi kutichititsa mantha.
24
Inuyo sindinu kanthu konse, ndipo zochita zanu nzopandapake. Amene amakupembedzaniyo amandinyansa.
25
“Ndautsa munthu wina kumpoto, ndipo wabwera. Munthuyo, kuchokera chakuvuma, amamva kuitana pomutchula dzina. Amaponda olamulira ngati matope, monga m'mene munthu woumba mbiya amapondera mtapo.
26
Ndani adaululiratu zimenezi poyamba pomwe kuti ife tidziŵe? Ndani adatiwuziratu zimenezi zisanachitike, kuti ife tinene kuti, ‘Wakhoza?’ Palibe ndi mmodzi yemwe adazinena, palibe ndi mmodzi yemwe adazilengeza, ndipo palibe amene adamva mau anu.
27
Ine Chauta ndine amene ndidayambirira kumuuza Ziyoni kuti, ‘Si awo! Akubwera!’ Ndine amene ndidatuma munthu wokanena uthenga wabwinowu ku Yerusalemu.
28
Koma ndikayang'ana, palibe ndi mmodzi yemwe: palibe wotha kulangiza, palibe wotha kuyankha mafunso anga.
29
Ndithudi, milungu yonseyi njachabe, zochita zake si kanthu konse. Mafano ake osungunula ali ngati mphepo yachabechabe.”
← Chapter 40
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 42 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→